Eksodo 20:12 - Buku Lopatulika Uzilemekeza atate wako ndi amai ako; kuti achuluke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Uzilemekeza atate wako ndi amai ako; kuti achuluke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Uzilemekeza atate ndi amai ako, kuti masiku a moyo wako achuluke m'dziko limene Chauta, Mulungu wako, akukupatsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Lemekeza abambo ako ndi amayi ako kuti ukhale ndi moyo wautali mʼdziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa. |
Tsono Bateseba ananka kwa mfumu Solomoni kukanenera Adoniya kwa iye. Ndipo mfumu inanyamuka kukomana naye, namuweramira nakhalanso pa mpando wake wachifumu, naikitsa mpando wina wa amake wa mfumu, nakhala iye ku dzanja lake lamanja.
Ndipo Elisa anapenya, nafuula, Atate wanga, atate wanga, galeta wa Israele ndi apakavalo ake! Koma analibe kumpenyanso; nagwira zovala zakezake, nazing'amba pakati.
Diso lochitira atate wake chiphwete, ndi kunyoza kumvera amake, makwangwala a kumtsinje adzalikolowola, ana a mphungu adzalidya.
Ndipo Yeremiya anati kwa nyumba ya Arekabu, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Chifukwa mwamvera lamulo la Yonadabu kholo lanu, ndi kusunga zonse anakulangizani inu, ndi kuchita monga mwa zonse anakuuzani inu;
ndiponso musamange nyumba, musafese mbeu, musaoke mipesa, musakhale nayo; koma masiku anu onse mudzakhale m'mahema; kuti mukhale ndi moyo masiku ambiri m'dziko limene mukhalamo alendo.
Mwa iwe anapepula atate ndi mai, pakati pa iwe anamchitira mlendo momzunza, mwa iwe anazunza ana amasiye, ndi mkazi wamasiye.
Aliyense aope mai wake, ndi atate wake; nimusunge masabata anga; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
Pali aimvi uziwagwadira, nuchitire ulemu munthu wokalamba; nuope Mulungu wako; Ine ndine Yehova.
Mwana alemekeza atate wake, ndi mnyamata mbuye wake; ngati Ine tsono ndine atate, uli kuti ulemu wanga? Ngati Ine ndine mbuye, kundiopa kuli kuti? Ati Yehova wa makamu kwa inu ansembe akupeputsa dzina langa. Ndipo mukuti, Tapeputsa dzina lanu motani?
Udziwa malamulo: Usaphe, Usachite chigololo, Usabe, Usachite umboni wakunama, Usanyenge, Lemekeza atate wako ndi amai ako.
Pakuti Mose anati, Lemekeza atate wako ndi amai ako; ndipo iye wakunenera zoipa atate wake kapena amai wake, afe ndithu;
Udziwa malamulo. Usachite chigololo, Usaphe, Usabe, Usachite umboni wonama, Lemekeza atate wako ndi amai ako.
Potero muzisunga malamulo onsewa ndikuuzani lero lino, kuti mukhale amphamvu, ndi kulowa ndi kulandira dziko, limene munkako kulilandira;
ndi kuti masiku anu achuluke m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, kuti adzawapatsa iwo ndi mbeu zao, dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.
Munthu akakhala naye mwana wamwamuna wopulukira, ndi wopikisana naye, wosamvera mau a atate wake, kapena mau a mai wake, wosawamvera angakhale anamlanga;
Muzikhala nao mwala wa muyeso wofikira ndi woyenera; mukhale nao muyeso wa efa wofikira ndi woyenera; kuti masiku anu achuluke m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.
Pakuti sichikhala kwa inu chinthu chopanda pake, popeza ndicho moyo wanu, ndipo mwa chinthu ichi mudzachulukitsa masiku anu m'dziko limene muolokera Yordani, kulilandira.
ndiitana kumwamba ndi dziko lapansi zichite mboni pa inu lero lino, kuti mudzaonongeka msangatu kuchotsedwa ku dziko limene muolokera Yordani kulilandira likhale lanulanu; masiku anu sadzachuluka pamenepo, koma mudzaonongeka konse.
Muzisunga malemba ake, ndi malamulo ake, amene ndikuuzani lero lino, kuti chikukomereni inu ndi ana anu akukutsatani, ndi kuti masiku anu achuluke padziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanu kosatha.
Lemekeza atate wako ndi amai ako, monga Yehova Mulungu wako anakulamulira; kuti masiku ako achuluke, ndi kuti chikukomere, m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.
Muziyenda m'njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani, kuti mukakhale ndi moyo, ndi kuti chikukomereni, ndi kuti masiku anu achuluke m'dziko limene mudzakhala nalo lanulanu.
kuti muope Yehova Mulungu wanu, kusunga malemba ake onse ndi malamulo ake, amene ndikuuzani inu ndi ana anu, ndi zidzukulu zanu, masiku onse a moyo wanu, ndi kuti masiku anu achuluke.
Ndipo Davide anachoka kumeneko kunka Mizipa wa ku Mowabu; nati kwa mfumu ya Mowabu, Mulole atate wanga ndi mai wanga atuluke nakhale nanu, kufikira ndidziwa chimene Mulungu adzandichitira.