Ndipo mfumu inalamulira anthu onse, kuti, Mchitireni Yehova Mulungu wanu Paska, monga mulembedwa m'buku ili la chipangano.
Eksodo 12:14 - Buku Lopatulika Ndipo tsiku lino lidzakhala kwa inu chikumbutso, muzilisunga la chikondwerero cha Yehova; ku mibadwo yanu muzilisunga la chikondwerero, likhale lemba losatha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo tsiku lino lidzakhala kwa inu chikumbutso, muzilisunga la chikondwerero cha Yehova; ku mibadwo yanu muzilisunga la chikondwerero, likhale lemba losatha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Tsiku limeneli muzidzalisunga. Tsiku limeneli muzidzalikumbukira, ndipo muzidzachita chikondwerero, kupembedza Chauta. Mibadwo yonse izidzakumbukira tsikuli, kuti likhale lamulo lamuyaya, lakuti muzidzachita chikondwerero pa tsiku limenelo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ili ndi tsiku la chikumbutso. Tsiku limeneli muzidzachita chikondwerero, kupembedza Yehova. Mibado yonse imene ikubwera izidzakumbukira tsiku limeneli ngati lamulo lamuyaya ndi kuti pa tsikuli azidzachita chikondwerero cholemekeza Yehova. |
Ndipo mfumu inalamulira anthu onse, kuti, Mchitireni Yehova Mulungu wanu Paska, monga mulembedwa m'buku ili la chipangano.
Dzina lanu, Yehova, likhala kosatha; chikumbukiro chanu, Yehova, kufikira mibadwomibadwo.
Ndipo muzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa; pakuti tsiku lomwe lino ndinatulutsa makamu anu m'dziko la Ejipito; chifukwa chake muzisunga tsiku lino m'mibadwo yanu, lemba losatha.
Ndipo muzisunga chinthu ichi chikhale lemba la kwa inu, ndi kwa ana anu ku nthawi zonse.
Ndipo Yehova anati kwa Mose ndi Aroni, Lemba la Paska ndi ili: mwana wa mlendo aliyense asadyeko;
Ndipo mukhale naye chisungire kufikira tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi womwe; ndipo gulu lonse la Israele lizamuphe madzulo.
Uzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa; masiku asanu ndi awiri uzidya mkate wopanda chotupitsa, monga ndinakuuza, nyengo yoikika, mwezi wa Abibu, pakuti m'menemo unatuluka mu Ejipito; koma asaoneke munthu pamaso panga opanda kanthu;
Aroni ndi ana ake aikonze m'chihema chokomanako, pamaso pa Yehova, kunja kwa nsalu yotchinga yokhala kumboni, kuyambira madzulo kufikira m'mawa; likhale lemba losatha mwa mibadwo yao, alisunge ana a Israele.
Ndipo pambuyo pake Mose ndi Aroni analowa nanena ndi Farao, Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Lola anthu anga apite, kundichitira madyerero m'chipululu.
Uperekenso nsembe yaufa pamodzi naye m'mawa ndi m'mawa, limodzi la magawo asanu ndi limodzi la efa, ndi limodzi la magawo atatu la hini wa mafuta, kusakaniza ndi ufa wosalala, ndiyo nsembe yaufa ya Yehova kosalekeza, mwa lemba losatha.
Ndipo tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi womwewo ndilo chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa a Yehova; masiku asanu ndi awiri muzidya mkate wopanda chotupitsa.
Ndipo akorona adzakhala wa Helidai, ndi wa Tobiya, ndi wa Yedaya, ndi wa Heni mwana wa Zefaniya, akhale chikumbutso mu Kachisi wa Yehova.
Ana aamuna a Aroni, ansembe, ndiwo aziliza malipenga; ndipo akhale kwa inu lemba losatha ku mibadwo yanu.
Kunena za khamu, pakhale lemba limodzi kwa inu, ndi kwa mlendo wakukhala kwanu, ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu; monga mukhala inu, momwemo mlendo pamaso pa Yehova.
chikhale chikumbutso kwa ana a Israele, kuti mlendo, wosati wa mbeu ya Aroni, asasendere kuchita chofukiza pamaso pa Yehova; angakhale monga Kora ndi khamu lake; monga Yehova adanena naye ndi dzanja la Mose.
Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Ndipo taona, Ine ndakupatsa udikiro wa nsembe zanga zokweza, ndizo zopatulika zonse za ana a Israele; chifukwa cha kudzozedwaku ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako aamuna, likhale lemba losatha.
Indetu ndinena kwa inu, kumene kulikonse Uthenga uwu Wabwino udzalalikidwa m'dziko lonse lapansi, ichi chimene mkaziyo anachitachi chidzakambidwanso chikumbukiro chake.
Ndipo m'mene adatenga mkate, nayamika, anaunyema, nawapatsa, nanena, Ichi ndi thupi langa lopatsidwa chifukwa cha inu; chitani ichi chikumbukiro changa.
Samalirani mwezi wa Abibu, kuti muzichitira Yehova Mulungu wanu Paska; popeza m'mwezi wa Abibu Yehova Mulungu wanu anakutulutsani m'dziko la Ejipito usiku.
Ndipo mukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi ana anu aamuna, ndi ana anu aakazi, ndi antchito anu aamuna, ndi antchito anu aakazi, ndi Mlevi wokhala m'mudzi mwanu, ndi mlendo, ndi mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye, okhala pakati pa inu, m'malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake.
Ndipo muziwamanga padzanja panu ngati chizindikiro, ndipo akhale ngati chapamphumi pakati pamaso anu.
Munene nao, Chifukwa madzi a Yordani anadulidwa patsogolo pa likasa la chipangano cha Yehova; muja lidaoloka Yordani, madzi a Yordani anadulidwa; ndipo miyala iyi idzakhala chikumbutso cha ana a Israele chikhalire.
Ndipo kuyambira tsiku lija kufikira lero lomwe anaika ichi, chikhale lemba ndi chiweruzo pa Aisraele.