Ndipo ndidzaikira anthu anga Israele malo, ndi kuwaoka kuti akakhale m'malo ao a iwo okha, osasunthikanso. Ndipo anthu a mphulupulu sadzawavutanso, monga poyamba paja,
Eksodo 15:17 - Buku Lopatulika Mudzawafikitsa, ndi kuwaoka paphiri la cholowa chanu, pamalo pamene munadzipangira mukhalepo, Yehova, malo oyera, amene manja anu, Ambuye, adakhazikika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mudzawafikitsa, ndi kuwaoka pa phiri la cholowa chanu, pamalo pamene munadzipangira mukhalepo, Yehova, malo oyera, amene manja anu, Ambuye, adakhazikika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mudzaŵaloŵetsa ndi kuŵakhazika pa phiri lanu, pa malo amene Inu Chauta mudaŵapanga kuti akhale anu, m'nyumba yopembedzera imene Inu mudaimanga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu mudzawalowetsa ndi kuwakhazikitsa pa phiri lanu. Pa malo pamene Inu Yehova munawapanga kuti muzikhalapo; malo wopatulika amene Inu Ambuye munawakonza ndi manja anu. |
Ndipo ndidzaikira anthu anga Israele malo, ndi kuwaoka kuti akakhale m'malo ao a iwo okha, osasunthikanso. Ndipo anthu a mphulupulu sadzawavutanso, monga poyamba paja,
Ine ndakumangirani ndithu nyumba yokhalamo Inu, ndiyo malo okhalamo Inu nthawi zosatha.
Inu munapirikitsa amitundu ndi dzanja lanu, koma iwowa munawaoka; munasautsa mitundu ya anthu, ndipo munawaingitsa.
Muchitiranji nsanje mapiri inu a mitumitu, ndi phirilo Mulungu analikhumba, akhaleko? Inde, Yehova adzakhalabe komweko kosatha.
Mwa chifundo chanu mwatsogolera anthu amene mudawaombola; mwamphamvu yanu mudawalondolera njira yakunka pokhala panu poyera.
Taona, ndituma mthenga akutsogolere, kukusunga panjira, ndi kukufikitsa pamaso pomwe ndakonzeratu.
Ndipo tsopano, muka, tsogolera anthu kunka nao kumene ndinakuuza; taona, mthenga wanga akutsogolera; koma tsiku lakuwazonda Ine ndidzawalanga chifukwa cha kuchimwa kwao.
Ndipo Ine ndinakuoka mpesa wangwiro, mbeu yoona; kodi bwanji wandisandukira Ine mbeu yopanda pake, ya mpesa wachilendo?
Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Kawirinso adzanena mau awa m'dziko la Yuda ndi m'mizinda yake, pamene ndibwezanso undende wao; Yehova akudalitse iwe, wokhalamo chilungamo, iwe phiri lopatulika.
Inde, ndidzasekerera iwo kuwachitira zabwino, ndipo ndidzawaoka ndithu m'dziko lino ndi mtima wanga wonse ndi moyo wanga wonse.
Ndipo ndidzapangana nao pangano la mtendere, lidzakhala pangano losatha nao, ndipo ndidzawakhazika, ndi kuwachulukitsa, ndi kuika malo anga opatulika pakati pao kosatha.
Ndipo amitundu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova wakupatula Israele, pokhala pakati pao malo anga opatulika kosatha.
Adzaitana mitundu ya anthu afike kuphiri; apo adzaphera nsembe za chilungamo; popeza adzayamwa zochuluka za m'nyanja, ndi chuma chobisika mumchenga.
Koma mukayesa dziko la cholowa chanu nchodetsa, olokani kulowa m'dziko la cholowa cha Yehova m'mene chihema cha Yehova chikhalamo, nimukhale nacho cholowa pakati pa ife; koma musapikisana ndi Yehova kapena kupikisana nafe, ndi kudzimangira nokha guwa la nsembe, pamodzi ndi guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu.