Genesis 2:4 - Buku Lopatulika Imeneyo ndiyo mibadwo yao ya zakumwamba ndi dziko lapansi, pamene zinalengedwa, tsiku lomwe Yehova Mulungu anapanga dziko lapansi ndi zakumwamba. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Imeneyo ndiyo mibadwo yao ya zakumwamba ndi dziko lapansi, pamene zinalengedwa, tsiku lomwe Yehova Mulungu anapanga dziko lapansi ndi zakumwamba. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndimo m'mene dziko lapansi ndi zonse zakuthambo zidalengedwera. Pamene Chauta ankalenga dziko lapansi ndi zonse zakuthambo, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mbiri ya momwe kumwamba ndi dziko lapansi zinalengedwera pa tsiku lija Yehova Mulungu ankazilenga ndi iyi: Yehova Mulungu atapanga dziko lapansi ndi kumwamba, |
Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pazamoyo zonse zokwawa padziko lapansi.
Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.
Ndipo anaona Mulungu kuti kuyerako kunali kwabwino; ndipo Mulungu analekanitsa kuyera ndi mdima.
Mibadwo ya ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti, ndi iyi; kwa iwo ndipo kunabadwa ana aamuna, chitapita chigumula chija.
Mibadwo ya Semu ndi iyi: Semu anali wa zaka zana limodzi ndipo anabala Aripakisadi, chitapita chigumula zaka ziwiri;
Mulungu ndipo anadalitsa tsiku lachisanu ndi chiwiri, naliyeretsa limenelo: chifukwa limenelo adapuma ku ntchito yake yonse imene Mulungu anailenga ndi kupanga.
Mibadwo ya Ismaele mwana wamwamuna wa Abrahamu, amene Hagara Mwejipito mdzakazi wa Sara anambalira Abrahamu ndi iyi:
Ili ndi buku la mibadwo ya Adamu. Tsiku lomwe Mulungu analenga munthu anamlenga m'chifanizo cha Mulungu;
Ndipo anthu onse anaona, nagwa nkhope zao pansi, nati, Yehova ndiye Mulungu, Yehova ndiye Mulungu.
nati, Yehova Mulungu wa makolo athu, Inu sindinu Mulungu wa mu Mwamba kodi? Sindinu woweruza maufumu onse a amitundu kodi? Ndi m'dzanja mwanu muli mphamvu yolimba; palibe wina wakulimbana ndi Inu.
Ndipo maina a ana aamuna a Levi, mwa kubadwa kwao ndiwo: Geresoni, ndi Kohati, ndi Merari; ndipo zaka za moyo wa Levi ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri.
Atero Yehova, mfumu ya Israele ndi Mombolo wake, Yehova wa makamu, Ine ndili woyamba ndi womaliza, ndi popanda Ine palibenso Mulungu.
Yohane kwa Mipingo isanu ndi iwiri mu Asiya: Chisomo kwa inu ndi mtendere, zochokera kwa Iye amene ali, ndi amene adali, ndi amene alinkudza; ndi kwa mizimu isanu ndi iwiri yokhala kumpando wachifumu wake;
Ine ndine Alefa ndi Omega, ati Ambuye Mulungu, amene ali, amene adali, ndi amene alinkudza, Wamphamvuyonse.
nati, Tikuyamikani, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse, amene muli, nimunali; popeza mwadzitengera mphamvu yanu yaikulu, ndipo mwachita ufumu.
Ndipo ndinamva mngelo wa madziwo nanena, Muli wolungama, amene muli, nimunali, Woyera Inu, chifukwa mudaweruza kotero;