Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 10:4 - Buku Lopatulika

4 Anena mau akulumbira monama, pakuchita mapangano momwemo; chiweruzo chiphuka ngati zitsamba zowawa m'michera ya munda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Anena mau akulumbira monama, pakuchita mapangano momwemo; chiweruzo chiphuka ngati zitsamba zowawa m'michera ya munda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Mafumu akungolankhula mau opandapake. Amangochita zipangano ndi malonjezo abodza. Chilungamo chasanduka kusalungama kumene kumaphuka ngati udzu woipa m'munda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Mafumu amalonjeza zambiri, amalumbira zabodza pochita mapangano. Kotero maweruzo amaphuka ngati zitsamba zakupha mʼmunda umene walimidwa.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 10:4
16 Mawu Ofanana  

Chifukwa kuti munda wampesa wa Yehova wa makamu ndiwo banja la Israele, ndi anthu a Yuda, mtengo wake womkondweretsa; Iye nayembekeza chiweruziro, koma onani kuphana; nayembekeza chilungamo, koma onani kufuula.


Koma kulumbira, ndi kunama, ndi kupha, ndi kuba, ndi kuchita chigololo; aboola, ndi mwazi ukhudzana nao mwazi.


Koma iwo analakwira chipangano ngati Adamu, m'mene anandichitira monyenga.


inu osintha chiweruzo chikhale chivumulo, nimugwetsa pansi chilungamo.


Kodi akavalo adzathamanga pathanthwe? Kodi adzalimako ndi ng'ombe pakuti mwasanduliza chiweruzo chikhale ndulu, ndi chipatso cha chilungamo chikhale chivumulo;


Pakuti ndiona kuti wagwidwa ndi ndulu yowawa ndi nsinga ya chosalungama.


opanda nzeru, osasunga mapangano, opanda chikondi cha chibadwidwe, opanda chifundo;


kuti angakhale pakati pa inu mwamuna, kapena mkazi, kapena banja, kapena fuko, mtima wao watembenuka kusiyana naye Yehova Mulungu wathu lero lino, kuti apite ndi kutumikira milungu ya amitundu aja; kuti ungakhale pakati pa inu muzu wakubala ndulu ndi chowawa.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, udzagona tulo ndi makolo ako; ndi anthu awa adzauka, nadzatsata ndi chigololo milungu yachilendo ya dziko limene analowa pakati pake, nadzanditaya Ine, ndi kuthyola chipangano changa ndinapangana naocho.


Pamenepo ndidzawapsera mtima tsiku ilo, ndipo ndidzawataya, ndi kuwabisira nkhope yanga, ndipo adzathedwa, ndi zoipa ndi zovuta zambiri zidzawafikira; kotero kuti adzati tsiku lija, Sizitifikira kodi zoipa izi popeza Mulungu wathu sakhala pakati pa ife?


osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudierekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino,


ndi kuyang'anira kuti pangakhale wina wakuperewera chisomo cha Mulungu, kuti ungapuke muzu wina wa kuwawa mtima ungavute inu, ndipo aunyinji angadetsedwe nao;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa