Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.
Ahebri 2:3 - Buku Lopatulika tidzapulumuka bwanji ife, tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotero? Chimene Ambuye adayamba kuchilankhula, ndipo iwo adachimva anatilimbikitsira ife; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 tidzapulumuka bwanji ife, tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotero? Chimene Ambuye adayamba kuchilankhula, ndipo iwo adachimva anatilimbikitsira ife; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nanga ife tingapulumuke bwanji tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotere? Ambuye ndiwo amene adalankhula poyamba za chipulumutsochi, kenaka amene adamva mau aowo, adatitsimikizira kuti ndi oona. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nanga ife tidzapulumuka bwanji tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotere? Ambuye ndiye anayamba kuyankhula za chipulumutsochi, kenaka amenenso anamvawo anatitsimikizira. |
Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.
Ndipo wokhala m'mphepete mwa nyanja muno adzati tsiku limenelo, Taonani, kuyembekeza kwathu kuli kotero, kumene ife tinathawira atithangate kupulumutsidwa kwa mfumu ya Asiriya, ndipo ife tidzapulumuka bwanji?
Chilungamo changa chili pafupi, chipulumutso changa chamuka; ndipo mikono yanga idzaweruza anthu; zisumbu zidzandilindira, ndipo adzakhulupirira mkono wanga.
Pakuti njenjete idzawadya ngati chofunda, ndi mbozi zidzawadya ngati ubweya; koma chilungamo changa chidzakhala kunthawi zonse, ndi chipulumutso changa kumibadwo yonse.
Taonani, Yehova walalikira kufikira malekezero a dziko lapansi. Nenani kwa mwana wamkazi wa Ziyoni, Taona chipulumutso chako chifika; taona mphotho yake ali nayo, ndi ntchito yake ili pamaso pake.
Koma anapandukira ndi kutuma mithenga yake ku Ejipito, kuti ampatse akavalo ndi anthu ambiri. Adzapindula kodi? Adzapulumuka wakuchita izi? Athyole pangano ndi kupulumuka kodi?
Pakuti anapepula lumbiro, ndi kuthyola pangano, angakhale anapereka dzanja lake; popeza anachita izi zonse sadzapulumuka.
Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kulalikira, ndi kunena, Tembenukani mitima, pakuti Ufumu wa Kumwamba wayandikira.
Ndipo ataperekedwa Yohane, Yesu anadza ku Galileya, nalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu,
Ndipo anati kwa iwo, Zinthu zanji? Ndipo anati kwa Iye, Izi za Yesu Mnazarene, ndiye munthu mneneri wamphamvu m'ntchito, ndi m'mau, pamaso pa Mulungu ndi anthu onse;
kuyambira ubatizo wa Yohane, kufikira tsiku lija anatengedwa kunka Kumwamba kutisiya ife, mmodzi wa awa akhale mboni ya kuuka kwake pamodzi ndi ife.
Amuna inu Aisraele, mverani mau awa: Yesu Mnazarayo, mwamuna wochokera kwa Mulungu, wosonyezedwa kwa inu ndi zimphamvu, ndi zozizwa, ndi zizindikiro, zimene Mulungu anazichita mwa Iye pakati pa inu monga mudziwa nokha;
Ndipo palibe chipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.
kuti ngati nkutheka ndikachititse nsanje anthu a mtundu wanga, ndi kupulumutsa ena a iwo.
Ndipo uganiza kodi, munthu iwe, amene umaweruza iwo akuchita zotere, ndipo uzichitanso iwe mwini, kuti udzapulumuka pa mlandu wa Mulungu?
Pakuti popeza m'nzeru ya Mulungu dziko lapansi, mwa nzeru yake, silinadziwe Mulungu, chidamkonda Mulungu kupulumutsa okhulupirirawo mwa chopusa cha kulalikira.
Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo chionongeko chobukapo chidzawagwera, monga zowawa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.
Mauwa ali okhulupirika ndi oyenera konse kuti awalandire, kuti Khristu Yesu anadza kudziko lapansi kupulumutsa ochimwa; wa iwowa ine ndine woposa;
Kodi siili yonse mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzalowa chipulumutso?
koma pakutha pake pa masiku ano analankhula ndi ife ndi Mwana amene anamuika wolowa nyumba wa zonse, mwa Iyenso analenga maiko ndi am'mwamba omwe;
Penyani musakane wolankhulayo. Pakuti ngati iwowa sanapulumuke, pomkana Iye amene anawachenjeza padziko, koposatu sitidzapulumuka ife, odzipatulira kwa Iye wa Kumwamba;
Chifukwa chake tiope kuti kapena likatsala lonjezano lakulowa mpumulo wake, wina wa inu angaoneke ngati adaliperewera.
Chifukwa chake tichite changu cha kulowa mpumulowo, kuti wina angagwe m'chitsanzo chomwe cha kusamvera.
ndipo pamene anakonzeka wamphumphu anakhala kwa onse akumvera Iye chifukwa cha chipulumutso chosatha;
kotero Khristunso ataperekedwa nsembe kamodzi kukasenza machimo a ambiri, adzaonekera pa nthawi yachiwiri, wopanda uchimo, kwa iwo amene amlindirira, kufikira chipulumutso.
Chimene chinaliko kuyambira pachiyambi, chimene tidachimva, chimene tidachiona m'maso mwathu, chimene tidachipenyerera, ndipo manja athu adachigwira cha Mau a moyo,
ndipo afuula ndi mau aakulu, nanena, Chipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.