Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Malaki 1:7 - Buku Lopatulika

7 Mupereka mkate wodetsedwa paguwa langa la nsembe; ndipo mukuti, Takudetsani motani? M'menemo, mwakuti munena, Gome la Yehova nlonyozeka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Mupereka mkate wodetsedwa pa guwa langa la nsembe; ndipo mukuti, Takudetsani motani? M'menemo, mwakuti munena, Gome la Yehova nlonyozeka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Mumalinyoza pakupereka chakudya chosayenera pa guwa langa lansembe. Inu mumafunsabe kuti, kodi ife takunyozani bwanji? Mwandinyoza pakuganiza kuti tebulo la Chauta nlonyozeka.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 “Inu mwanyoza dzina langa popereka chakudya chodetsedwa pa guwa langa lansembe. “Komatu mukufunsa kuti, ‘Kodi ife takunyozani bwanji?’ “Mwandinyoza ponena kuti tebulo la Yehova ndi lonyozeka.

Onani mutuwo Koperani




Malaki 1:7
14 Mawu Ofanana  

Guwa la nsembe linali lamtengo, msinkhu wake mikono itatu, ndi m'litali mwake mikono iwiri, ndi ngodya zake, ndi tsinde lake, ndi thupi, nza mtengo; ndipo ananena ndi ine, Ili ndiko gome lili pamaso pa Yehova.


iwowa adzalowa m'malo anga opatulika, nadzayandikira kugome langa kunditumikira, nadzasunga udikiro wanga.


Nsembe iliyonse yaufa, imene mubwera nayo kwa Yehova, isapangike ndi chotupitsa, pakuti musamatenthera Yehova nsembe yamoto yachotupitsa, kapena yauchi.


Azikhala opatulikira Mulungu wao, osaipsa dzina la Mulungu wao; popeza amapereka nsembe zamoto za Yehova, mkate wa Mulungu wao; chifukwa chake akhale opatulika.


Chifukwa chake umpatule; popeza amapereka mkate wa Mulungu wako; umuyese wopatulika; pakuti Ine Yehova wakupatula iwe, ndine woyera.


Ndipo wansembe azitenthe paguwa la nsembe; ndicho chakudya cha nsembe yamoto ya kwa Yehova.


Koma inu muliipsa, pakunena inu, Gome la Ambuye laipsidwa, ndi zipatso zake, chakudya chake, chonyozeka.


Mukutinso, Taonani, ncholemetsa ichi! Ndipo mwachipeputsa, ati Yehova wa makamu; ndipo mwabwera nazo zofunkha, ndi zotsimphina, ndi zodwala; momwemo mubwera nayo nsembe; kodi ndiyenera kuilandira kudzanja lanu? Ati Yehova.


Ndipo pamene mupereka yakhungu ikhale nsembe, mukuti, Palibe choipa! Ndi popereka yotsimphina ndi yodwala, palibe choipa! Kaiperekeni kwa kazembe wanu, mudzamkomera kodi? Kapena adzakuvomerezani kodi? Ati Yehova wa makamu.


Simungathe kumwera chikho cha Ambuye, ndi chikho cha ziwanda; simungathe kulandirako kugome la Ambuye, ndi kugome la ziwanda.


Koma ikakhala nacho chilema, yotsimphina, kapena yakhungu, chilema chilichonse choipa, musamaiphera nsembe Yehova Mulungu wanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa