Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Chivumbulutso 1:4 - Buku Lopatulika

4 Yohane kwa Mipingo isanu ndi iwiri mu Asiya: Chisomo kwa inu ndi mtendere, zochokera kwa Iye amene ali, ndi amene adali, ndi amene alinkudza; ndi kwa mizimu isanu ndi iwiri yokhala kumpando wachifumu wake;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Yohane kwa Mipingo isanu ndi iwiri m'Asiya: Chisomo kwa inu ndi mtendere, zochokera kwa Iye amene ali, ndi amene adali, ndi amene alinkudza; ndi kwa mizimu isanu ndi iwiri yokhala kumpando wachifumu wake;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Ndine, Yohane, ndikulembera mipingo isanu ndi iŵiri ya ku Asiya. Akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere Mulungu amene alipo, amene analipo kale, amene alikudza. Ikukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere mizimu isanu ndi iŵiri yokhala patsogolo pa mpando wachifumu wa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ndine Yohane, Kupita ku mipingo isanu ndi iwiri ya mʼchigawo cha Asiya. Chisomo ndi mtendere kwa inu, kuchokera kwa Iye amene ali, amene analipo ndi amene akubwera ndi kwa mizimu isanu ndi iwiri yokhala patsogolo pa mpando wake waufumu,

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 1:4
41 Mawu Ofanana  

Asanabadwe mapiri, kapena musanalenge dziko lapansi, ndi lokhalamo anthu, inde, kuyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha, Inu ndinu Mulungu.


Ndipo Mulungu anati kwa Mose, INE NDINE YEMWE NDILI INE. Anatinso, Ukatero ndi ana a Israele, INE NDINE wandituma kwa inu.


Ndipo mzimu wa Yehova udzambalira iye mzimu wanzeru ndi wakuzindikira, mzimu wa uphungu ndi mphamvu, mzimu wakudziwa ndi wakuopa Yehova;


Ndani wachipanga, nachimaliza icho, kutchula mibadwo chiyambire? Ine Yehova, ndine woyamba, ndi pachimaliziro ndine ndemwe.


Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.


Koma iwe, Betelehemu Efurata, ndiwe wamng'ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditulukira wina wakudzakhala woweruza mu Israele; matulukiro ake ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.


Pakuti taona mwalawo ndinauika pamaso pa Yoswa; pamwala umodzi pali maso asanu ndi awiri; taonani, ndidzalocha malochedwe ake, ati Yehova wa makamu, ndipo ndidzachotsa mphulupulu ya dziko lija tsiku limodzi.


Pakuti wapeputsa tsiku la tinthu tating'ono ndani? Pakuti adzakondwera, asanu ndi awiri awa, nadzaona chingwe cholungamitsira chilili m'dzanja la Zerubabele, ndiwo maso a Yehova; ayendayenda mwa dziko lonse.


Ndi mthenga anayankha, nati kwa ine, Izi ndi mphepo zinai zakumwamba zakutuluka kumene zimaimirira pamaso pa Ambuye wa dziko lonse lapansi.


Pachiyambi panali Mau, ndipo Mau anali kwa Mulungu, ndipo Mau ndiye Mulungu.


Ndipo anachita chomwecho zaka ziwiri; kotero kuti onse akukhala mu Asiya anamva mau a Ambuye, Ayuda ndi Agriki.


Aparti ndi Amedi, ndi Aelamu, ndi iwo akukhala mu Mesopotamiya, mu Yudeya, ndiponso mu Kapadokiya, mu Ponto, ndi mu Asiya;


kwa onse a ku Roma, okondedwa a Mulungu, oitanidwa kuti akhale oyera mtima: Chisomo chikhale ndinu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.


Chisomo kwa inu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.


Chisomo kwa inu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.


Yesu Khristu ali yemweyo dzulo, ndi lero, ndi kunthawi zonse.


Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.


Chivumbulutso cha Yesu Khristu, chimene Mulungu anamvumbulutsira achionetsera akapolo ake, ndicho cha izi ziyenera kuchitika posachedwa: ndipo potuma mwa mngelo wake anazindikiritsa izi kwa kapolo wake Yohane;


ndi kuti, Chimene upenya, lemba m'buku, nulitumize kwa Mipingo isanu ndi iwiri, ku Efeso, ndi ku Smirina, ndi ku Pergamo, ndi ku Tiatira, ndi ku Sardi, ndi ku Filadelfiya, ndi ku Laodikea.


Ndipo pamene ndinamuona Iye, ndinagwa pa mapazi ake ngati wakufa; ndipo anaika dzanja lake lamanja pa ine, nati, Usaope, Ine ndine Woyamba ndi Wotsiriza,


chinsinsi cha nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene unaziona padzanja langa lamanja, ndi zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide: nyenyezi zisanu ndi ziwiri ndizo angelo a Mipingo isanu ndi iwiri; ndipo zoikaponyali zisanu ndi ziwiri ndizo Mipingo isanu ndi iwiri.


Ine ndine Alefa ndi Omega, ati Ambuye Mulungu, amene ali, amene adali, ndi amene alinkudza, Wamphamvuyonse.


Ine Yohane, mbale wanu ndi woyanjana nanu m'chisautso ndi ufumu ndi chipiriro zokhala mwa Yesu, ndinakhala pa chisumbu chotchedwa Patimosi, chifukwa cha mau a Mulungu ndi umboni wa Yesu.


Ndipo ndinamva mngelo wa madziwo nanena, Muli wolungama, amene muli, nimunali, Woyera Inu, chifukwa mudaweruza kotero;


Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Pergamo lemba: Izi anena Iye wokhala nalo lupanga lakuthwa konsekonse:


Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Tiatira lemba: Izi azinena Mwana wa Mulungu, wakukhala nao maso ake ngati lawi la moto, ndi mapazi ake ngati mkuwa wonyezimira:


Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Smirina lemba: Izi anena woyamba ndi wotsiriza, amene anakhala wakufa, nakhalanso ndi moyo:


Ine Yesu ndatuma mngelo wanga kukuchitirani umboni za izi mu Mipingo. Ine ndine muzu ndi mbadwa ya Davide, nyenyezi yonyezimira ya nthanda.


Ndipo ine Yohane ndine wakumva ndi wakupenya izi. Ndipo pamene ndinamva ndi kupenya, ndinagwa pansi kulambira pa mapazi a mngelo wakundionetsa izo.


Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Sardi lemba: Izi anena Iye wakukhala nayo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri: Ndidziwa ntchito zako, kuti uli nalo dzina lakuti uli ndi moyo, ndipo uli wakufa.


Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Laodikea lemba: Izi anena Ameni'yo, mboni yokhulupirika ndi yoona, woyamba wa chilengo cha Mulungu:


Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Filadelfiya lemba: Izi anena Iye amene ali Woyera, Iye amene ali Woona, Iye wakukhala nacho chifungulo cha Davide, Iye wotsegula, ndipo palibe wina atseka; Iye wotseka, ndipo palibe wina atsegula:


Ndipo mu mpando wachifumu mudatuluka mphezi ndi mau ndi mabingu. Ndipo panali nyali zisanu ndi ziwiri za moto zoyaka kumpando wachifumu, ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu;


Ndipo zamoyozo zinai, chonse pa chokha chinali nao mapiko asanu ndi limodzi; ndipo zinadzala ndi maso pozinga ponse ndi m'katimo; ndipo sizipumula usana ndi usiku, ndi kunena, Woyera, woyera, woyera, Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, amene anali, amene ali, ndi amene alinkudza.


Ndipo ndinaona pakati pa mpando wachifumu ndi zamoyo zinai, ndi pakati pa akulu, Mwanawankhosa ali chilili ngati waphedwa; wokhala nazo nyanga zisanu ndi ziwiri, ndi maso asanu ndi awiri, ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, yotumidwa ilowe m'dziko lonse.


Ndipo ndinaona angelo asanu ndi awiri amene amaimirira pamaso pa Mulungu; ndipo anawapatsa malipenga asanu ndi awiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa