Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 2:5 - Buku Lopatulika

5 Pakuti Ine, ati Yehova, ndidzakhala kwa iye linga lamoto pozungulira pake, ndipo ndidzakhala ulemerero m'kati mwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Pakuti Ine, ati Yehova, ndidzakhala kwa iye linga lamoto pozungulira pake, ndipo ndidzakhala ulemerero m'kati mwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Chauta akuti Iye yemwe ndiye adzakhale linga lamoto loteteza mzindawo, ndipo adzaonetsa ulemerero wake m'kati mwake.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Ndipo Ine mwini ndidzakhala linga lamoto kuteteza mzindawo,’ akutero Yehova, ‘ndipo ndidzakhala ulemerero mʼkati mwake.’

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 2:5
28 Mawu Ofanana  

Monga mapiri azinga Yerusalemu, momwemo Yehova azinga anthu ake, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.


Ndipo Inu Yehova, ndinu chikopa changa; ulemerero wanga, ndi wondiweramutsa mutu wanga.


Mulungu ali m'kati mwake, sudzasunthika, Mulungu adzauthandiza mbandakucha.


Zungulirani Ziyoni, ndipo muuzinge, werengani nsanja zake.


Mulungu adziwika m'zinyumba zake ngati msanje.


Indedi chipulumutso chake chili pafupi ndi iwo akumuopa Iye; kuti m'dziko mwathu mukhale ulemu.


Tafuula, takuwa iwe, wokhala mu Ziyoni, chifukwa Woyera wa Israele wa m'kati mwako ali wamkulu.


Ndipo mwala wake udzachoka, chifukwa cha mantha, ndi akalonga ake adzaopa mbendera, ati Yehova, amene moto wake uli mu Ziyoni, ndi ng'anjo yake mu Yerusalemu.


Ndipo anthu anga adzakhala m'malo a mtendere, ndi mokhala mokhulupirika ndi mopuma mwa phee.


Koma pamenepo Yehova adzakhala ndi ife mu ulemerero, malo a nyanja zachitando ndi mitsinje; m'menemo ngalawa sizidzayenda ndi ngombo, ngakhale zombo zazikulu sizidzapita pamenepo.


Ndipo Yehova adzalenga pokhala ponse paphiri la Ziyoni, ndi pa misonkhano yake, mtambo ndi utsi usana, ndi kung'azimira kwa malawi a moto usiku; chifukwa kuti pa ulemerero wonse padzayalidwa chophimba.


Ndipo chingwe choyesera chidzatulukanso kulunjika ku chitunda cha Garebu, ndipo chidzazungulira kunka ku Gowa.


Chifukwa chake nenera, wobadwa ndi munthu iwe, uziti kwa Gogi, Atero Ambuye Yehova, Tsiku ilo, pokhala mosatekeseka anthu anga Israele, sudzachidziwa kodi?


Analiyesa mbali zake zinai, linali nalo linga pozungulira pake, utali wake mikono mazana asanu, chitando chake mikono mazana asanu, kusiyanitsa pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba.


Potuluka munthuyu kunka kum'mawa ndi chingwe choyesera m'dzanja lake, anayesa mikono chikwi chimodzi, nandipititsa pamadzi, madzi oyesa m'kakolo.


Chifukwa chake atero Yehova: Ndabwera kudza ku Yerusalemu ndi zachifundo; nyumba yanga idzamangidwamo, atero Yehova wa makamu, ndipo adzayesa Yerusalemu ndi chingwe.


Imba, nukondwere, mwana wamkazi wa Ziyoni; pakuti taonani, ndilinkudza, ndipo ndidzakhala pakati pako, ati Yehova.


Ndipo amitundu ambiri adzaphatikidwa kwa Yehova tsiku ilo, nadzakhala anthu anga; ndipo ndidzakhala pakati pako, ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma kwa iwe.


Ndipo Yehova adzaoneka pamwamba pao, ndi muvi wake udzatuluka ngati mphezi; ndipo Ambuye Mulungu adzaomba lipenga, nadzayenda ndi akamvulumvulu a kumwera.


Ndipo ndidzamangira nyumba yanga misasa, kuiletsera nkhondo, asapitepo munthu kapena kubweranso; ndipo wakuwasautsa sadzapitanso pakati pao; pakuti tsopano ndapenya ndi maso anga.


kuunika kukhale chivumbulutso cha kwa anthu a mitundu, ndi ulemerero wa anthu anu Israele.


Ndipo pamzinda sipafunika dzuwa, kapena mwezi wakuuwalira; pakuti ulemerero wa Mulungu uunikira umenewu, ndipo nyali yake ndiye Mwanawankhosa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa