Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 26:21 - Buku Lopatulika

21 Pamenepo Saulo anati, Ndinachimwa; bwera, mwana wanga Davide; pakuti sindidzakuchitiranso choipa, popeza moyo wanga unali wa mtengo wapatali pamaso pako lero; ona, ndinapusa ndi kulakwa kwakukulu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Pamenepo Saulo anati, Ndinachimwa; bwera, mwana wanga Davide; pakuti sindidzakuchitiranso choipa, popeza moyo wanga unali wa mtengo wapatali pamaso pako lero; ona, ndinapusa ndi kulakwa kwakukulu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Tsono Saulo adati, “Ndachimwa. Bwerera, mwana wanga Davide, sindidzakuchitanso choipa, popeza kuti moyo wanga wauwona ngati wa mtengo wapatali. Ndithu ndachita zauchitsiru ndipo ndachimwa kwambiri.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Ndipo Sauli anati, “Ine ndachimwa. Bwerera mwana wanga Davide. Sindidzakuchitanso choyipa popeza lero wauwona moyo wanga ngati wamtengowapatali. Taona, ndachita zauchitsiru ndipo ndachimwa kwambiri.”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 26:21
16 Mawu Ofanana  

Ndipo anabwerezanso kutuma mtsogoleri wachitatu ndi makumi asanu ake. Nakwera mtsogoleri wachitatuyo, nadzagwada ndi maondo ake pamaso pa Eliya, nampembedza, nanena naye, Munthu wa Mulungu inu, ndikupemphani, moyo wanga ndi moyo wa anyamata anu makumi asanu awa akhale a mtengo wake pamaso panu.


Taonani, watsika moto wakumwamba, nunyeketsa atsogoleri awiri oyamba aja pamodzi ndi makumi asanu ao; koma tsopano moyo wanga ukhale wa mtengo wake pamaso panu.


Imfa ya okondedwa ake nja mtengo wake pamaso pa Yehova.


Popeza chiombolo cha moyo wao ncha mtengo wake wapatali, ndipo chilekeke nthawi zonse.


Adzaombola moyo wao ku chinyengo ndi chiwawa; ndipo mwazi wao udzakhala wa mtengo pamaso pake.


Ndipo Farao anatumiza, naitana Mose ndi Aroni, nanena nao, Ndachimwa tsopano; Yehova ndiye wolungama, ine ndi anthu anga ndife oipa.


Pamenepo Balamu anati kwa mthenga wa Yehova, Ndachimwa, popeza sindinadziwe kuti munaima mondiletsa m'njira; ndipo tsopano, ngati chikuipirani, ndibwerera.


nanena, Ndinachita koipa ine, pakupereka mwazi wosalakwa. Koma iwo anati, Tili nacho chiyani ife? Udzionere wekha.


Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Munachita kopusa; simunasunge lamulo la Yehova Mulungu wanu, limene Iye anakulamulirani; mwenzi Yehova atakhazikitsa nthawi ino ufumu wanu, ukhale pa Israele nthawi yosatha.


Ndipo Saulo anati kwa Samuele, Ndinachimwa; pakuti ndinalumpha lamulo la Yehova, ndi mau anu omwe; chifukwa ndinaopa anthuwo, ndi kumvera mau ao.


Pomwepo iye anati, Ndinachimwa, koma mundichitire ulemu tsopano pamaso pa akulu a anthu anga, ndi pamaso pa Israele, nimubwerere pamodzi ndi ine, kuti ndikalambire Yehova Mulungu wanu.


Pomwepo mafumu a Afilisti anatuluka; ndipo nthawi zonse anatuluka iwo, Davide anali wochenjera koposa anyamata onse a Saulo, chomwecho dzina lake linatamidwa kwambiri.


Nati kwa Davide, Iwe ndiwe wolungama woposa ine; popeza unandibwezera zabwino, koma ine ndinakubwezera zoipa.


Davide nayankha, nati, Tapenyani mkondo wa mfumu! Abwere mnyamata wina kuutenga.


Ndipo onani, monga lero ndinasamalira ndithu moyo wanu, momwemo usamaliridwe ndithu moyo wanga pamaso pa Yehova, ndipo Iye andipulumutse ku masautso onse.


Ndipo anauza Saulo kuti Davide anathawira ku Gati; ndipo iye sanamfunenso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa