Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 68:16 - Buku Lopatulika

16 Muchitiranji nsanje mapiri inu a mitumitu, ndi phirilo Mulungu analikhumba, akhaleko? Inde, Yehova adzakhalabe komweko kosatha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Muchitiranji nsanje mapiri inu a mitumitu, ndi phirilo Mulungu analikhumba, akhaleko? Inde, Yehova adzakhalabe komweko kosatha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Iwe phiri la nsonga zambiriwe, chifukwa chiyani ukuliyang'ana mwansanje phiri limene Mulungu adasankha kuti azikhalapo? Ndithu Chauta adzakhalapo mpaka muyaya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Muyangʼaniranji mwansanje inu mapiri a msonga zambiri, pa phiri limene Mulungu analisankha kuti azilamulira, kumene Yehova mwini adzakhalako kwamuyaya?

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 68:16
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anati kwa iye, Ndamva pemphero lako ndi pembedzero lako wandipembedza nalo; ndapatula nyumba imene waimangayi kuikamo dzina langa nthawi zosatha, ndipo maso anga ndi mtima wanga zidzakhala kumeneko masiku onse.


Mapiri anatumphatumpha ngati nkhosa zamphongo, timapiri ngati anaankhosa.


Munatumphatumphiranji ngati nkhosa zamphongo, mapiri inu? Ngati anaankhosa, zitunda inu?


Ndipo padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pansonga ya mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda; mitundu yonse idzasonkhana kumeneko.


Pamenepo padzakhala malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake, kumeneko muzibwera nazo zonse ndikuuzanizi; nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zophera, magawo anu onse a magawo khumi, ndi nsembe yokweza dzanja lanu, ndi zowinda zanu zosankhika zimene muzilonjezera Yehova.


Koma kumalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha mwa mafuko anu onse kuikapo dzina lake, ndiko ku chokhalamo chake, muzifunako, ndi kufikako;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa