Masalimo 129 - Buku LopatulikaIsraele asautsidwa koma osafafanizidwa Nyimbo yokwerera. 1 Anandisautsa kawirikawiri kuyambira ubwana wanga, anene tsono Israele; 2 Anandisautsa kawirikawiri kuyambira ubwana wanga; koma sanandilake. 3 Olima analima pamsana panga; anatalikitsa mipere yao. 4 Yehova ndiye wolungama; anadulatu zingwe za oipa. 5 Achite manyazi nabwerere m'mbuyo. Onse akudana naye Ziyoni. 6 Akhale ngati udzu womera patsindwi, wakufota asanauzule; 7 umene womweta sadzaza nao dzanja lake, kapena womanga mitolo sakupatira manja. 8 Angakhale opitirirapo sanena, Dalitso la Mulungu likhale pa inu; tikudalitsani m'dzina la Yehova. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi