Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 22:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo Davide anachoka kumeneko kunka Mizipa wa ku Mowabu; nati kwa mfumu ya Mowabu, Mulole atate wanga ndi mai wanga atuluke nakhale nanu, kufikira ndidziwa chimene Mulungu adzandichitira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo Davide anachoka kumeneko kunka Mizipa wa ku Mowabu; nati kwa mfumu ya Mowabu, Mulole atate wanga ndi mai wanga atuluke nakhale nanu, kufikira ndidziwa chimene Mulungu adzandichita.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Pambuyo pake Davide adachoka kumeneko, napita ku Mizipa ku Mowabu. Adapempha mfumu ya ku Mowabu kuti, “Chonde, bwanji bambo wanga ndi mai wanga akhale nao kuno, mpaka nditadziŵa zimene Mulungu adzandichitire.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Kuchokera kumeneko Davide anapita ku Mizipa ku Mowabu ndipo anapempha mfumu ya Mowabu kuti, “Bwanji abambo ndi amayi anga akhale nanu mpaka ine nditadziwa chimene Mulungu adzachite nane?”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 22:3
15 Mawu Ofanana  

Ndipo Yosefe anakhazika atate wake ndi abale ake, napatsa iwo pokhala m'dziko la Ejipito, m'dera lokometsetsa la m'dziko, m'dziko la Ramsesi, monga analamulira Farao.


Ndipo anakantha Amowabu nawayesa ndi chingwe, nawagonetsa pansi; ndipo anawayesera zingwe ziwiri kupha, ndi chingwe chimodzi chathunthu kusunga ndi moyo. Ndipo Amowabu anakhala anthu a Davide, nabwera nayo mitulo.


Uzilemekeza atate wako ndi amai ako; kuti achuluke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.


Koma ngati wamasiye wina ali nao ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kuchitira ulemu a m'banja lao, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu.


Pamenepo mzimu wa Yehova unamdzera Yefita, napitira iye ku Giliyadi, ndi Manase, napitira ku Mizipa wa Giliyadi, ndi kuchokera ku Mizipa wa Giliyadi anapitira kwa ana a Amoni.


Ndiponso Rute Mmowabu, mkazi wa Maloni ndamgula akhale mkazi wanga kuukitsa dzina la wakufayo pa cholowa chake; kuti dzina la wakufayo lisaiwalike pakati pa abale ake, ndi pa chipata cha malo ake; inu ndinu mboni lero lino.


Ndi akazi anansi ake anamutcha dzina, ndi kuti, Kwa Naomi kwambadwira mwana; namutcha dzina lake Obedi; ndiye atate wa Yese atate wa Davide.


Ndipo pamene Saulo atakhazikitsa ufumu wa pa Israele, iye anaponyana ndi adani ake onse pozungulira ponse, ndi Mowabu, ndi ana a Amoni, ndi Edomu ndi mafumu a Zoba, ndi Afilisti; ndipo paliponse anapotolokerapo, anawalanga.


Ndipo yense wosautsidwa, ndi yense wa ngongole, ndi yense wowawidwa mtima, anaunjikana kwa iye; iye nakhala mtsogoleri wao; ndipo anali nao anthu ngati mazana anai.


Ndipo anawatenga kunka nao pamaso pa mfumu ya Mowabu; ndipo iwo anakhala naye nthawi yonse Davide anali ku lingalo.


Ndipo Samuele anamuuza zonse, sanambisire kanthu. Ndipo iye anati, Ndiye Yehova; achite chomkomera pamaso pake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa