Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 13:11 - Buku Lopatulika

11 Ndinakupatsa mfumu mu mkwiyo wanga; ndinamchotsanso mu ukali wanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndinakupatsa mfumu mu mkwiyo wanga; ndinamchotsanso m'ukali wanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Ndidakupatsani mafumu mwachipsera mtima. Kenaka atandikwiyitsa, ndidaŵachotsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Choncho Ine ndinakupatsani mfumu mwachipseramtima, ndipo ndinayichotsa mwaukali.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 13:11
18 Mawu Ofanana  

Pochimwa dziko akalonga ake achuluka; koma anthu ozindikira ndi odziwa alikhazikikitsa nthawi yaikulu.


Pakuti tsopano adzati, Tilibe mfumu, popeza sitiopa Yehova; ndi mfumu idzatichitira chiyani?


Ndipo Samariya, mfumu yake yamwelera ngati thovu pamadzi.


Pakuti ana a Israele adzakhala masiku ambiri opanda mfumu, ndi opanda kalonga, ndi opanda nsembe, ndi opanda choimiritsa, ndi opanda efodi kapena aterafi;


Analonga mafumu, koma sikunachokera kwa Ine; anaika akalonga, koma sindinadziwa; anadzipangira mafano a siliva wao ndi golide wao, kuti akalikhidwe.


Ndipo Samuele anaitana anthu onse asonkhane kwa Yehova ku Mizipa;


koma lero inu mwakana Mulungu wanu amene anakupulumutsani yekha m'matsoka anu onse, ndi m'masautso anu; ndipo munanena naye, Koma mutipatse mfumu. Chifukwa chake tsono mudzionetse pamaso pa Yehova mafukomafuko, ndi magulumagulu.


Ndipo Samuele anauza Aisraele onse, kuti, Onani ndinamvera mau anu mwa zonse munalankhula ndi ine, ndipo ndinakulongerani mfumu.


Chifukwa chake siyi mfumu imene munaisankha, imene munandipempha; ndipo taonani, Yehova anakuikirani mfumu.


Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Ine sindibwerera nanu; pakuti munakaniza mau a Yehova, ndipo Yehova anakaniza inu, kuti simudzakhalanso mfumu ya Israele.


Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Iwe ukuti ulire chifukwa cha Saulo nthawi yotani, popeza Ine ndinamkana kuti asakhale mfumu ya Israele? Dzaza nyanga yako ndi mafuta, numuke, ndidzakutumiza kwa Yese wa ku Betelehemu; pakuti ndinadzionera mfumu pakati pa ana ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa