pamenepo mverani Inu mu Mwamba mokhala Inu, ndi kukhululukira, ndi kuchita, ndi kubwezera munthu yense monga njira zake zonse, amene Inu mumdziwa mtima wake, popeza Inu, Inu nokha, mudziwa mitima ya ana onse a anthu;
1 Samueli 2:3 - Buku Lopatulika Musalankhulenso modzikuza kwambiri motero; m'kamwa mwanu musatuluke zolulutsa; chifukwa Yehova ndi Mulungu wanzeru, ndipo Iye ayesa zochita anthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Musalankhulenso modzikuza kwambiri motero; m'kamwa mwanu musatuluke zolulutsa; chifukwa Yehova ndi Mulungu wanzeru, ndipo Iye ayesa zochita anthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu inu musalankhulenso modzitama, pakamwa panu pasatuluke zodzikuza. Pakuti Chauta ndi Mulungu wanzeru, ndiye amene amaweruza ntchito za anthu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Musandiyankhulenso modzitama, pakamwa panu pasatuluke zonyada, pakuti Yehova ndi Mulungu wanzeru, ndipo ndiye amene amayesa ntchito za anthu onse. |
pamenepo mverani Inu mu Mwamba mokhala Inu, ndi kukhululukira, ndi kuchita, ndi kubwezera munthu yense monga njira zake zonse, amene Inu mumdziwa mtima wake, popeza Inu, Inu nokha, mudziwa mitima ya ana onse a anthu;
Ikhale yosalankhula milomo ya mabodza, imene imalankhula mwachipongwe pa olungama mtima, ndi kudzikuza ndi kunyoza.
Ukanena, Taonani, sitinadziwe chimenechi; kodi woyesa mitima sachizindikira ichi? Ndi wosunga moyo wako kodi sachidziwa? Ndipo kodi sabwezera munthu yense monga mwa machitidwe ake?
Kuopa Yehova ndiko kuda zoipa; kunyada, ndi kudzikuza, ndi njira yoipa, ndi m'kamwa mokhota, ndizida.
Njira ya wolungama ili njira yoongoka; Inu amene muli woongoka, mukonza njira ya wolungama.
Ndani amene, iwe wamtonza ndi kumlalatira? Ndani amene iwe wakwezera mau ako ndi kutukulira maso ako kumwamba? Ndiye Woyera wa Israele.
Ine Yehova ndisanthula mtima, ndiyesa impso, kuti ndimpatse munthu yense monga mwa njira zake, monga zipatso za ntchito zake.
Tsono ine Nebukadinezara ndiyamika, ndi kukuza, ndi kulemekeza Mfumu ya Kumwamba, pakuti ntchito zake zonse nzoona, ndi njira zake chiweruzo; ndi oyenda m'kudzikuza kwao, Iye akhoza kuwachepetsa.
Pakuti mau a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m'mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.
Yehova Chauta Mulungu, Yehova Chauta Mulungu, Iye adziwa, ndi Israele adzadziwa; ngati mopikisana, ngati molakwira Yehova,
Ndipo ndidzaononga ana ake ndi imfa; ndipo idzazindikira Mipingo yonse kuti Ine ndine Iye amene ayesa impso ndi mitima; ndipo ndidzaninkha kwa yense wa inu monga mwa ntchito zanu.
Pamenepo Zebuli anati kwa iye, Pakamwa pako mpoti tsopano, muja udanena, Ndani Abimeleki kuti timtumikire? Awa si anthuwo unawapeputsa? Utuluke tsopano, nulimbane nao.
Koma Yehova ananena ndi Samuele, Usayang'ane nkhope yake, kapena kutalika kwa msinkhu wake, popeza Ine ndinamkana iye; pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang'ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang'ana mumtima.