Malaki 1:6 - Buku Lopatulika6 Mwana alemekeza atate wake, ndi mnyamata mbuye wake; ngati Ine tsono ndine atate, uli kuti ulemu wanga? Ngati Ine ndine mbuye, kundiopa kuli kuti? Ati Yehova wa makamu kwa inu ansembe akupeputsa dzina langa. Ndipo mukuti, Tapeputsa dzina lanu motani? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Mwana alemekeza atate wake, ndi mnyamata mbuye wake; ngati Ine tsono ndine atate, uli kuti ulemu wanga? Ngati Ine ndine mbuye, kundiopa kuli kuti? Ati Yehova wa makamu kwa inu ansembe akupeputsa dzina langa. Ndipo mukuti, Tapeputsa dzina lanu motani? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Mwana amapatsa ulemu bambo wake ndipo kapolo amaopa mbuye wake. Ngati Ine ndine bambo wanu, nanga ulemu wanga uli kuti? Ngati ndine mbuye wanu, nanga kundiwopa kuli kuti, Ansembe inu, amene mumanyoza dzina langa. Komabe mumanena kuti, kodi dzina lanu timalinyoza bwanji? Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 “Mwana amalemekeza abambo ake, ndipo wantchito amaopa abwana ake. Ngati Ine ndine abambo anu, ulemu wanga uli kuti? Ngati ndine mbuye wanu, nanga kundiopa kuli kuti?” Akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Ndinu, inu ansembe, amene mumanyoza dzina langa. “Komatu mukufunsa kuti, ‘Kodi timanyoza dzina lanu bwanji?’ Onani mutuwo |