Eksodo 15:16 - Buku Lopatulika16 Kuopa kwakukulu ndi mantha ziwagwera; padzanja lanu lalikulu akhala chete ngati mwala; kufikira apita anthu anu, Yehova, kufikira apita anthu amene mudawaombola. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 Kuopa kwakukulu ndi mantha ziwagwera; pa dzanja lanu lalikulu akhala chete ngati mwala; kufikira apita anthu anu, Yehova, kufikira apita anthu amene mudawaombola. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa16 Onsewo agwidwa ndi mantha oopsa. Iwo akhala chete ngati mwala, chifukwa cha kuwopa mphamvu zanu zazikulu. Angokhala chete mpaka anthu anu, Inu Chauta, atabzola, anthu amene mudaŵaombola mu ukapolo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 Onse agwidwa ndi mantha woopsa. Popeza anaona mphamvu zanu zazikulu, iwo ayima chilili ngati mwala mpaka anthu anu, Inu Yehova atadutsa; inde mpaka atadutsa anthu amene munawagula. Onani mutuwo |
Ndiponso mtundu uti wa padziko lapansi ufanana ndi anthu anu, ndiwo Israele, amene Mulungu anakadziombolera akhale anthu ake, ndi kuti limveke dzina lake, ndi kukuchitirani zinthu zazikulu ndi kuchitira dziko lanu zoopsa, pamaso pa anthu anu, amene munadziombolera kuwatulutsa ku dziko la Ejipito mwa amitundu ndi milungu yao?