Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 32:41 - Buku Lopatulika

41 Inde, ndidzasekerera iwo kuwachitira zabwino, ndipo ndidzawaoka ndithu m'dziko lino ndi mtima wanga wonse ndi moyo wanga wonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

41 Inde, ndidzasekerera iwo kuwachitira zabwino, ndipo ndidzawaoka ndithu m'dziko lino ndi mtima wanga wonse ndi moyo wanga wonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

41 Ndidzakondwera kuŵachitira zabwino. Ndipo ndidzaŵakhazikitsa m'dziko lino mokhulupirika ndi mtima wanga wonse ndi kufuna kwanga konse.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

41 Ndidzakondwera powachitira zabwino, ndipo ndidzawakhazikitsa ndithu mʼdziko lino ndi mtima wanga wonse ndi moyo wanga wonse.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 32:41
16 Mawu Ofanana  

Mudatenga mpesa kuchokera ku Ejipito, munapirikitsa amitundu ndi kuuoka uwu.


Anthu ako adzakhalanso onse olungama; dzikolo lidzakhala cholowa chao kunthawi zonse, nthambi yooka Ine, ntchito ya manja anga, kuti Ine ndikuzidwe.


Iwe sudzatchedwanso Wosiyidwa; dziko lako silidzatchedwanso Bwinja; koma iwe udzatchedwa Hefiziba ndi dziko lako Beula; pakuti Yehova akondwera mwa iwe, ndipo dziko lako lidzakwatiwa.


Pakuti monga mnyamata akwatira namwali, momwemo ana ako aamuna adzakukwatira iwe; ndi monga mkwati akondwera ndi mkwatibwi, momwemo Mulungu wako adzakondwera nawe.


Ndipo ndidzasangalala mu Yerusalemu, ndi kukondwera mwa anthu anga; ndipo mau akulira sadzamvekanso mwa iye, pena mau akufuula.


Ndipo mphindi imene ndikanenera mtundu, ndi ufumu, kuti ndimangitse mudzi wake ndi kuuoka;


Pakuti ndidzaika maso anga pa iwo kuti ndiwachitire iwo bwino, ndipo ndidzawabwezanso kudziko ili: ndipo ndidzamangitsa mudzi wao, osawapasula; ndi kuwabzala, osawazula iwo.


Ndipo padzakhala kuti, monga ndayang'anira iwo kuzula ndi kupasula ndi kugwetsa, ndi kuononga ndi kusautsa; momwemo ndidzayang'anira iwo kumangitsa mudzi ndi kubzala, ati Yehova.


Pamenepo amitundu otsala pozungulira panu adzadziwa kuti Ine Yehova ndamanga malo opasuka, ndi kubzala pamene panali chipululu; Ine Yehova ndanena ndidzachita.


Ndidzakhala kwa Israele ngati mame; adzachita maluwa ngati kakombo, ndi kutambalalitsa mizu yake ngati Lebanoni.


Ndipo ndidzawaoka m'dziko mwao ndipo sadzazulidwanso m'dziko lao limene ndawapatsa, ati Yehova Mulungu wako.


Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, wakukhululukira mphulupulu, wakupitirira zolakwa za otsala a cholowa chake? Sasunga mkwiyo wake kunthawi yonse popeza akondwera nacho chifundo.


Yehova Mulungu wako ali pakati pako, wamphamvu wakupulumutsa; adzakondwera nawe ndi chimwemwe, adzakhala wopanda thamo m'chikondi chake; adzasekerera nawe ndi kuimbirapo.


Ndipo kudzali kuti, monga Yehova anakondwera nanu kukuchitirani zabwino, ndi kukuchulukitsani; momwemo Yehova adzakondwera nanu kutayikitsa ndi kuononga inu, ndipo adzakuzulani kudziko kumene mulowako kulilandira.


Ndipo Yehova Mulungu wanu adzakuchulukitsirani ntchito zonse za dzanja lanu, zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za zoweta zanu, ndi zipatso za nthaka yanu, zikukomereni; popeza Yehova Mulungu wanu adzakondweranso kukuchitirani zokoma; monga anakondwera ndi makolo anu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa