Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 2:4 - Buku Lopatulika

4 nanena naye, Thamanga, lankhula ndi mnyamata uyu, ndi kuti, Mu Yerusalemu mudzakhala anthu ngati m'midzi yopanda malinga, chifukwa cha kuchuluka anthu ndi zoweta momwemo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 nanena naye, Thamanga, lankhula ndi mnyamata uyu, ndi kuti, M'Yerusalemu mudzakhala anthu ngati m'midzi yopanda malinga, chifukwa cha kuchuluka anthu ndi zoweta momwemo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Woyamba uja adauza mnzakeyo kuti, “Thamangira mnyamata wachingweyo, ukamuuze kuti mu Yerusalemu mudzakhala anthu ambiri ndiponso zoŵeta zochuluka, kotero kuti mzindawo udzakhala wopanda malinga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 ndipo anamuwuza kuti, “Thamanga, kamuwuze mnyamatayo kuti, ‘Yerusalemu udzakhala mzinda wopanda malinga chifukwa mudzakhala anthu ambiri ndiponso ziweto zochuluka.

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 2:4
24 Mawu Ofanana  

Chifukwa chake Ayuda a kumidzi, okhala m'mizinda yopanda malinga, amaliyesa tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi wa Adara tsiku la kukondwera ndi madyerero, ndi tsiku lokoma, ndi lakutumizirana magawo.


Tayang'ana pa Ziyoni, mzinda wa zikondwerero zathu; maso ako adzaona, Yerusalemu malo a phee, chihema chimene sichidzasunthidwa, zichiri zake sizidzazulidwa konse, zingwe zake sizidzadulidwa.


Ndine amene ndilimbitsa mau a mtumiki wanga, kuchita uphungu wa amithenga anga; ndi kunena za Yerusalemu, Adzakhalamo anthu; ndi za mizinda ya Yuda; Idzamangidwa; ndipo ndidzautsa malo abwinja ake.


Ana ako amasiye adzanena m'makutu ako, Malo andichepera ine, ndipatse malo, kuti ndikhalemo.


Taona, ndalenga wachipala amene avukuta moto wamakala, ndi kutulutsamo chida cha ntchito yake; ndipo ndalenga woononga kuti apasule.


Ndipo ndinati, Ha, Ambuye Mulungu! Taonani, sindithai kunena pakuti ndili mwana.


Ndipo Yuda ndi mizinda yake yonse adzakhalamo pamodzi; alimi, ndi okusa zoweta.


Taonani, masiku adza, ati Yehova, amene ndidzafesera nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda ndi mbeu ya anthu ndi mbeu ya nyama.


Monga khamu la kuthambo silingathe kuwerengedwa, ndi mchenga wa kunyanja sungathe kuyesedwa; chomwecho ndidzachulukitsa mbeu za Davide mtumiki wanga, ndi Alevi akunditumikira Ine.


nudzati, Ndidzakwera kunka kudziko la midzi yopanda malinga, ndidzanka kwa iwo amtendere okhala mosatekeseka, onsewo akukhala opanda malinga, opanda mapiringidzo, kapena zitseko;


Koma anyamata amene anai, Mulungu anawapatsa chidziwitso ndi luntha la m'mabuku ali onse, ndi nzeru; koma Daniele anali nalo luntha la m'masomphenya ndi maloto onse.


anyamata opanda chilema, a maonekedwe okoma, a luso la nzeru zonse, ochenjera m'kudziwa, a luntha lakuganizira, okhoza kuimirira m'chinyumba cha mfumu; ndi kuti awaphunzitse m'mabuku, ndi manenedwe a Ababiloni.


Tsiku lakumanga malinga ako, tsiku lomwelo lembalo lidzachotsedwa kunka kutali.


Chifukwa chake atero Yehova: Ndabwera kudza ku Yerusalemu ndi zachifundo; nyumba yanga idzamangidwamo, atero Yehova wa makamu, ndipo adzayesa Yerusalemu ndi chingwe.


Fuulanso, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu: Mizinda yanga idzalemerera ndi kufalikiranso; ndipo Yehova adzasangalatsanso Ziyoni, nadzasankhamo Yerusalemu.


Tsiku ilo ndidzaika akalonga a Yuda ngati phale la moto pansi pa nkhuni, ndi ngati muuni wamoto mwa mitolo ya tirigu; ndipo adzatha mitundu yonse ya anthu pozungulirapo, kudzanja lamanja ndi lamanzere; ndipo Yerusalemu adzakhalanso m'malo mwake, mu Yerusalemu.


Ndipo mliri umene Yehova adzakantha nao mitundu yonse ya anthu imene idathira nkhondo pa Yerusalemu ndi uwu: nyama yao idzaonda akali chilili pa mapazi ao, ndi maso ao adzapuwala m'funkha mwao, ndi lilime lao lidzanyala m'kamwa mwao.


Munthu asapeputse ubwana wako; komatu khala chitsanzo kwa iwo okhulupirira, m'mau, m'mayendedwe, m'chikondi, m'chikhulupiriro, m'kuyera mtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa