Yoswa 3:16 - Buku Lopatulika16 pamenepo madzi ochokera kumagwero anaima, nauka ngati mulu, kutalitu ku Adama, ndiwo mzinda wa ku mbali ya Zaretani; koma madzi akutsikira kunka ku nyanja ya chidikha, ndiyo Nyanja ya Mchere, anadulidwa konse; ndipo anthu anaoloka pandunji pa Yeriko. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 pamenepo madzi ochokera kumagwero anaima, nauka ngati mulu, kutalitu ku Adama, ndiwo mudzi wa ku mbali ya Zaretani; koma madzi akutsikira kunka ku nyanja ya chidikha, ndiyo Nyanja ya Mchere, anadulidwa konse; ndipo anthu anaoloka pandunji pa Yeriko. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa16 madzi onse adaima osayendanso. Madzi akumtunda adaundana ngati khoma lalitali, kuchokera ku Adama mpaka ku mzinda wa Zaretani. Madzi othamangira ku nyanja ya Araba, ndiye kuti Nyanja Yakufa, adatheratu pamalopo, ndipo anthu adaolokera tsidya lina, pafupi ndi Yeriko. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 madzi ochokera ku mtunda anasiya kuyenda. Madzi a Yorodani ochokera ku mtunda anawunjikana pamodzi ngati khoma lalitali pa mtunda wautali ndithu ndi mzinda wa Adama chapafupi ndi mzinda wa Zaretani. Madzi othamangira ku nyanja ya Araba, ngakhalenso amene amachokera kuti Nyanja ya Mchere amathera pamenepo. Choncho anthu anawoloka tsidya lina moyangʼanana ndi Yeriko. Onani mutuwo |
Chifukwa chanji ndinafika osapeza munthu? Ndi kuitana koma panalibe wina woyankha? Kodi dzanja langa lafupika konse, kuti silingathe kuombola? Pena Ine kodi ndilibe mphamvu zakupulumutsa? Taona pa kudzudzula kwanga ndiumitsa nyanja, ndi kusandutsa mitsinje chipululu; nsomba zake zinunkha chifukwa mulibe madzi, ndipo zifa ndi ludzu.