Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 27:21 - Buku Lopatulika

21 Aroni ndi ana ake aikonze m'chihema chokomanako, pamaso pa Yehova, kunja kwa nsalu yotchinga yokhala kumboni, kuyambira madzulo kufikira m'mawa; likhale lemba losatha mwa mibadwo yao, alisunge ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Aroni ndi ana ake aikonze m'chihema chokomanako, kunja kwa nsalu yotchinga yokhala kumboni, kuyambira madzulo kufikira m'mawa; likhale lemba losatha mwa mibadwo yao, alisunge ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Aroni ndi ana ake aamuna aziyatsa nyale m'chihema chamsonkhanomo amakumana ndi anthu ake, kunja kwa chochinga, patsogolo pa miyala yaumboni ija. Tsono nyalezo ziziyaka kumeneko kuyambira madzulo mpaka m'maŵa. Lamulo limeneli adzalisunge Aisraele ndi zidzukulu zao mpaka muyaya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Mʼchihema cha msonkhano, koma kunja kwa nsalu yotchinga Bokosi la Chipangano, Aaroni ndi ana ake azionetsetsa kuti nyale ikukhala chiyakire pamaso pa Yehova kuyambira madzulo mpaka mmawa. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pakati pa Aisraeli pa mibado yonse.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 27:21
44 Mawu Ofanana  

Ndipo Mulungu anatcha kuyerako Usana, ndi mdimawo anautcha Usiku. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku loyamba.


Ndipo Mulungu analitcha thambolo Kumwamba. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachiwiri.


nafukizira Yehova nsembe zopsereza m'mawa ndi m'mawa, ndi madzulo onse, ndi zonunkhira za fungo lokoma, nakonza mkate woonekera pa gome lopatulika, ndi choikaponyali chagolide ndi nyali zake, ziyake madzulo onse; pakuti tisunga chilangizo cha Yehova Mulungu wathu, koma inu mwamsiya Iye.


Taonani, lemekezani Yehova, atumiki a Yehova inu nonse, akuimirira m'nyumba ya Yehova usiku.


Ndipo tsiku lino lidzakhala kwa inu chikumbutso, muzilisunga la chikondwerero cha Yehova; ku mibadwo yanu muzilisunga la chikondwerero, likhale lemba losatha.


Monga Yehova analamula Mose, momwemo Aroni anauika patsogolo pa Mboni, usungikeko.


Ndipo uziika m'likasamo mboni imene ndidzakupatsa.


Ndipo azivale Aroni ndi ana ake, pakulowa iwo ku chihema chokomanako, kapena poyandikiza iwo kuguwa la nsembe kutumikira m'malo opatulika; anganyamule mphulupulu, nangafe; likhale lemba losatha la iye ndi mbumba zake pambuyo pake.


ndipo zikhale za Aroni ndi za ana ake aamuna, mwa lemba losatha, ziwadzere kwa ana a Israele; popeza ndiyo nsembe yokweza; ndipo ikhale nsembe yokweza yodzera kwa ana a Israele, ya kwa nsembe zamtendere zao, ndiyo nsembe yao yokweza ya Yehova.


Ikhale nsembe yopsereza yosalekeza ya mwa mibadwo yanu, pa khomo la chihema chokomanako, pamaso pa Yehova, kumene ndidzakomana nanu, kulankhula nawe komweko.


Ndipo ndidzapatula chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe; ndidzapatulanso Aroni ndi ana ake aamuna omwe, andichitire ntchito ya nsembe.


asambe manja ao ndi mapazi ao, kuti angafe: liwakhalire lemba losatha, kwa iye ndi kwa mbeu zake, mwa mibadwo yao.


nupere china chisalale, nuchiike chakuno cha mboni m'chihema chokomanako, kumene ndidzakomana ndi iwe; uchiyese chopatulika ndithu.


Ndipo pamene Aroni ayatsa nyalizo madzulo, achifukize chofukiza chosatha pamaso pa Yehova mwa mibadwo yanu.


Ndipo ukaikemo likasa la mboni, nutchinge likasalo ndi nsalu yotchingayo.


Usamamwa vinyo, kapena choledzeretsa, iwe ndi ana ako omwe, m'mene mulowa m'chihema chokomanako, kuti mungafe; likhale lemba losatha mwa mibadwo yanu;


Ndipo ichi chikhale kwa inu lemba losatha, kuchita chotetezera ana a Israele, chifukwa cha zochimwa zao zonse, kamodzi chaka chimodzi. Ndipo anachita monga Yehova adauza Mose.


Ndipo asamapheranso milungu ina nsembe zao, zimene azitsata ndi chigololo. Ili liwakhalire lemba losatha mwa mibadwo yao.


Musamadya mkate, kapena tirigu wokazinga, kapena ngala zaziwisi, kufikira tsiku lomweli, kufikira mutadza nacho chopereka cha Mulungu wanu; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu m'nyumba zanu zonse.


Ndipo mulalikire tsiku lomwelo; kuti mukhale nao msonkhano wopatulika; musamagwira ntchito ya masiku ena; ndilo lemba losatha m'nyumba zanu zonse, mwa mibadwo yanu yonse.


Uza ana a Israele, kuti akutengere mafuta a azitona oyera opera akuunikira, kuti aziwalitsa nyali nthawi zonse.


Aroni aikonze kunja kwa nsalu yotchinga ya mboni, m'chihema chokomanako, kuyambira madzulo kufikira m'mawa, pamaso pa Yehova nthawi zonse; likhale lemba losatha mwa mibadwo yanu.


Ndipo ukhale wa Aroni ndi ana ake, audye pamalo popatulika; pakuti auyese wopatulika kwambiri wochokera ku nsembe zamoto za Yehova; ndilo lemba losatha.


Likhale lemba losatha m'mibadwo yanu m'nyumba zanu zonse, musamadya kapena mafuta kapena mwazi.


naike dzanja lake pamutu pa chopereka chake, naiphe patsogolo pa chihema chokomanako; ndipo ana a Aroni awaze mwazi wake paguwa la nsembe pozungulira.


Ndipo atengeko wodzala manja pa ufa wa chopereka cha ufa wosalala, ndi pa mafuta ake, ndi lubani lonse lili pa chopereka chaufa, nazitenthe paguwa la nsembe, zichite fungo lokoma, ndizo chikumbutso chake cha kwa Yehova.


limene Yehova analamula ana a Israele aziwapatsa, tsiku limene Iye anawadzoza. Likhale lemba losatha mwa mibadwo yao.


Pakuti milomo ya wansembe iyenera kusunga chidziwitso, ndi anthu ayenera kufunafuna chilamulo pakamwa pake; pakuti iye ndiye mthenga wa Yehova wa makamu.


Koma Alevi azichita ntchito ya chihema chokomanako, iwo ndiwo azisenza mphulupulu yao; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu; ndipo asakhale nacho cholowa pakati pa ana a Israele.


Ndipo musunge udikiro wa malo opatulika, ndi udikiro wa guwa la nsembe; kuti pasakhalenso mkwiyo pa ana a Israele.


Ndipo likhale kwa iwo lemba losatha; kuti iye wakuwaza madzi akusiyanitsa azitsuka zovala zake; ndi iye wakukhudza madzi akusiyanitsa adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.


Ndipo izi zikhale kwa inu lemba la chiweruzo mwa mibadwo yanu, m'nyumba zanu zonse.


Ndipo ubwere nao Alevi pakhomo pa chihema chokomanako; nuwasonkhanitse khamu lonse la ana a Israele;


anthu akukhala mumdima adaona kuwala kwakukulu, ndi kwa iwo okhala m'malo a mthunzi wa imfa, kuwala kunatulukira iwo.


Khalani odzimangira m'chuuno, ndipo nyali zanu zikhale zoyaka;


Iyeyo anali nyali yoyaka ndi yowala; ndipo inu munafuna kukondwera m'kuunika kwake kanthawi.


Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kutuluka mumdima, ndiye amene anawala m'mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziwitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Khristu.


Ndipo tili nao mau a chinenero okhazikika koposa; amene muchita bwino powasamalira, monga nyali younikira m'malo a mdima, kufikira kukacha, nikauka nthanda pa mtima yanu;


Kwa mngelo wa Mpingo wa ku Efeso lemba: Izi azinena Iye amene agwira nyenyezi zisanu ndi ziwiri m'dzanja lake lamanja, Iye amene ayenda pakati pa zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide:


ndi nyali ya Mulungu isanazime, Samuele nagona mu Kachisi wa Yehova, m'mene munali likasa la Mulungu.


Ndipo kuyambira tsiku lija kufikira lero lomwe anaika ichi, chikhale lemba ndi chiweruzo pa Aisraele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa