Pakuti kwa mmodzi kwapatsidwa mwa Mzimu mau a nzeru; koma kwa mnzake mau a chidziwitso, monga mwa Mzimu yemweyo:
Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye.
kuti Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa ulemerero, akupatseni inu mzimu wa nzeru, ndi wa vumbulutso kuti mukamzindikire Iye;
kuti itonthozeke mitima yao, nalumikizike pamodzi iwo m'chikondi, kufikira chuma chonse cha chidzalo cha chidziwitso, kuti akazindikire iwo chinsinsi cha Mulungu, ndiye Khristu,
Ngati munafa pamodzi ndi Khristu kusiyana nazo zoyamba za dziko lapansi, mugonjeranji kuzoikikazo, monga ngati moyo wanu mukhala nao m'dziko lapansi,
usaikapo dzanja, usalawa, usakhudza,
(ndizo zonse zakuonongedwa pochita nazo), monga mwa malangizo ndi maphunziro a anthu?
Zimene zili naotu manenedwe a nzeru m'kutumikira kwa chifuniro cha mwini wake, ndi kudzichepetsa, ndi kusalabadira thupi; koma zilibe mphamvu konse yakuletsa chikhutitso cha thupi.
amene zolemera zonse za nzeru ndi chidziwitso zibisika mwa Iye.
Kumuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru; onse akuchita chotero ali nacho chidziwitso chokoma; chilemekezo chake chikhalitsa kosatha.
Koma nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, yosadzikometsera pamaso.
Pakuti nzeru idzalowa m'mtima mwako, moyo wako udzakondwera ndi kudziwa,
kulingalira kudzakudikira, kuzindikira kudzakutchinjiriza;
Ha! Kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake nzosalondoleka!
Ndipo Mulungu anampatsa Solomoni nzeru ndi luntha lambiri, ndi mtima wodziwa za mitundumitundu, zonga mchenga uli m'mphepete mwa nyanja.
Elihorefe ndi Ahiya ana a Sisa alembi, Yehosafati mwana wa Ahiludi wolembera mbiri,
Ndipo nzeru ya Solomoni inaposa nzeru za anthu onse akum'mawa, ndi nzeru zonse za ku Ejipito.
Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru;
akuchita machawi, popeza masiku ali oipa.
Malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo; mboni za Yehova zili zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru.
ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziwa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.
Kodi kulandira nzeru sikupambana ndi golide, kulandira luntha ndi kusankhika koposa siliva?
Koma tilankhula nzeru mwa angwiro; koma si nzeru ya nthawi yino ya pansi pano, kapena ya akulu a nthawi yino ya pansi pano, amene alinkuthedwa;
koma tilankhula nzeru ya Mulungu m'chinsinsi, yobisikayo, imene Mulungu anaikiratu, pasanakhale nyengo za pansi pano, ku ulemerero wathu,
Ndani ali wanzeru, ndi waluso mwa inu? Aonetsere ndi mayendedwe ake abwino ntchito zake mu nzeru yofatsa.
Koma anyamata amene anai, Mulungu anawapatsa chidziwitso ndi luntha la m'mabuku ali onse, ndi nzeru; koma Daniele anali nalo luntha la m'masomphenya ndi maloto onse.
Malamulo anu andipatsa nzeru yakuposa adani anga; pakuti akhala nane chikhalire.
Ndili nayo nzeru yakuposa aphunzitsi anga onse; pakuti ndilingalira mboni zanu.
Ndipo kudzakhala chilimbiko m'nthawi zako, chipulumutso chambiri, nzeru ndi kudziwa; kuopa kwa Yehova ndiko chuma chake.
Nzeru imangitsa nyumba; luntha liikhazikitsa.
Ndinapita pa munda wa waulesi, polima mphesa munthu wosowa nzeru.
Taonani, ponsepo panamera minga, ndi kuwirirapo khwisa; tchinga lake lamiyala ndi kupasuka.
Pamenepo ndinayang'ana ndi kuganizira, ndinaona ndi kulandira mwambo.
Tulo tapang'ono, kungoodzera pang'ono, kungomanga manja pang'ono m'kugona,
ndipo umphawi wako udzafika ngati mbala; ndi kusauka kwako ngati munthu wachikopa.
Kudziwa kudzaza zipinda zake ndi chuma chonse chofunika cha mtengo wake.
Chifukwa chimenechi yense amene akamva mau anga amenewa, ndi kuwachita, ndidzamfanizira iye ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe;
Nzeru ya wochenjera ndiyo yakuti azindikire njira yake; koma utsiru wa opusa ndiwo chinyengo.
kwa Mulungu wanzeru yekhayo, mwa Yesu Khristu, kwa yemweyo ukhale ulemerero kunthawi zonse. Amen.
koma kwa iwo oitanidwa, ndiwo Ayuda ndi Agriki, Khristu mphamvu ya Mulungu, ndi nzeru ya Mulungu.
Koma kwa munthu anati, Taonani, kuopa Ambuye ndiko nzeru; ndi kupatukana nacho choipa ndiko luntha.
Muyendere munzeru ndi iwo akunja, kuchita machawi nthawi ingatayike.
Mau anu akhale m'chisomo, okoleretsa, kuti mukadziwe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani.
Pakuti Ine ndidzakupatsani inu kamwa ndi nzeru, zimene adani anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.
Koma kwa ife Mulungu anationetsera izi mwa Mzimu; pakuti Mzimu asanthula zonse, zakuya za Mulungu zomwe.
Ichinso chifumira kwa Yehova wa makamu, uphungu wake uzizwitsa ndi nzeru yake impambana.
kuti mu Mpingo azindikiritse tsopano kwa akulu ndi maulamuliro m'zakumwamba nzeru ya mitundumitundu ya Mulungu,
Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang'ana iwe.
Ambuye Yehova wandipatsa Ine lilime la ophunzira, kuti ndidziwe kunena mau akuchirikiza iye amene ali wolema. Iye andigalamutsa m'mawa ndi m'mawa, nagalamutsa khutu langa kuti limve monga ophunzira.
pakuti amasanduliza nthawi ndi nyengo, achotsa mafumu, nalonga mafumu, apatsa anzeru nzeru, ndi chidziwitso kwa iwo okhoza kuzindikira.
Koma nzeru, idzapezeka kuti? Ndi luntha, malo ake ali kuti?
Munthu sadziwa mtengo wake; ndipo silipezeka m'dziko la amoyo.
Mundidziwitse njira zanu, Yehova; Mundiphunzitse mayendedwe anu.
Munditsogolere m'choonadi chanu, ndipo mundiphunzitse; pakuti Inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; Inu ndikuyembekezerani tsiku lonseli.
Anatizindikiritsa ife chinsinsi cha chifuniro chake, monga kunamkomera ndi monga anatsimikiza mtima kale mwa Iye,
amene timlalikira ife, ndi kuchenjeza munthu aliyense ndi kuphunzitsa munthu aliyense mu nzeru zonse, kuti tionetsere munthu aliyense wamphumphu mwa Khristu;
Malangizo a Yehova ali olungama, akukondweretsa mtima; malamulo a Yehova ali oyera, akupenyetsa maso.
Ha! Ndikondadi chilamulo chanu; ndilingiriramo ine tsiku lonse.
Malamulo anu andipatsa nzeru yakuposa adani anga; pakuti akhala nane chikhalire.
Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m'chilungamo:
kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.
Koma kwa Iye muli inu mwa Khristu Yesu, amene anayesedwa kwa ife nzeru ya kwa Mulungu, ndi chilungamo ndi chiyeretso ndi chiombolo;
Tenga nzeru, tenga luntha; usaiwale, usapatuke pa mau a m'kamwa mwanga;
usasiye nzeru, ndipo idzakusunga; uikonde, idzakutchinjiriza.
Ndinati, Amisinkhu anene, ndi a zaka zochuluka alangize nzeru.
Koma m'munthu muli mzimu, ndi mpweya wa Wamphamvuyonse wawazindikiritsa.
ndipo ndamdzaza ndi mzimu wa Mulungu, ndi luso, ndi nzeru, ndi chidziwitso, ndi m'ntchito zilizonse,
Patsani tsono kapolo wanu mtima womvera wakuweruza anthu anu; kuti ndizindikire pakati pa zabwino ndi zoipa; pakuti akutha ndani kuweruza anthu anu ambiri amene?
Mwananga, ukalandira mau anga, ndi kusunga malamulo anga;
Pakuti nzeru idzalowa m'mtima mwako, moyo wako udzakondwera ndi kudziwa,
kulingalira kudzakudikira, kuzindikira kudzakutchinjiriza;
kukupulumutsa kunjira yoipa, kwa anthu onena zokhota;
akusiya mayendedwe olungama, akayende m'njira za mdima;
omwe asangalala pochita zoipa, nakondwera ndi zokhota zoipa;
amene apotoza njira zao, nakhotetsa mayendedwe ao.
Nzeru idzakupulumutsa kwa mkazi wachiwerewere, kwa mkazi wachilendo wosyasyalika ndi mau ake;
wosiya bwenzi la ubwana wake, naiwala chipangano cha Mulungu wake.
Nyumba yake itsikira kuimfa, ndi mayendedwe ake kwa akufa;
onse akunka kwa iye sabweranso, safika kunjira za moyo;
kutcherera makutu ako kunzeru, kulozetsa mtima wako kukuzindikira;
nzeru idzakuyendetsa m'njira ya anthu abwino, kuti usunge mayendedwe a olungama.
Pakuti oongoka mtima adzakhala m'dziko, angwiro nadzatsalamo.
Koma oipa adzalikhidwa m'dziko, achiwembu adzazulidwamo.
ukaitananso luntha, ndi kufuulira kuti ukazindikire;
ukaifunafuna ngati siliva, ndi kuipwaira ngati chuma chobisika;
pompo udzazindikira kuopa Yehova ndi kumdziwadi Mulungu.
Pakuti Yehova apatsa nzeru; kudziwa ndi kuzindikira kutuluka m'kamwa mwake.
pali munthu m'ufumu mwanu mwa iye muli mzimu wa milungu yoyera; ndipo masiku a atate wanu munapezeka mwa iye kuunika, ndi luntha, ndi nzeru, ngati nzeru ya milungu; ndipo mfumu Nebukadinezara atate wanu, inde mfumu atate wanu anamuika akhale mkulu wa alembi, openda, Ababiloni, ndi alauli;
popeza m'Daniele yemweyo, amene mfumu adamutcha Belitesazara, mudapezeka mzimu wopambana, ndi chidziwitso, ndi luntha, kumasulira maloto ndi kutanthauzira mau ophiphiritsa ndi kumasula mfundo. Amuitane Daniele tsono, iye adzafotokozera kumasuliraku.
Ndipo mwanayo anakula nalimbika, nalikudzala ndi nzeru; ndi chisomo cha Mulungu chinali pa Iye.
chimene anatichulukitsira ife m'nzeru zonse, ndi chisamaliro.
Anatizindikiritsa ife chinsinsi cha chifuniro chake, monga kunamkomera ndi monga anatsimikiza mtima kale mwa Iye,
Atero Yehova, wanzeru asadzitamandire m'nzeru zake, wamphamvu asadzitamandire m'mphamvu yake, wachuma asadzitamandire m'chuma chake;
koma wakudzitamandira adzitamandire adzikweze umo, kuti ali wakuzindikira, ndi kundidziwa Ine, kuti ndine Yehova wakuchita zokoma mtima, chiweruziro, ndi chilungamo m'dziko lapansi, pakuti m'menemo ndikondwerera, ati Yehova.
Chifukwa chake, abale, yang'anani mwa inu amuna asanu ndi awiri a mbiri yabwino, odzala ndi Mzimu ndi nzeru, amene tikawaike asunge ntchito iyi.
Koma sitinalandira ife mzimu wa dziko lapansi, koma Mzimu wa kwa Mulungu, kuti tikadziwe zimene zipatsidwa kwa ife ndi Mulungu kwaufulu.
Zimenenso tilankhula, si ndi mau ophunzitsidwa ndi nzeru za munthu, koma ophunzitsidwa ndi Mzimu; ndi kulinganiza zamzimu ndi zamzimu.
Kodi iwe sunadziwe? Kodi sunamve? Mulungu wachikhalire, Yehova, Mlengi wa malekezero a dziko lapansi, salefuka konse, salema; nzeru zake sizisanthulika.
Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalmo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu.
Mwa ichinso nzeru ya Mulungu inati, Ndidzatumiza kwa iwo aneneri ndi atumwi; ndipo ena a iwo adzawapha, nadzawazunza;
Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.
Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako;
umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.
Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.
Mundizindikiritse, ndipo ndidzasunga malamulo anu; ndidzawasamalira ndi mtima wanga wonse.
Pita kunyerere, waulesi iwe, penya njira zao nuchenjere;
zilibe mfumu, ngakhale kapitao, ngakhale mkulu;
koma zitengeratu zakudya zao m'malimwe; nizituta dzinthu zao m'masika.
Kuopa Yehova kuli mbee, kwakukhalabe nthawi zonse; maweruzo a Yehova ali oona, alungama konsekonse.
Koma atadza Iyeyo, Mzimu wa choonadi, adzatsogolera inu m'choonadi chonse; pakuti sadzalankhula za Iye mwini; koma zinthu zilizonse adzazimva, adzazilankhula; ndipo zinthu zilinkudza adzakulalikirani.
Chiwerengero cha mau anu ndicho choonadi; ndi maweruzo anu olungama onse akhala kosatha.