Ndipo Davide anati kwa Natani, Ndinachimwira Yehova. Natani nati kwa Davide, Ndiponso Yehova wachotsa tchimo lanu, simudzafa.
Eksodo 9:27 - Buku Lopatulika Ndipo Farao anatumiza, naitana Mose ndi Aroni, nanena nao, Ndachimwa tsopano; Yehova ndiye wolungama, ine ndi anthu anga ndife oipa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Farao anatumiza, naitana Mose ndi Aroni, nanena nao, Ndachimwa tsopano; Yehova ndiye wolungama, ine ndi anthu anga ndife oipa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Farao adaitana Mose ndi Aroni naŵauza kuti, “Zoonadi, ndachimwa ndithu tsopano. Chauta ndi wolungama, koma ineyo pamodzi ndi anthu anga, tonse ndife ochimwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni nati kwa iwo, “Tsopano ndachimwa, Yehova ndi wolungama, ine ndi anthu anga ndife olakwa. |
Ndipo Davide anati kwa Natani, Ndinachimwira Yehova. Natani nati kwa Davide, Ndiponso Yehova wachotsa tchimo lanu, simudzafa.
Pamenepo Farao anafulumira kuitana Mose ndi Aroni; nati, Ndalakwira Yehova Mulungu wanu, ndi inu.
Ndipo tsopano, ndikhululukiretu kulakwa kwanga nthawi ino yokha, nimundipembere kwa Yehova Mulungu wanu, kuti andichotsere imfa ino yokha.
Pamenepo Farao anaitana Mose ndi Aroni, nati, Mukani, mphereni nsembe Mulungu wanu m'dzikomu.
Pamenepo Farao anaitana Mose ndi Aroni, nati, Mundipembere Yehova, kuti andichotsere ine ndi anthu anga achulewo; ndipo ndidzalola anthu amuke, kuti amphere Yehova nsembe.
Yehova ali wolungama; pakuti ndapikisana ndi m'kamwa mwake; mumvetu, mitundu ya anthu nonsenu, nimuone chisoni changa; anamwali ndi anyamata anga atha kulowa m'ndende.
Chifukwa chake Yehova wakhala maso pa choipacho, ndi kutifikitsira icho; pakuti Yehova Mulungu wathu ali wolungama mu ntchito zake zonse azichita; ndipo sitinamvere mau ake.
Ndipo anthu anadza kwa Mose, nati, Tachimwa, popeza tinanena motsutsana ndi Yehova, ndi inu; pempherani kwa Yehova kuti atichotsere njokazi. Ndipo Mose anawapempherera anthu.
Pamenepo Balamu anati kwa mthenga wa Yehova, Ndachimwa, popeza sindinadziwe kuti munaima mondiletsa m'njira; ndipo tsopano, ngati chikuipirani, ndibwerera.
nanena, Ndinachita koipa ine, pakupereka mwazi wosalakwa. Koma iwo anati, Tili nacho chiyani ife? Udzionere wekha.
Koma kolingana ndi kuuma kwako, ndi mtima wako wosalapa, ulikudziunjikira wekha mkwiyo pa tsiku la mkwiyo ndi la kuvumbulutsa kuweruza kolungama kwa Mulungu;
Ndipo tidziwa kuti zinthu zilizonse chizinena chilamulo chizilankhulira iwo ali nacho chilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi litsutsidwe ndi Mulungu;
Ndipo Akani anayankha Yoswa nati, Zoonadi, ndachimwira Yehova Mulungu wa Israele, ndachita zakutizakuti;
Ndipo Saulo anati kwa Samuele, Ndinachimwa; pakuti ndinalumpha lamulo la Yehova, ndi mau anu omwe; chifukwa ndinaopa anthuwo, ndi kumvera mau ao.
Pomwepo iye anati, Ndinachimwa, koma mundichitire ulemu tsopano pamaso pa akulu a anthu anga, ndi pamaso pa Israele, nimubwerere pamodzi ndi ine, kuti ndikalambire Yehova Mulungu wanu.
Pamenepo Saulo anati, Ndinachimwa; bwera, mwana wanga Davide; pakuti sindidzakuchitiranso choipa, popeza moyo wanga unali wa mtengo wapatali pamaso pako lero; ona, ndinapusa ndi kulakwa kwakukulu.