Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 15:17 - Buku Lopatulika

17 Mudzawafikitsa, ndi kuwaoka paphiri la cholowa chanu, pamalo pamene munadzipangira mukhalepo, Yehova, malo oyera, amene manja anu, Ambuye, adakhazikika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Mudzawafikitsa, ndi kuwaoka pa phiri la cholowa chanu, pamalo pamene munadzipangira mukhalepo, Yehova, malo oyera, amene manja anu, Ambuye, adakhazikika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Mudzaŵaloŵetsa ndi kuŵakhazika pa phiri lanu, pa malo amene Inu Chauta mudaŵapanga kuti akhale anu, m'nyumba yopembedzera imene Inu mudaimanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Inu mudzawalowetsa ndi kuwakhazikitsa pa phiri lanu. Pa malo pamene Inu Yehova munawapanga kuti muzikhalapo; malo wopatulika amene Inu Ambuye munawakonza ndi manja anu.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 15:17
24 Mawu Ofanana  

Ndipo ndidzaikira anthu anga Israele malo, ndi kuwaoka kuti akakhale m'malo ao a iwo okha, osasunthikanso. Ndipo anthu a mphulupulu sadzawavutanso, monga poyamba paja,


Ine ndakumangirani ndithu nyumba yokhalamo Inu, ndiyo malo okhalamo Inu nthawi zosatha.


Yuda anakhala malo ake oyera, Israele ufumu wake.


Koma Ine ndadzoza mfumu yanga Pa Ziyoni, phiri langa loyera.


Inu munapirikitsa amitundu ndi dzanja lanu, koma iwowa munawaoka; munasautsa mitundu ya anthu, ndipo munawaingitsa.


Muchitiranji nsanje mapiri inu a mitumitu, ndi phirilo Mulungu analikhumba, akhaleko? Inde, Yehova adzakhalabe komweko kosatha.


Msasa wake unali mu Salemu, ndipo pokhala Iye mu Ziyoni.


ndi tsinde limene dzanja lanu lamanja linaoka, ndi mphanda munadzilimbikitsira.


Mudatenga mpesa kuchokera ku Ejipito, munapirikitsa amitundu ndi kuuoka uwu.


Mwa chifundo chanu mwatsogolera anthu amene mudawaombola; mwamphamvu yanu mudawalondolera njira yakunka pokhala panu poyera.


Taona, ndituma mthenga akutsogolere, kukusunga panjira, ndi kukufikitsa pamaso pomwe ndakonzeratu.


Ndipo andimangire malo opatulika; kuti ndikhale pakati pao.


Ndipo tsopano, muka, tsogolera anthu kunka nao kumene ndinakuuza; taona, mthenga wanga akutsogolera; koma tsiku lakuwazonda Ine ndidzawalanga chifukwa cha kuchimwa kwao.


Ndipo Ine ndinakuoka mpesa wangwiro, mbeu yoona; kodi bwanji wandisandukira Ine mbeu yopanda pake, ya mpesa wachilendo?


Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Kawirinso adzanena mau awa m'dziko la Yuda ndi m'mizinda yake, pamene ndibwezanso undende wao; Yehova akudalitse iwe, wokhalamo chilungamo, iwe phiri lopatulika.


Inde, ndidzasekerera iwo kuwachitira zabwino, ndipo ndidzawaoka ndithu m'dziko lino ndi mtima wanga wonse ndi moyo wanga wonse.


Ndipo ndidzapangana nao pangano la mtendere, lidzakhala pangano losatha nao, ndipo ndidzawakhazika, ndi kuwachulukitsa, ndi kuika malo anga opatulika pakati pao kosatha.


Ndipo amitundu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova wakupatula Israele, pokhala pakati pao malo anga opatulika kosatha.


Adzaitana mitundu ya anthu afike kuphiri; apo adzaphera nsembe za chilungamo; popeza adzayamwa zochuluka za m'nyanja, ndi chuma chobisika mumchenga.


Koma mukayesa dziko la cholowa chanu nchodetsa, olokani kulowa m'dziko la cholowa cha Yehova m'mene chihema cha Yehova chikhalamo, nimukhale nacho cholowa pakati pa ife; koma musapikisana ndi Yehova kapena kupikisana nafe, ndi kudzimangira nokha guwa la nsembe, pamodzi ndi guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa