Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 4:7 - Buku Lopatulika

7 Munene nao, Chifukwa madzi a Yordani anadulidwa patsogolo pa likasa la chipangano cha Yehova; muja lidaoloka Yordani, madzi a Yordani anadulidwa; ndipo miyala iyi idzakhala chikumbutso cha ana a Israele chikhalire.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Munene nao, Chifukwa madzi a Yordani anadulidwa patsogolo pa likasa la chipangano cha Yehova; muja lidaoloka Yordani, madzi a Yordani anadulidwa; ndipo miyala iyi idzakhala chikumbutso cha ana a Israele chikhalire.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 muzidzaŵauza kuti, ‘Madzi a Yordani adaaima osayendanso, pamene Bokosi lachipangano la Chauta linkaoloka mtsinjewu.’ Miyala imeneyi idzakhala chikumbutso kwa Aisraele.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Muzidzawawuza kuti, ‘Madzi a Yorodani analeka kuyenda pamene Bokosi la Chipangano la Yehova linkawoloka mtsinjewo. Miyala iyi idzakhala chikumbutso kwa anthu a Israeli kwa muyaya.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 4:7
11 Mawu Ofanana  

Anachita chokumbukitsa zodabwitsa zake; Yehova ndiye wachisomo ndi nsoni zokoma.


Ndipo tsiku lino lidzakhala kwa inu chikumbutso, muzilisunga la chikondwerero cha Yehova; ku mibadwo yanu muzilisunga la chikondwerero, likhale lemba losatha.


Ndipo uiike miyala iwiriyo pa zapamapewa za efodi, ikhale miyala ya chikumbutso cha ana a Israele; ndipo Aroni azinyamula maina ao pa mapewa ake awiri, akhale chikumbutso pamaso pa Yehova.


Ndipo uzilandira ndalama za choteteza kwa ana a Israele, ndi kuzipereka pa ntchito ya chihema chokomanako; kuti zikhale chikumbutso cha ana a Israele pamaso pa Yehova, kuchita choteteza cha miyoyo yanu.


Wakupha ng'ombe alingana ndi wakupha munthu; iye wapereka nsembe ya mwanawankhosa alingana ndi wothyola khosi la galu; wothira nsembe yaufa akunga wothira mwazi wa nkhumba; wofukiza lubani akunga wodalitsa fano; inde iwo asankha njira zaozao, ndipo moyo wao ukondwerera m'zonyansa zao;


chikhale chikumbutso kwa ana a Israele, kuti mlendo, wosati wa mbeu ya Aroni, asasendere kuchita chofukiza pamaso pa Yehova; angakhale monga Kora ndi khamu lake; monga Yehova adanena naye ndi dzanja la Mose.


Ndipo kudzali, kuti ndodo ya munthu ndimsankheyo, idzaphuka; ndipo ndidzadziletsera madandaulo a ana a Israele amene adandaula nao pa inu.


ndipo m'mene adayamika, ananyema, nati, Ichi ndi thupi langa la kwa inu; chitani ichi chikhale chikumbukiro changa.


Musamadyera nayo mkate wa chotupitsa; masiku asanu ndi awiri mudyere nayo mkate wopanda chotupitsa, ndiwo mkate wa chizunziko popeza munatuluka m'dziko la Ejipito mofulumira; kuti mukumbukire tsiku lotuluka inu m'dziko la Ejipito masiku onse a moyo wanu.


kuti ichi chikhale chizindikiro pakati pa inu. Akakufunsani ana anu m'tsogolomo, ndi kuti, Miyala iyi nja chiyani ndi inu?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa