Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 15:30 - Buku Lopatulika

30 Pomwepo iye anati, Ndinachimwa, koma mundichitire ulemu tsopano pamaso pa akulu a anthu anga, ndi pamaso pa Israele, nimubwerere pamodzi ndi ine, kuti ndikalambire Yehova Mulungu wanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Pomwepo iye anati, Ndinachimwa, koma mundichitire ulemu tsopano pamaso pa akulu a anthu anga, ndi pamaso pa Israele, nimubwerere pamodzi ndi ine, kuti ndikalambire Yehova Mulungu wanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Tsono Saulo adati, “Inde ndachimwa, komabe chonde mundilemekeze pakati pa atsogoleri a anthu anga ndi pamaso pa Aisraele onse, ndipo mubwerere nane pamodzi, kuti ndikapembedze Chauta, Mulungu wanu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Sauli anati, “Ine ndachimwa. Komabe, chonde mundilemekeze pamaso pa akuluakulu, anthu anga, ndiponso pamaso pa Israeli. Mubwerere nane kuti ndikapembedze Yehova Mulungu wanu.”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 15:30
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anati kwa Natani, Ndinachimwira Yehova. Natani nati kwa Davide, Ndiponso Yehova wachotsa tchimo lanu, simudzafa.


Ndipo Farao anatumiza, naitana Mose ndi Aroni, nanena nao, Ndachimwa tsopano; Yehova ndiye wolungama, ine ndi anthu anga ndife oipa.


Ndipo Ambuye anati, Popeza anthu awa ayandikira ndi Ine ndi m'kamwa mwao, nandilemekeza ndi milomo yao, koma mtima wao uli kutali ndi Ine, ndi mantha ao akundiopa Ine, ndi lamulo la anthu analiphunzira;


Taonani, moyo wake udzikuza, wosaongoka m'kati mwake; koma wolungama adzakhala ndi moyo mwa chikhulupiriro chake.


pakuti anakonda ulemerero wa anthu koposa ulemerero wa Mulungu.


Mungathe inu bwanji kukhulupirira, popeza mulandira ulemu wina kwa mnzake ndipo ulemu wakuchokera kwa Mulungu yekha simuufuna?


akukhala nao maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana; kwa iwonso udzipatule.


Chomwecho Samuele anabwerera natsata Saulo; ndi Saulo analambira Yehova.


Pamenepo Saulo anati, Ndinachimwa; bwera, mwana wanga Davide; pakuti sindidzakuchitiranso choipa, popeza moyo wanga unali wa mtengo wapatali pamaso pako lero; ona, ndinapusa ndi kulakwa kwakukulu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa