Numeri 33:8 - Buku Lopatulika8 Ndipo anachokera ku Pihahiroti, naoloka pakati pa nyanja nalowa m'chipululu; nayenda ulendo wa masiku atatu m'chipululu cha Etamu, namanga mu Mara. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Ndipo anachokera ku Pihahiroti, naoloka pakati pa nyanja nalowa m'chipululu; nayenda ulendo wa masiku atatu m'chipululu cha Etamu, namanga m'Mara. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Adanyamuka ku Pihahiroti naoloka pakatimpakati pa nyanja, ndipo adaloŵa m'chipululu. Tsono adayenda ulendo wa masiku atatu m'chipululu cha Etamu, nakamanga mahema ku Mara. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Atachoka ku Pihahiroti anadutsa mʼkati mwa nyanja kupita ku chipululu ndipo atayenda masiku atatu mʼchipululu cha Etamu, anamanga misasa yawo ku Mara. Onani mutuwo |