Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 2:5 - Buku Lopatulika

5 Ndi zomera zonse za m'munda zisanakhale m'dziko lapansi, ndiponso matherere onse a m'munda asanamere; chifukwa Yehova Mulungu sanavumbitsire mvula padziko lapansi, ndipo panalibe munthu wakulima nthaka;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndi zomera zonse za m'munda zisanakhale m'dziko lapansi, ndiponso matherere onse a m'munda asanamere; chifukwa Yehova Mulungu sanavumbitsire mvula pa dziko lapansi, ndipo panalibe munthu wakulima nthaka;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 panalibe chomera chilichonse pa dziko lapansi, ndipo mbeu zinali zisanamere, chifukwa Chauta Mulungu anali asanagwetse mvula pa dziko lapansi. Ndipo panalibenso wina aliyense wolima pa nthaka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 zitsamba zinali zisanamere ndipo chomera chilichonse chinali chisanamerenso popeza Yehova Mulungu anali asanagwetse mvula pa dziko lapansi. Panalibe munthu wolima nthaka,

Onani mutuwo Koperani




Genesis 2:5
15 Mawu Ofanana  

koma inakwera nkhungu yotuluka padziko lapansi, nkuthirira ponse pamwamba panthaka.


Yehova Mulungu anamtulutsa iye m'munda wa Edeni, kuti alime nthaka m'mene anamtenga iye.


pamene udzalima panthaka siidzaperekanso kwa iwe mphamvu yake: udzakhala wothawathawa ndi woyendayenda padziko lapansi.


Ndipo anabalanso mphwake Abele. Abele anakhala mbusa wa nkhosa, koma Kaini anali wakulima nthaka.


Amene avumbitsa mvula panthaka, natumiza madzi paminda;


Ameretsa msipu ziudye ng'ombe, ndi zitsamba achite nazo munthu; natulutse chakudya chochokera m'nthaka;


Akweza mitambo ichokere ku malekezero a dziko lapansi; ang'animitsa mphezi zidzetse mvula; atulutsa mphepo mosungira mwake.


Iye analenga dziko lapansi ndi mphamvu yake, nakhazikitsa dziko lapansi ndi nzeru yake, nayala thambo ndi kuzindikira kwake;


polankhula Iye, pali unyinji wa madzi m'mwamba, ndipo akweretsa nkhungu ku malekezero a dziko lapansi, alenga mphezi idzetse mvula, natulutsa mphepo m'zosungira zake.


Mwa zachabe za mitundu ya anthu zilipo kodi, zimene zingathe kuvumbitsa mvula? Kapena miyamba kubweretsa mivumbi? Kodi si ndinu, Yehova, Mulungu wathu? Ndipo tidzakudikirani Inu; pakuti munalenga zonse zimenezi.


kotero kuti mukakhale ana a Atate wanu wa Kumwamba; chifukwa Iye amakwezera dzuwa lake pa oipa ndi pa abwino, namavumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama.


Pakuti nthaka imene idamwa mvula iigwera kawirikawiri, nipatsa therere loyenera iwo amene adailimira, ilandira dalitso lochokera kwa Mulungu:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa