Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Samueli 2:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 “Musandiyankhulenso modzitama, pakamwa panu pasatuluke zonyada, pakuti Yehova ndi Mulungu wanzeru, ndipo ndiye amene amayesa ntchito za anthu onse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Musalankhulenso modzikuza kwambiri motero; m'kamwa mwanu musatuluke zolulutsa; chifukwa Yehova ndi Mulungu wanzeru, ndipo Iye ayesa zochita anthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Musalankhulenso modzikuza kwambiri motero; m'kamwa mwanu musatuluke zolulutsa; chifukwa Yehova ndi Mulungu wanzeru, ndipo Iye ayesa zochita anthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Anthu inu musalankhulenso modzitama, pakamwa panu pasatuluke zodzikuza. Pakuti Chauta ndi Mulungu wanzeru, ndiye amene amaweruza ntchito za anthu.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 2:3
26 Mawu Ofanana  

pamenepo imvani kumwambako, malo anu wokhalamo. Khululukani ndipo chitanipo kanthu. Muchitire aliyense molingana ndi zonse zimene anachita, popeza inu mumadziwa mtima wake (pakuti ndinu nokha amene mumadziwa mitima ya anthu onse),


Mulungu andiyeze ndi muyeso wake wolungama ndipo Iye adzadziwa kuti ine ndine wosalakwa,


Yehova ndi wamkulu ndi wamphamvu kwambiri; nzeru zake zilibe malire.


Iwo amatseka mitima yawo yopanda chifundo, ndi pakamwa pawo amayankhula modzitamandira.


Milomo yawo yabodzayo ikhale chete, pakuti chifukwa cha kunyada ayankhula modzikuza kutsutsana ndi wolungama.


kodi Mulungu wathu sakanazidziwa zimenezi, pakuti Iye amadziwa zinsinsi zamumtima?


Musatukule nyanga zanu motsutsana ndi kumwamba; musayankhule ndi khosi losololoka.’ ”


Amakhuthula mawu onyada; onse ochita zoyipa ndi odzaza ndi kudzikuza.


Zochita zonse za munthu zimaoneka zabwino pamaso pake, koma Yehova ndiye amasanthula zolinga zako.


Ukanena kuti, “Koma ife sitinadziwe kanthu za izi,” kodi Iye amene amasanthula mtima sazindikira zimenezi? Kodi Iye amene amateteza moyo wako sazidziwa zimenezi? Kodi Iye sadzalipira munthu malingana ndi ntchito zake?


Kuopa Yehova ndiko kudana ndi zoyipa. Ine ndimadana ndi kunyada, kudzitama, kuchita zoyipa, ndiponso kuyankhula zonyenga.


Njira ya munthu wolungama ndi yosalaza, Inu Wolungamayo, mumasalaza njira ya wolungama.


Kodi iwe wanyoza ndi kulalatira ndani? Kodi iwe wafuwulira ndi kumuyangʼana monyada ndani? Watsutsana ndi Woyerayo wa Israeli!


“Ine Yehova ndimafufuza mtima ndi kuyesa maganizo, ndimachitira munthu aliyense molingana ndi makhalidwe ake ndiponso moyenera ntchito zake.”


Mawu anu amene munayankhula monyada kundinyoza Ine ndinawamva.


Tsopano ine Nebukadinezara, ndikutamanda, kukweza ndi kulemekeza Mfumu yakumwamba chifukwa zonse zimene amachita ndi zoyenera ndipo njira zake zonse ndi zachilungamo. Ndipo onse amene amayenda modzikuza adzawatsitsa.


Tekeli: Inu mwayesedwa pa sikelo ndipo mwapezeka kuti mukuperewera.


Yehova akuti, “Mwayankhula mawu owawa onena za Ine. “Komabe inu mukufunsa kuti, ‘Kodi tanena chiyani chotsutsana nanu?’


Paja Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse. Amalowa mpaka molumikizirana moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana fundo ndi mafuta a mʼmafupa. Amaweruza malingaliro ndi zokhumba za mʼmitima.


“Wamphamvu uja, Mulungu ndiye Yehova! Wamphamvu uja Mulungu ndiye Yehova. Iyeyu ndiye akudziwa chifukwa chiyani tinachita zimenezi. Tikufunanso kuti inu mudziwe. Ngati tinachita izi mopandukira ndiponso moonetsa kusakhulupirira Yehova, lero lomwe lino musatisiye ndi moyo.


Ana ake ndidzawakantha ndi kuwapheratu. Kotero mipingo yonse idzadziwa kuti Ine ndine uja amene ndimafufuza mʼmitima mwa anthu ndi mʼmaganizo mwawo. Aliyense wa inu ndidzachita naye monga mwa ntchito zake.


Ndipo Zebuli anamufunsa iye kuti, “Pakamwa pako paja pali kuti tsopano, iwe amene umanena kuti, Abimeleki ndaninso kuti ife timutumikire? Kodi amenewa si anthu aja umawanyozawa? Tsopano tuluka ukamenyane nawo.”


Koma Yehova anati kwa Samueli, “Usaone maonekedwe ake kapena msinkhu wake, pakuti ndamukana iyeyu. Yehova sapenya zimene munthu amapenya. Anthu amapenya zakunja, koma Mulungu amapenya za mu mtima.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa