Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 10:6 - Buku Lopatulika

6 Adzachitengeranso ku Asiriya chikhale mphatso ya kwa mfumu Yarebu; Efuremu adzatenga manyazi, ndi Israele adzachita manyazi ndi uphungu wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Adzachitengeranso ku Asiriya chikhale mphatso ya kwa mfumu Yarebu; Efuremu adzatenga manyazi, ndi Israele adzachita manyazi ndi uphungu wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Zoonadi, fanolo lidzatengedwa kupita ku Asiriya, kuti likakhale mphatso yoperekedwa kwa mfumu yaikulu. Aefuremu adzachita manyazi, Aisraelewo adzachita manyazi chifukwa cha malangizo onama amene ankamvera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Fanolo lidzatengedwa kupita ku Asiriya ngati mphatso kwa mfumu yayikulu. Efereimu adzachititsidwa manyazi chifukwa cha mafano ake amitengo.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 10:6
22 Mawu Ofanana  

Anamkwerera Salimanezere mfumu ya Asiriya kumthira nkhondo; ndipo Hoseya anamgonjera, namsonkhera mitulo.


Mapondedwe ake amphamvu adzasautsidwa, ndi uphungu wakewake udzamgwetsa.


Chifukwa adzakhala ndi manyazi, chifukwa cha mitengo yathundu munaikhumba, ndipo inu mudzagwa nkhope, chifukwa cha minda imene mwaisankha.


Chifukwa chake mphamvu za Farao zidzakhala kwa inu manyazi, ndi kukhulupirira mthunzi wa Ejipito kudzakhala chisokonezo chanu.


Iwo adzakhala ndi manyazi, inde, adzathedwa nzeru onsewo; adzalowa m'masokonezo pamodzi, amene apanga mafano.


Ndipo Mowabu adzachita manyazi chifukwa cha Kemosi, monga nyumba ya Israele inachita manyazi chifukwa cha Betele amene anamkhulupirira.


Koma sanamvere, sanatchere khutu, koma anayenda mu upo ndi m'kuuma kwa mtima wao woipa, nabwerera chambuyo osayenda m'tsogolo.


Unachitanso chigololo ndi Aasiriya, pakuti unakhala wosakoledwa, inde unachita chigololo nao, koma sunakoledwe.


Pamenepo mudzakumbukira njira zanu zoipa, ndi zochita inu zimene sizinali zabwino; ndipo mudzanyansidwa nokha pamaso panu, chifukwa cha mphulupulu zanu ndi zonyansa zanu.


ndi milungu yao yomwe, pamodzi ndi akalonga ao, ndi zipangizo zao zofunika zasiliva ndi golide adzazitenga kunka nazo ndende ku Ejipito; ndi zaka zake zidzaposa za mfumu ya kumpoto.


Mphepo yamkulunga m'mapiko ake, ndipo adzachita manyazi chifukwa cha nsembe zao.


Monga anachuluka, momwemo anandichimwira; ndidzasanduliza ulemerero wao ukhale manyazi.


Pamene Efuremu anaona nthenda yake, ndi Yuda bala lake, Efuremu anamuka kwa Asiriya, natumiza kwa mfumu Yarebu; koma iye sakhoza kukuchiritsani, kapena kupoletsa bala lanu.


Pakuti ichi chomwe chafumira kwa Israele; mmisiri wampanga, koma sali Mulungu; inde mwanawang'ombe wa Samariya adzaphwanyikaphwanyika.


Pakuti asunga malemba a Omuri, ndi ntchito za nyumba ya Ahabu, ndipo mumayenda mu uphungu wao; kuti ndikusandulize bwinja, ndi okhalamo chotsonya; ndipo mudzasenza chitonzo cha anthu anga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa