Numeri 15:15 - Buku Lopatulika15 Kunena za khamu, pakhale lemba limodzi kwa inu, ndi kwa mlendo wakukhala kwanu, ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu; monga mukhala inu, momwemo mlendo pamaso pa Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201415 Kunena za khamu, pakhale lemba limodzi kwa inu, ndi kwa mlendo wakukhala kwanu, ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu; monga mukhala inu, momwemo mlendo pamaso pa Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa15 Kunena za msonkhano wonse, pakhale lamulo limodzi lokha kwa inu ndi kwa alendo amene akhale pakati panu, lamulo lamuyaya pa mibadwo yanu yonse. Monga momwe muliri inu, alendonso ali momwemo pamaso pa Chauta. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero15 Gulu lonse likhale ndi malamulo ofanana a inu kapena mlendo wokhala pakati panu. Limeneli ndi lamulo lamuyaya kwa mibado imene ikubwera. Inuyo ndi mlendo mudzakhala wofanana pamaso pa Yehova. Onani mutuwo |
Ndipo Aisraele onse, ndi akulu ao, ndi akapitao ao, ndi oweruza ao anaima chakuno ndi chauko cha likasa, pamaso pa ansembe Alevi, akusenza likasa la chipangano la Yehova, mbadwa ndi alendo omwe; ena a iwo pandunji paphiri la Gerizimu, ndi ena pandunji paphiri la Ebala; monga Mose, mtumiki wa Yehova, adalamulira poyamba paja kuti adalitse anthu a Israele.