Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 1:22 - Buku Lopatulika

22 kuyambira ubatizo wa Yohane, kufikira tsiku lija anatengedwa kunka Kumwamba kutisiya ife, mmodzi wa awa akhale mboni ya kuuka kwake pamodzi ndi ife.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 kuyambira ubatizo wa Yohane, kufikira tsiku lija anatengedwa kunka Kumwamba kutisiya ife, mmodzi wa awa akhale mboni ya kuuka kwake pamodzi ndi ife.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 kuyambira pamene Iye adabatizidwa ndi Yohane mpaka tsiku limene adatengedwa kuchoka pakati pathu kupita Kumwamba. Mmodzi mwa anthu ameneŵa akhale mboni pamodzi ndi ife, yakuti Yesu adauka kwa akufa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 kuyambira pa nthawi ya ubatizo wa Yohane mpaka nthawi imene Yesu anatengedwa pakati pathu. Pakuti mmodzi wa anthu awa ayenera kukhala mboni pamodzi ndi ife zakuuka kwake.”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 1:22
16 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali masiku omwewo, Yesu anadza kuchokera ku Nazarete wa ku Galileya, nabatizidwa ndi Yohane mu Yordani.


Pamenepo Ambuye Yesu, atatha kulankhula nao, analandiridwa Kumwamba, nakhala padzanja lamanja la Mulungu.


Inu ndinu mboni za izi.


Pamene anthu onse anabatizidwa, Yesu nayenso anabatizidwa. Iye anali kupemphera, ndipo kuthambo kunatseguka,


Ndipo inunso muchita umboni, pakuti muli ndi Ine kuyambira chiyambi.


amenenso anati, Amuna a ku Galileya, muimiranji ndi kuyang'ana kumwamba? Yesu amene walandiridwa kunka Kumwamba kuchokera kwa inu, adzadza momwemo monga munamuona alinkupita Kumwamba.


kufikira tsiku lija anatengedwa kunka Kumwamba, atatha kulamula mwa Mzimu Woyera atumwi amene adawasankha;


Yesu ameneyo, Mulungu anamuukitsa; za ichi tili mboni ife tonse.


Ndipo atumwi anachita umboni ndi mphamvu yaikulu za kuuka kwa Ambuye Yesu; ndipo panali chisomo chachikulu pa iwo onse.


tidzapulumuka bwanji ife, tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotero? Chimene Ambuye adayamba kuchilankhula, ndipo iwo adachimva anatilimbikitsira ife;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa