Numeri 21:7 - Buku Lopatulika7 Ndipo anthu anadza kwa Mose, nati, Tachimwa, popeza tinanena motsutsana ndi Yehova, ndi inu; pempherani kwa Yehova kuti atichotsere njokazi. Ndipo Mose anawapempherera anthu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Ndipo anthu anadza kwa Mose, nati, Tachimwa, popeza tinanena motsutsana ndi Yehova, ndi inu; pempherani kwa Yehova kuti atichotsere njokazi. Ndipo Mose anawapempherera anthu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Ndipo anthu adabwera kwa Mose, namuuza kuti, “Pepani tidachimwa poti tidakangana ndi Chauta ndi inu nomwe. Mupemphere kwa Chauta kuti atichotsere njokazi.” Choncho Mose adaŵapempherera anthuwo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Anthuwo anabwera kwa Mose ndi kunena kuti, “Tachimwa chifukwa tayankhula motsutsana ndi Yehova komanso inu. Pempherani kwa Yehova kuti atichotsere njokazi.” Tsono Mose anapempherera anthuwo. Onani mutuwo |
Ndipo tsono, mudzitengere ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri, mumuke kwa mtumiki wanga Yobu, mudzifukizire nokha nsembe yopsereza; ndi mtumiki wanga Yobu adzapempherera inu, pakuti ndidzamvomereza iyeyu, kuti ndisachite nanu monga mwa kupusa kwanu; popeza simunandinenere choyenera monga ananena mtumiki Yobu.