Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 10:5 - Buku Lopatulika

5 Okhala mu Samariya adzaopera chifanizo cha anaang'ombe a ku Betaveni; pakuti anthu ake adzamva nacho chisoni, ndi ansembe ake amene anakondwera nacho, chifukwa cha ulemerero wake, popeza unachichokera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Okhala m'Samariya adzaopera chifanizo cha anaang'ombe a ku Betaveni; pakuti anthu ake adzamva nacho chisoni, ndi ansembe ake amene anakondwera nacho, chifukwa cha ulemerero wake, popeza unachichokera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Anthu a ku Samariya adzachita mantha, fano la mwanawang'ombe la ku Betehaveni likadzaonongedwa. Anthu ake adzalirira. Nawonso ansembe ake aja adzalira maliro a mulungu waoyo, chifukwa ulemerero wake wonse wachokeratu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Anthu amene amakhala mu Samariya akuchita mantha chifukwa cha fano la mwana wangʼombe ku Beti-Aveni. Anthu ake adzalirira fanolo, chimodzimodzinso ansembe ake adamawo, amene anakondwera ndi kukongola kwake, chifukwa lachotsedwa pakati pawo ndi kupita ku ukapolo.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 10:5
20 Mawu Ofanana  

Koma Yehu sanazileke zoipa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene adachimwitsa nazo Israele, ndizo anaang'ombe agolide okhala mu Betele ndi mu Dani.


Ndipo anasiya malamulo onse a Yehova Mulungu wao, nadzipangira mafano oyenga, anaang'ombe awiri, napanga chifanizo, nagwadira khamu lonse la kuthambo, natumikira Baala.


Naletsa ansembe opembedza mafano, amene mafumu a Yuda anawaika afukize zonunkhira pa misanje m'mizinda ya Yuda, ndi pamalo pozinga Yerusalemu; iwo omwe ofukizira zonunkhira Baala, ndi dzuwa, ndi mwezi, ndi nthanda, ndi khamu lonse la kuthambo.


nadziikira ansembe a misanje, ndi a ziwanda, ndi a anaang'ombe adawapanga.


Ndipo tsopano, mukuti mudzilimbikitse kutsutsana nao ufumu wa Yehova m'dzanja la ana a Davide; ndinu aunyinji ambiri, ndi pamodzi nanu anaang'ombe agolide adawapanga Yerobowamu akhale milungu yanu.


Milunguyo iwerama, igwada pansi pamodzi; singapulumutse katundu, koma iyo yeni yalowa m'ndende.


Ndipo tsopano aonjeza kuchimwa, nadzipangira mafano oyenga a siliva wao, mafano monga mwa nzeru zao, onsewo ntchito ya amisiri; anena za iwo, Anthu ophera nsembe apsompsone anaang'ombe.


Chinkana iwe, Israele, uchita uhule, koma asapalamule Yuda; ndipo musafika inu ku Giligala, kapena kukwera ku Betaveni, kapena kulumbira, Pali Yehova.


Ombani mphalasa mu Gibea, ndi lipenga mu Rama; fuulani ku Betaveni; pambuyo pako, Benjamini.


Usakondwera, Israele, ndi kusekerera, ngati mitundu ya anthu; pakuti wachita chigololo kuleka Mulungu wako, wakonda mphotho ya chigololo pa dwale la tirigu lililonse.


Kunena za Efuremu, ulemerero wao udzauluka ndi kuchoka ngati mbalame; sipadzakhala kubala, ndi kukhala ndi pakati, ndi kuima.


Pakuti tsiku lakumlanga Israele chifukwa cha zolakwa zake, ndidzalanganso maguwa a nsembe a ku Betele; ndi nyanga za guwa la nsembe zidzadulidwa, ndipo zidzagwa pansi.


Ndipo ndidzatambasulira dzanja langa pa Yuda, ndi pa onse okhala mu Yerusalemu; ndipo ndidzaononga otsala a Baala kuwachotsa m'malo muno, ndi dzina la Akemari pamodzi ndi ansembe;


ndipo tiopa ife kuti ntchito yathuyi idzayamba kunyonyosoka; komanso kuti Kachisi wa mulungu wamkazi Aritemi adzayamba kuyesedwa wachabe; ndiponso kuti iye adzayamba kutsitsidwa ku ukulu wake, iye amene a mu Asiya onse, ndi onse a m'dziko lokhalamo anthu, ampembedza.


Ndipo Yoswa anatuma amuna kuchokera ku Yeriko apite ku Ai, ndiwo pafupi pa Betaveni, kum'mawa kwa Betele; nanena nao, Kwerani ndi kukazonda dziko. Nakwera amunawo, nazonda Ai.


Nati iye, Mwanditengera milungu yanga ndinaipanga, ndi wansembe, ndi kuchoka; chinditsaliranso chiyani? Ndipo muneneranji kwa ine, Chakusowa nchiyani?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa