Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 129:5 - Buku Lopatulika

5 Achite manyazi nabwerere m'mbuyo. Onse akudana naye Ziyoni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Achite manyazi nabwerere m'mbuyo. Onse akudana naye Ziyoni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Anthu onse odana ndi Ziyoni agonjetsedwe ndi kupirikitsidwa mwamanyazi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Onse amene amadana ndi Ziyoni abwezedwe pambuyo mwamanyazi.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 129:5
17 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali atachimva adani athu onse, amitundu onse akutizinga anaopa, nagwadi nkhope; popeza anazindikira kuti ntchitoyi inachitika ndi Mulungu wathu.


Ndipo Hamani anafotokozera Zeresi mkazi wake, ndi mabwenzi ake onse, zonse zidamgwera. Nanena naye anzeru ake, ndi Zeresi mkazi wake, Mordekai amene wayamba kutsika pamaso pake, akakhala wa mbumba ya Ayuda, sudzamgonjetsa; koma udzagwada pamaso pake.


Ndipo Ayuda anakantha adani ao onse, kuwakantha ndi lupanga, ndi kuwapulula, nachitira odana nao monga anafuna.


Mupempherere mtendere wa Yerusalemu; akukonda inu adzaona phindu.


Apululuke, mobwezera manyazi ao amene anena nane, Hede, hede.


Adani a moyo wanga achite manyazi, nathawe; chotonza ndi chimpepulo zikute ondifunira choipa.


Chifukwa chake padzaoneka, kuti pamene Ambuye atatha ntchito yake yonse paphiri la Ziyoni ndi pa Yerusalemu, ndidzalanga zipatso za mtima wolimba wa mfumu ya Asiriya, ndi ulemerero wa maso ake okwezedwa.


Ndipo kudzafanana ndi munthu wanjala, pamene alota, ndipo, taonani, akudya; koma auka, ndipo m'kati mwake muli zii; kapena monga munthu waludzu pamene alota, ndipo taonani, akumwa; koma auka ndipo taonani walefuka, ndipo m'kati mwake muli gwaa; momwemo lidzakhala khamu la mitundu yonse yomenyana ndi phiri la Ziyoni.


awa ndiwo mau amene Yehova wanena za iye, Namwali, mwana wamkazi wa Ziyoni, wakunyoza iwe ndi kuseka iwe ndi chiphwete; mwana wamkazi wa Yerusalemu wapukusa mutu wake pambuyo pako.


Pakuti ndidzatchinjiriza mzinda uno, kuupulumutsa, chifukwa cha Ine mwini, ndi mtumiki wanga Davide.


Ndipo tsopano amitundu ambiri asonkhana kuyambana nawe, akuti, Aipsidwe, diso lathu lipenye ku Ziyoni.


Ndipo kudzachitika tsiku ilo, ndidzaika Yerusalemu akhale mwala wolemetsa mitundu yonse ya anthu; onse akuusenza adzadzilasa nao; ndi amitundu onse a padziko lapansi adzasonkhana kutsutsana nao.


Tsiku ilo ndidzaika akalonga a Yuda ngati phale la moto pansi pa nkhuni, ndi ngati muuni wamoto mwa mitolo ya tirigu; ndipo adzatha mitundu yonse ya anthu pozungulirapo, kudzanja lamanja ndi lamanzere; ndipo Yerusalemu adzakhalanso m'malo mwake, mu Yerusalemu.


Ngati wina sakonda Ambuye, akhale wotembereredwa. Akudza Ambuye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa