Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 20:12 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 “Lemekeza abambo ako ndi amayi ako kuti ukhale ndi moyo wautali mʼdziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

12 Uzilemekeza atate wako ndi amai ako; kuti achuluke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Uzilemekeza atate wako ndi amai ako; kuti achuluke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 “Uzilemekeza atate ndi amai ako, kuti masiku a moyo wako achuluke m'dziko limene Chauta, Mulungu wako, akukupatsa.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 20:12
42 Mawu Ofanana  

Tsono Yosefe anawachotsa ana aja pa mawondo a Israeli ndipo anamuweramira nkhope pansi.


Choncho ana a Yakobo anachita monga momwe abambo awo anawalamula:


Batiseba atapita kwa Mfumu Solomoni kukayankhula naye mʼmalo mwa Adoniya, mfumu inanyamuka kukumana naye, ndipo inaweramira amayi akewo, kenaka inakhala pa mpando wake waufumu. Iye anayitanitsa mpando wina kuti amayi ake akhalepo ndipo anakhala pansi ku dzanja lake lamanja.


Elisa anaona zimenezi ndipo anafuwula kuti, “Abambo anga! Abambo anga! Magaleta a Israeli ndi anthu ake okwera pa akavalo!” Ndipo Elisa sanamuonenso Eliyayo. Pamenepo Elisa anagwira zovala zake nazingʼamba pakati.


“Munthu aliyense amene amenya abambo ake kapena mayi ake ayenera kuphedwa.


“Aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa.


Chitsiru chimanyoza mwambo wa abambo ake, koma wochenjera amasamala chidzudzulo.


Zidzukulu ndiye ulemu wa anthu okalamba, ndipo makolo ndiye ulemerero wa ana.


Ngati munthu atemberera abambo ake kapena amayi ake, moyo wake udzazimitsidwa ngati nyale mu mdima wandiweyani.


Amene amabera abambo ake kapena amayi ake namanena kuti “kumeneko sikulakwa,” ndi mnzake wa munthu amene amasakaza.


Mʼdzanja lake lamanja muli moyo wautali; mʼdzanja lake lamanzere muli chuma ndi ulemu.


“Alipo ena amene amatemberera abambo awo, ndipo sadalitsa amayi awo.


Aliyense amene amanyoza abambo ake, ndi kunyozera kumvera amayi ake, makwangwala a ku chigwa adzamukolowola maso ndipo mphungu zidzadya mnofu wake.


Yeremiya anawuza banja la Arekabu mawu onse a Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, kuti, “Munamvera lamulo la kholo lanu Yehonadabu ndipo mwatsatira malangizo ake onse ndi kuchita chilichonse chimene anakulamulani.”


Musadzamange nyumba kapena kufesa mbewu, kapena kulima minda ya mpesa; musadzakhale ndi zinthu zimenezi. Mʼmalo mwake muzidzakhale mʼmatenti. Mukadzatero mudzakhala nthawi yayitali mʼdziko limene mukukhalamo.’


Mu mzindamo anthu amanyoza abambo ndi amayi awo. Iwo amapondereza alendo ndi kuzunza ana amasiye ndi akazi amasiye.


“ ‘Aliyense mwa inu azilemekeza abambo ake ndi amayi ake. Ndipo muzisunga masabata anga. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.


“ ‘Muzikhala mwa ulemu pamaso pa munthu wachikulire, ndipo muzichitira ulemu munthu wokalamba. Kumeneko ndiye kuopa Mulungu wanu. Ine ndine Yehova.


“Mwana amalemekeza abambo ake, ndipo wantchito amaopa abwana ake. Ngati Ine ndine abambo anu, ulemu wanga uli kuti? Ngati ndine mbuye wanu, nanga kundiopa kuli kuti?” Akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Ndinu, inu ansembe, amene mumanyoza dzina langa. “Komatu mukufunsa kuti, ‘Kodi timanyoza dzina lanu bwanji?’


lemekeza abambo ako ndi amayi ako ndipo konda mnansi wako monga iwe mwini.”


Iwe umadziwa malamulo: ‘Usaphe, usachite chigololo, usabe, usapereke umboni wonama, usachite chinyengo, lemekeza abambo ndi amayi ako.’ ”


Pakuti Mose anati, ‘Lemekeza abambo ako ndi amayi ako,’ ndipo, ‘aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa.’


Iwe umadziwa malamulo: ‘Usachite chigololo, usaphe, usabe, usapereke umboni wonama, lemekeza abambo ndi amayi ako.’ ”


Gonjeranani wina ndi mnzake, kuonetsa kuopa Khristu.


Tsono muzisunga malamulo onse amene ndikukupatsani lero kuti mukhale ndi mphamvu ndi kuti mupite kukalanda mʼdziko limene mwakhala pangʼono kulowamo mukawoloka Yorodani,


ndiponso kuti mukhalitse mʼdziko limene Yehova analumbira kupatsa makolo anu ndi zidzukulu zawo, lomwe ndi dziko loyenda mkaka ndi uchi.


Ngati munthu ali ndi mwana wamwamuna wosamvera ndi wowukira amene samvera a abambo ake ndi amayi ake akamuweruza,


Muyenera kukhala ndi miyeso ndi milingo yoyenera ndi yosanyenga kuti mukhalitse mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.


“Ndi wotembereredwa munthu amene sachitira ulemu abambo ake kapena amayi ake.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”


Mawuwa sikuti ndi mawu achabe kwa inu. Mawuwa ndi moyo wanu. Mukawamvera mudzakhala ndi moyo wautali mʼdziko limene mukukalitenga kukhala lanu mukawoloka Yorodani.”


ine ndi kuti kumwamba ndi dziko lapansi zikhale mboni lero zokutsutsani kuti mudzawonongedwa msanga ndipo mudzachotsedwa mʼdziko limene mutenge mukawoloka Yorodani. Simudzakhalitsa kumeneko koma mudzawonongedwa ndithu.


Sungani malangizo ake ndi malamulo ake amene ndikukupatsani lero lino, kuti zikuyendereni bwino inu ndi ana anu kutsogoloko, ndi kuti mukhalitse mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kwa nthawi zonse.


“Lemekeza abambo ako ndi amayi ako monga Yehova Mulungu wako wakulamulira iwe kuti ukhale ndi moyo wautali ndi kuti zikuyendere bwino mʼdziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.


Muyende mʼnjira yonse imene Yehova Mulungu wanu wakulamulirani kuti mukhale ndi moyo ndi kupambana, ndi kuti masiku anu achuluke mʼdziko limene mudzatengelo.


kuti inuyo, ana anu, ndi zidzukulu zanu mʼtsogolomo mudzaope Yehova Mulungu wanu moyo wanu wonse posunga malangizo ndi malamulo ake onse amene ndinakupatsani inu kuti musangalale ndi moyo wautali.


Inu ana, mverani makolo anu mu zonse pakuti izi zimakondweretsa Ambuye.


Choncho Rute anapita ku malo opunthirawo ndipo anachita monga momwe apongozi ake anamuwuza.


Kuchokera kumeneko Davide anapita ku Mizipa ku Mowabu ndipo anapempha mfumu ya Mowabu kuti, “Bwanji abambo ndi amayi anga akhale nanu mpaka ine nditadziwa chimene Mulungu adzachite nane?”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa