Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 22:34 - Buku Lopatulika

34 Pamenepo Balamu anati kwa mthenga wa Yehova, Ndachimwa, popeza sindinadziwe kuti munaima mondiletsa m'njira; ndipo tsopano, ngati chikuipirani, ndibwerera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

34 Pamenepo Balamu anati kwa mthenga wa Yehova, Ndachimwa, popeza sindinadziwa kuti munaima mondiletsa m'njira; ndipo tsopano, ngati chikuipirani, ndibwerera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

34 Balamu adayankha mngelo wa Chauta uja kuti, “Ndachimwa. Sindinalikudziŵa kuti mukunditsekera njira. Nchifukwa chake tsono, ngati zakuipirani, ndibwerera.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

34 Balaamu anati kwa mngelo wa Yehova uja, “Ndachimwa. Sindinadziwe kuti munayima pa njira kunditsutsa. Tsopano ngati Inu simunakondwe, ineyo ndibwerera.”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 22:34
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anati kwa Natani, Ndinachimwira Yehova. Natani nati kwa Davide, Ndiponso Yehova wachotsa tchimo lanu, simudzafa.


Ndipo Mulungu anaipidwa nacho chinthuchi, chifukwa chake Iye anakantha Israele.


Pamene anawapha ndipo anamfuna Iye; nabwerera, nafunitsitsa Mulungu.


Ndipo Farao anatumiza, naitana Mose ndi Aroni, nanena nao, Ndachimwa tsopano; Yehova ndiye wolungama, ine ndi anthu anga ndife oipa.


kuti Yehova angaone kukondwa kwako, ndi kukuyesa koipa, ndi kuleka kumkwiyira.


Ndipo anthu anaipa, namadandaula m'makutu a Yehova; ndipo pamene Yehova anamva anapsa mtima; ndi moto wa Yehova unayaka pakati pao, nunyeketsa ku chilekezero cha chigono.


Ndipo anauka mamawa, nakwera pamwamba paphiri, nati, Tili pano, tidzakwera kunka ku malo amene Yehova ananena; popeza tachimwa.


Koma Mulungu anati kwa Balamu, Usapita nao; usatemberera anthuwa; pakuti adalitsika.


koma bulu anandiona, nandipatukira nthawi izi zitatu pondiona; akadapanda kundipatukira, ndikadakupha iwe ndithu, ndi kumsunga iye wamoyo.


Ndipo Saulo anati kwa Samuele, Ndinachimwa; pakuti ndinalumpha lamulo la Yehova, ndi mau anu omwe; chifukwa ndinaopa anthuwo, ndi kumvera mau ao.


Pomwepo iye anati, Ndinachimwa, koma mundichitire ulemu tsopano pamaso pa akulu a anthu anga, ndi pamaso pa Israele, nimubwerere pamodzi ndi ine, kuti ndikalambire Yehova Mulungu wanu.


Nati kwa Davide, Iwe ndiwe wolungama woposa ine; popeza unandibwezera zabwino, koma ine ndinakubwezera zoipa.


Pamenepo Saulo anati, Ndinachimwa; bwera, mwana wanga Davide; pakuti sindidzakuchitiranso choipa, popeza moyo wanga unali wa mtengo wapatali pamaso pako lero; ona, ndinapusa ndi kulakwa kwakukulu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa