2 Mafumu 2:12 - Buku Lopatulika12 Ndipo Elisa anapenya, nafuula, Atate wanga, atate wanga, galeta wa Israele ndi apakavalo ake! Koma analibe kumpenyanso; nagwira zovala zakezake, nazing'amba pakati. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Ndipo Elisa anapenya, nafuula, Atate wanga, atate wanga, galeta wa Israele ndi apakavalo ake! Koma analibe kumpenyanso; nagwira zovala zakezake, nazing'amba pakati. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 Elisa adaona zimenezi nafuula kuti, “Bambo wanga, Bambo wanga! Magaleta a Aisraele ndi anthu ake okwera pa akavalo.” Ndipo sadamuwonenso Eliyayo. Tsono Elisa adagwira zovala zake nazing'amba paŵiri. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Elisa anaona zimenezi ndipo anafuwula kuti, “Abambo anga! Abambo anga! Magaleta a Israeli ndi anthu ake okwera pa akavalo!” Ndipo Elisa sanamuonenso Eliyayo. Pamenepo Elisa anagwira zovala zake nazingʼamba pakati. Onani mutuwo |