Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 14:22 - Buku Lopatulika

Ndipo ana a Israele analowa pakati pa nyanja pouma; ndi madziwo anakhala kwa iwo ngati khoma palamanja, ndi palamanzere.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo ana a Israele analowa pakati pa nyanja pouma; ndi madziwo anakhala kwa iwo ngati khoma palamanja, ndi palamanzere.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

ndipo adakhala ngati chipupa pa mbali zonse ziŵiri, motero Aisraele adaoloka pouma.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndipo Aisraeli anawoloka pakati pa nyanja powuma, madzi atasanduka khoma kumanja ndi kumanzere kwawo.

Onani mutuwo



Eksodo 14:22
27 Mawu Ofanana  

Ndipo anatenga chofunda cha Eliya chidamtayikiracho, napanda madziwo, nati, Ali kuti Yehova Mulungu wa Eliya? Ndipo atapanda madziwo anagawikana kwina ndi kwina, naoloka Elisa.


Ndipo Eliya anagwira chofunda chake, nachipindapinda napanda madzi, nagawikana kwina ndi kwina; ndipo anaoloka iwo onse awiri pansi pouma.


Ndipo munagawanitsa nyanja pamaso pao, napita iwo pakati pa nyanja pouma, ndipo munaponya mozama owalondola, ngati mwala m'madzi olimba.


Ndipo anadzudzula Nyanja Yofiira, ndipo inaphwa: Potero anawayendetsa mozama ngati m'chipululu.


Amene anagawa magawo Nyanja Yofiira; pakuti chifundo chake nchosatha.


Napititsa Israele pakati pake; pakuti chifundo chake nchosatha.


Anasanduliza nyanja ikhale mtunda. Anaoloka mtsinje choponda pansi, apo tinakondwera mwa Iye.


Mudagawa kasupe ndi mtsinje; mudaphwetsa mitsinje yaikulu.


Anagawa nyanja nawapititsapo; naimitsa madziwo ngati khoma.


Koma ana a Israele anayenda pouma pakati pa nyanja; ndi madziwo anakhala ngati khoma kwa iwo, palamanja ndi lamanzere.


Pakuti akavalo a Farao analowa m'nyanja, ndi magaleta ake ndi apakavalo ake, ndipo Yehova anawabwezera madzi a m'nyanja; koma ana a Israele anayenda pouma pakati pa nyanja.


Ndipo ndi mpumo wa m'mphuno mwanu madzi anaunjikika, mayendedwe ake anakhala chilili ngati mulu; zozama zinalimba m'kati mwa nyanja.


Ndipo Yehova adzaononga ndithu bondo la nyanja ya Ejipito; ndipo ndi mphepo yake yopsereza adzagwedeza dzanja lake pa Mtsinje, ndipo adzaimenya ikhale mphaluka zisanu ndi ziwiri, nadzaolotsa anthu pansi pouma.


Ndipo padzakhala khwalala la anthu ake otsala ochokera ku Asiriya; monga lija la Israele tsiku lokwera iwo kutuluka m'dziko la Ejipito.


Atero Yehova, amene akonza njira panyanja, ndi popita m'madzi amphamvu;


Kodi si ndiwe amene unaumitsa nyanja, madzi akuya kwambiri; anasandutsa nyanja zikhale njira ya kupitapo oomboledwa?


amene anayendetsa mkono wake waulemerero padzanja lamanja la Mose? Amene anagawanitsa madzi pamaso pao, kuti adzitengere mbiri yosatha?


Amene anawatsogolera kupitira mwa kuya monga kavalo m'chipululu osaphunthwa iwo?


Pakuti Ine, ati Yehova, ndidzakhala kwa iye linga lamoto pozungulira pake, ndipo ndidzakhala ulemerero m'kati mwake.


Ndipo anachokera ku Pihahiroti, naoloka pakati pa nyanja nalowa m'chipululu; nayenda ulendo wa masiku atatu m'chipululu cha Etamu, namanga mu Mara.


Pakuti sindifuna, kuti mukhale osadziwa, abale, kuti makolo athu onse anali pansi pa mtambo, naoloka nyanja onse;


Ndi chikhulupiriro anaoloka Nyanja Yofiira kupita ngati pamtunda: ndiko Aejipito poyesanso anamizidwa.


pamenepo madzi ochokera kumagwero anaima, nauka ngati mulu, kutalitu ku Adama, ndiwo mzinda wa ku mbali ya Zaretani; koma madzi akutsikira kunka ku nyanja ya chidikha, ndiyo Nyanja ya Mchere, anadulidwa konse; ndipo anthu anaoloka pandunji pa Yeriko.


Ndipo ansembe akulisenza likasa la chipangano la Yehova, anaima pouma pakati pa Yordani, ndi Aisraele onse anaoloka pouma mpaka mtundu wonse unatha kuoloka Yordani.


Pamenepo muzidziwitsa ana anu, ndi kuti, Israele anaoloka Yordani uyu pouma.


iwo anatikhalira ngati linga usana ndi usiku, nthawi yonse tinali nao ndi kusunga nkhosazo.