Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 22:35 - Buku Lopatulika

35 Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa Balamu, Pita nao anthuwa; koma mau okhaokha ndinena ndi iwe, ndiwo ukanene. Potero Balamu anamuka nao akalonga a Balaki.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

35 Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa Balamu, Pita nao anthuwa; koma mau okhaokha ndinena ndi iwe, ndiwo ukanene. Potero Balamu anamuka nao akalonga a Balaki.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

35 Apo mngelo wa Chauta adauza Balamu kuti, “Pita nawo anthuŵa. Koma ukanene zokhazo zimene ndikakuuze.” Choncho Balamu adapitirira ulendo wake pamodzi ndi akalonga a Balaki aja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

35 Mngelo wa Yehova anati kwa Balaamu, “Pita ndi anthuwa koma ukayankhule zokhazo zimene ndikakuwuze.” Choncho Balaamu anapita ndi akuluakulu a Balaki.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 22:35
8 Mawu Ofanana  

Nati Mikaya, Pali Yehova, chonena Mulungu wanga ndidzanena chomwechi.


Potero ndinawaperekera kuuma mtima kwao, ayende monga mwa uphungu waowao.


Woyenda mwangwiro adzapulumuka; koma wokhota m'mayendedwe ake adzagwa posachedwa.


Pamene Balaki anamva kuti wafika Balamu, anamtulukira kukakomana naye kumzinda wa Mowabu, wokhala m'mphepete mwa Arinoni, ndiwo ku malekezero a malire ake.


koma sindinafuna kumvera Balamu, potero anakudalitsani chidalitsire, ndipo ndinakulanditsani m'dzanja lake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa