Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 19:15 - Buku Lopatulika

15 Pamenepo anafuula iwowa, Chotsani, Chotsani, mpachikeni Iye! Pilato ananena nao, Ndipachike mfumu yanu kodi? Ansembe aakulu anayankha, Tilibe mfumu koma Kaisara.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Pamenepo anafuula iwowa, Chotsani, Chotsani, mpachikeni Iye! Pilato ananena nao, Ndipachike mfumu yanu kodi? Ansembe aakulu anayankha, Tilibe mfumu koma Kaisara.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Koma iwo adafuula kuti, “Mchotseni! Mchotseni! Kampachikeni pa mtanda!” Pilato adaŵafunsa kuti, “Ndipachike Mfumu yanu kodi?” Akulu a ansembe adati, “Tilibe mfumu ina ai, koma Mfumu ya ku Roma yokha.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Koma iwo anafuwula kuti, “Choka nayeni! Choka nayeni! Mpachikeni!” Pilato anafunsa kuti, “Kodi ine ndipachike mfumu yanuyi?” Akulu a ansembe anayankha kuti, “Ife tilibe mfumu ina koma Kaisara.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 19:15
9 Mawu Ofanana  

Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo; ndipo anthu adzamvera iye.


Chifukwa chake mutiuze ife, muganiza chiyani? Kuloledwa kodi kupatsa msonkho kwa Kaisara, kapena iai?


Koma iwo onse pamodzi anafuula, nati, Chotsani munthu uyu, mutimasulire Barabasi;


Ndipo Pilato anati kwa iwo, Mumtenge Iye inu, ndi kumweruza Iye monga mwa chilamulo chanu. Ayuda anati kwa iye, Tilibe ulamuliro wakupha munthu aliyense;


Ndipo pamene ansembe aakulu ndi anyamata anamuona Iye, anafuula nanena, Mpachikeni, mpachikeni. Pilato ananenana nao, Mtengeni Iye inu nimumpachike; pakuti ine sindipeza chifukwa mwa Iye.


Ndipo ngakhale sanapeze chifukwa cha kumphera, anapempha Pilato kuti aphedwe.


pakuti unyinji wa anthu unatsata, nufuula, Mchotse iye.


Ndipo adamumva kufikira mau awa; ndipo anakweza mau ao nanena, Achoke padziko lapansi munthu wotere; pakuti sayenera iye kukhala ndi moyo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa