Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


48 Mau a m'Baibulo Okhudza Anthu Ogwidwa ndi Ziwanda

48 Mau a m'Baibulo Okhudza Anthu Ogwidwa ndi Ziwanda

Mizimu yoipa ndi yamphamvu kwambiri ndipo imafuna kuti tichite zinthu zoyipa. Mizimu iyi siyingachite chilichonse popanda thupi la munthu, choncho imafuna kukhala mwa ife. Koma sangakukakamize; uyenera kuwalola kuti alowe mwa iwe. Amagwiritsa ntchito zomwe umawona, zomwe umamva, ndi zomwe umagwira kuti alowe m'moyo mwako.

Satana safuna zabwino zako. Mizimu yoipa imapangitsa anthu ochita zoyipa kukhala ndi moyo wodetsa. Baibulo limanena za anthu omwe anali ndi mizimu yoipa, ndipo izi zinawabweretsera mavuto ambiri m'thupi lawo. Yuda ndi chitsanzo chabwino cha munthu amene anapatutsidwa ndi kulola kuti choipa chimulamule.

Mulungu analola kuti Mfumu Sauli, atamuchimwira, azunzidwe ndi mzimu woyipa. Izi zinamupangitsa kukhala wachisoni nthawi zonse ndiponso kufuna kupha Davide (1 Samueli 18:10-11).

Nkhani yabwino ndi yakuti Yesu Khristu satisiya, ngakhale titakhala bwanji kapena ngakhale anthu ena atatisiya. Njira yokha yopezera ufulu weniweni ndiyo kuyandikira Yesu. Pamene Yesu ali m'moyo mwathu, ndiye kuti tili omasuka kotheratu. Choncho, samalira mtima wako ndipo pemphera kwa Yesu kuti alamulire moyo wako, kuti Mdyerekezi asapeze malo mwa iwe.




Mateyu 12:28-30

Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu yake ya Mzimu wa Mulungu, pomwepo Ufumu wa Mulungu unafika pa inu. Kapena akhoza bwanji munthu kulowa m'banja la munthu wolimba, ndi kufunkha akatundu ake, ngati iye sayamba kumanga munthu wolimbayo? Ndipo pamenepo adzafunkha za m'banja lake. Koma Iye anati kwa iwo, Kodi simunawerenga chimene anachichita Davide, pamene anali ndi njala, ndi iwo amene anali naye? Iye wosakhala pamodzi ndi Ine akana Ine, ndi iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwazamwaza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 7:26

Koma mkaziyo anali Mgriki, mtundu wake Msiro-Fenisiya. Ndipo anampempha Iye kuti atulutse chiwanda m'mwana wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 1:32

Ndipo madzulo, litalowa dzuwa, anadza nao kwa Iye onse akudwala, ndi akugwidwa ndi ziwanda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:12

Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 2:19

Ukhulupirira iwe kuti Mulungu ali mmodzi; uchita bwino; ziwanda zikhulupiriranso, ndipo zinthunthumira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 4:1

Koma Mzimu anena monenetsa, kuti m'masiku otsiriza ena adzataya chikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosocheretsa ndi maphunziro a ziwanda,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 3:11

Ndipo mizimu yonyansa, m'mene inamuona Iye, inamgwadira, nifuula, niti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 17:18

Ndipo Yesu anamdzudzula; ndipo chiwanda chinatuluka mwa iye; ndipo mnyamatayo anachira kuyambira nthawi yomweyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 8:7

Pakuti ambiri a iwo akukhala nayo mizimu yonyansa inawatulukira, yofuula ndi mau akulu; ndipo ambiri amanjenje, ndi opunduka, anachiritsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 5:1-20

Ndipo anafika tsidya lina la nyanja, kudziko la Agerasa. Ndipo anampempha Iye kwambiri kuti asaitulutsire kunja kwake kwa dziko. Ndipo panali pamenepo gulu lalikulu la nkhumba zilinkudya kuphiri. Ndipo inampempha Iye, kuti, Titumizeni ife mu nkhumbazo, kuti tilowe mu izo. Ndipo anailola. Ndipo mizimu yonyansa inatuluka, nilowa mu nkhumba; ndipo gulu linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m'nyanja, ndizo ngati zikwi ziwiri; ndipo zinatsamwa m'nyanja. Ndipo akuziweta anathawa, nauza m'mudzi, ndi kuminda. Ndipo anadza kudzaona chochitikacho. Ndipo anadza kwa Yesu, napenya wogwidwa ziwandayo alikukhala pansi, wovala ndi wa nzeru zake zabwino, ndiye amene anali ndi legio; ndipo anaopa iwo. Ndipo adapenyawo adawafotokozera umo anachitira ndi wogwidwa ziwandayo, ndi za nkhumbazo. Ndipo anayamba kumpempha Iye kuti achoke m'malire ao. Ndipo m'mene Iye analikulowa mungalawa, anampempha waziwanda uja kuti akhale ndi Iye. Ndipo sanamlole, koma ananena naye, Muka kwanu kwa abale ako, nuwauze zinthu zazikulu anakuchitira Ambuye, ndi kuti anakuchitira chifundo. Ndipo pamene adatuluka mungalawa, pomwepo anakomana naye munthu wotuluka kumanda wa mzimu wonyansa, Ndipo anamuka nayamba kulalikira ku Dekapoli zinthu zazikulu Yesu adamchitira iye; ndipo anthu onse anazizwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:17

Ndipo makumi asanu ndi awiri aja anabwera mokondwera, nanena, Ambuye, zingakhale ziwanda zinatigonjera ife m'dzina lanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:22

Ndipo onani, mkazi wa ku Kanani anatuluka m'malire, nafuula, nati, Mundichitire ine chifundo Ambuye, mwana wa Davide; mwana wanga wamkazi wagwidwa koopsa ndi chiwanda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 9:17-18

Ndipo wina wa m'khamulo anamyankha Iye, kuti, Mphunzitsi, ndadza naye kwa Inu mwana wanga, ali nao mzimu wosalankhula; ndipo ponse pamene umgwira, umgwetsa; ndipo achita thovu, nakukuta mano, nanyololoka; ndipo ndinalankhula nao ophunzira anu kuti autulutse; koma sanakhoze.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 5:16

Komanso unasonkhana pamodzi unyinji wa anthu ochokera kumidzi yozungulira Yerusalemu, alikutenga odwala, ndi ovutika ndi mizimu yonyansa; ndipo anachiritsidwa onsewa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 8:28-34

Ndipo pofika Iye kutsidya lina, kudziko la Agadara, anakomana naye awiri ogwidwa ndi ziwanda, akutuluka kumanda, aukali ndithu, kotero kuti sangathe kupitapo munthu pa njira imeneyo. Ndipo onani, anafuula nati, Tili nanu chiyani, Inu Mwana wa Mulungu? Mwadza kuno kodi kutizunza ife, nthawi yake siinafike? Ndipo Yesu anatambalitsa dzanja lake, namkhudza iye, nati, Ndifuna; takonzedwa. Ndipo pomwepo khate lake linachoka. Ndipo panali patali ndi iwo gulu la nkhumba zambiri zilinkudya. Ndipo mizimuyo inampempha Iye ninena, Ngati mutitulutsa, mutitumize ife tilowe m'gulu la nkhumbazo. Ndipo anati kwa iyo, Mukani. Ndipo inatuluka, nimuka, kukalowa m'nkhumbazo; ndipo onani, gulu lonse linathamangira kunsi kuphompho m'nyanjamo, ndipo linafa m'madzi. Koma akuziweta anathawa, namuka kumidzi, nauza zonse, ndi zakuti zao za aziwanda aja. Ndipo onani, mudzi wonse unatulukira kukakumana naye Yesu, ndipo m'mene anamuona Iye, anampempha kuti achoke m'malire ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 5:18

Ndipo m'mene Iye analikulowa mungalawa, anampempha waziwanda uja kuti akhale ndi Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 8:26-39

Ndipo iwo anakocheza kudooko ku dziko la Agerasa, ndilo lopenyana ndi Galileya. Ndipo atatuluka pamtunda Iye, anakomana naye mwamuna wa kumudzi, amene anali nazo ziwanda; ndipo masiku ambiri sanavale chovala, nisanakhala m'nyumba, koma m'manda. Ndipo pakuona Yesu, iye anafuula, nagwa pansi pamaso pake, nati ndi mau akulu, Ndili nacho chiyani ndi Inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkulukulu? Ndikupemphani Inu musandizunze. Pakuti Iye adalamula mzimu wonyansa utuluke mwa munthuyo. Pakuti nthawi zambiri unamgwira; ndipo anthu anammanga ndi maunyolo ndi matangadza kumsungira; ndipo anamwetula zomangirazo, nathawitsidwa ndi chiwandacho kumapululu. ndi Yohana, mkazi wake wa Kuza kapitao wa Herode, ndi Suzana, ndi ena ambiri, amene anawatumikira ndi chuma chao. Ndipo Yesu anamfunsa iye, kuti, Dzina lako ndiwe yani? Ndipo anati, Legio, chifukwa ziwanda zambiri zidalowa mwa iye. Ndipo zinampempha Iye, kuti asazilamulire zichoke kulowa ku chiphompho chakuya. Ndipo panali pamenepo gulu la nkhumba zambiri zilinkudya m'phiri. Ndipo zinampempha Iye kuti azilole zilowe mu izo. Ndipo anazilola. Ndipo ziwandazo zinatuluka mwa munthu nizilowa mu nkhumba: ndipo gululo linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m'nyanjamo, nilitsamwa. Ndipo akuwetawo m'mene anaona chimene chinachitika, anathawa, nauza akumudzi ndi kumilaga yake. Ndipo iwo anatuluka kukaona chimene chinachitika; ndipo anadza kwa Yesu, nampeza munthuyo, amene ziwanda zinatuluka mwa iye, alikukhala pansi kumapazi ake a Yesu wovala ndi wa nzeru zake; ndipo iwo anaopa. Ndipo amene anaona anawauza iwo machiritsidwe ake a wogwidwa chiwandayo. Ndipo anthu aunyinji onse a dziko la Agerasa loyandikira anamfunsa Iye achoke kwa iwo; chifukwa anagwidwa ndi mantha akulu. Ndipo Iye analowa m'ngalawa, nabwerera. Ndipo munthuyo amene ziwanda zinatuluka mwa iye anampempha Iye akhale ndi Iye; koma anamuuza apite, nanena, Pita kunyumba kwako, nufotokozere zazikuluzo anakuchitira iwe Mulungu. Ndipo iye anachoka, nalalikira kumudzi wonse zazikuluzo Yesu anamchitira iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 5:2

Ndipo pamene adatuluka mungalawa, pomwepo anakomana naye munthu wotuluka kumanda wa mzimu wonyansa,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 1:32-34

Ndipo madzulo, litalowa dzuwa, anadza nao kwa Iye onse akudwala, ndi akugwidwa ndi ziwanda. Ndipo mudzi wonse unasonkhana pakhomo. Ndipo anachiritsa anthu ambiri akudwala nthenda za mitundumitundu, natulutsa ziwanda zambiri; ndipo sanalole ziwandazo zilankhule, chifukwa zinamdziwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 11:24

Pamene paliponse mzimu wonyansa ukatuluka mwa munthu, upyola malo opanda madzi nufunafuna mpumulo; ndipo posaupeza unena, Ndidzabwera kunyumba kwanga kumene ndinatulukako;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 4:33-36

Ndipo munali m'sunagoge munthu, wokhala nacho chiwanda chonyansa; nafuula ndi mau olimba, kuti, Ha! Tili ndi chiyani ndi Inu, Yesu wa ku Nazarete? Kodi munadza kutiononga ife? Ndikudziwani Inu muli yani, ndinu Woyera wake wa Mulungu. Ndipo Yesu anamdzudzula iye, nanena, Tonthola, nutuluke mwa iye. Ndipo chiwandacho m'mene chinamgwetsa iye pakati, chinatuluka mwa iye chosamphweteka konse. Ndipo anthu onse anadabwa, nalankhulana wina ndi mnzake, nanena, Mau amenewa ali otani? Chifukwa ndi ulamuliro ndi mphamvu angolamulira mizimu yonyansa, ndipo ingotuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 8:28

Ndipo pofika Iye kutsidya lina, kudziko la Agadara, anakomana naye awiri ogwidwa ndi ziwanda, akutuluka kumanda, aukali ndithu, kotero kuti sangathe kupitapo munthu pa njira imeneyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 1:23-26

Ndipo pomwepo panali munthu m'sunagoge mwao ali ndi mzimu wonyansa; ndipo anafuula iye. Kuti, Tili ndi chiyani ife ndi Inu Yesu wa ku Nazarete? Kodi mwadza kudzationonga ife: Ndikudziwani, ndinu Woyerayo wa Mulungu. Ndipo Yesu anaudzudzula, kuti, Khala uli chete, nutuluke mwa iye. Ndipo mzimu wonyansa, pomng'amba, ndi kufuula ndi mau akulu, unatuluka mwa iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 13:11

Ndipo mkazi anali nao mzimu wakumdwalitsa zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu; nakhala wopeteka, ndimo analibe mphamvu konse yakuweramuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 9:25

Ndipo pamene Yesu anaona kuti khamu la anthu lilikuthamangira pamodzi, anadzudzula mzimu woipawo, nanena ndi uwo, Mzimu wosalankhula ndi wogontha iwe, Ine ndikulamula iwe, tuluka mwa iye, ndipo usalowenso mwa iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 11:14-15

Ndipo analikutulutsa chiwanda chosalankhula. Ndipo kunali, chitatuluka chiwanda, wosalankhulayo analankhula; ndipo makamu a anthu anazizwa. Koma ena mwa iwo anati, Ndi Belezebulu mkulu wa ziwanda amatulutsa ziwanda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 9:37-43

Ndipo panali, m'mawa mwake, atatsika m'phiri, khamu lalikulu la anthu linakomana naye. Ndipo onani, anafuula munthu wa m'khamulo, nanena, nati, Mphunzitsi, ndikupemphani, yang'anirani mwana wanga; chifukwa ndiye mmodzi yekha wa ine: ndipo onani, umamgwira iye mzimu, nafuula modzidzimuka; ndipo umamng'amba iye ndi kumchititsa thovu pakamwa, nuchoka pa iye mwa unyenzi, numgola iye. Ndipo m'nyumba iliyonse mukalowemo, khalani komweko, ndipo muzikachokera kumeneko. Ndipo ndinapempha ophunzira anu kuti autulutse; koma sanathe. Ndipo Yesu anayankha, nati, Ha! Obadwa inu osakhulupirira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji, ndi kulekerera inu? Idza naye kuno mwana wako. Ndipo akadadza iye, chiwandacho chinamgwetsa, ndi kumng'ambitsa. Koma Yesu anadzudzula mzimu wonyansawo, nachiritsa mnyamata, nambwezera iye kwa atate wake. Ndipo onse anadabwa pa ukulu wake wa Mulungu. Koma pamene onse analikuzizwa ndi zonse anazichita, Iye anati kwa ophunzira ake,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:22

Pomwepo anabwera naye kwa Iye munthu wogwidwa ndi chiwanda, wakhungu ndi wosalankhula; ndipo Iye anamchiritsa, kotero kuti wosalankhulayo analankhula, napenya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 16:16-18

Ndipo panali, pamene tinali kunka kukapemphera, anakomana ndi ife mdzakazi wina amene anali ndi mzimu wambwebwe, amene anapindulira ambuye ake zambiri pakubwebweta pake. Ameneyo anatsata Paulo ndi ife, nafuula, kuti, Anthu awa ndi akapolo a Mulungu wa Kumwambamwamba, amene akulalikirani inu njira ya chipulumutso. Ndipo anachita chotero masiku ambiri. Koma Paulo anavutika mtima ndithu, nacheuka, nati kwa mzimuwo, Ndikulamulira iwe m'dzina la Yesu Khristu, tuluka mwa iye. Ndipo unatuluka nthawi yomweyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:1

Ndipo pamene Iye anadziitanira ophunzira ake khumi ndi awiri, anapatsa iwo mphamvu pa mizimu yoipa, yakuitulutsa, ndi yakuchiza nthenda iliyonse ndi zofooka zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 9:17-27

Ndipo wina wa m'khamulo anamyankha Iye, kuti, Mphunzitsi, ndadza naye kwa Inu mwana wanga, ali nao mzimu wosalankhula; ndipo ponse pamene umgwira, umgwetsa; ndipo achita thovu, nakukuta mano, nanyololoka; ndipo ndinalankhula nao ophunzira anu kuti autulutse; koma sanakhoze. Ndipo Iye anawayankha nanena, Mbadwo wosakhulupirira inu, ndidzakhala ndi inu kufikira liti? Ndidzakulekererani nthawi yanji? Mudze naye kwa Ine. Ndipo atapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu anatenga Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, nakwera nao pa phiri lalitali padera pa okha; ndipo anasandulika pamaso pao: Ndipo anadza naye kwa Iye; ndipo pakumuona, pomwepo mzimuwo unamng'amba koopsa; ndipo anagwa pansi navimvinika ndi kuchita thovu. Ndipo Iye anafunsa atate wake, kuti, Chimenechi chinayamba kumgwira liti? Ndipo anati, Chidamyamba akali mwana. Ndipo kawirikawiri ukamtaya kumoto ndi kumadzi, kumuononga; koma ngati mukhoza kuchita kanthu mtithandize, ndi kutichitira chifundo. Ndipo Yesu ananena naye, Ngati mukhoza! Zinthu zonse zitheka ndi iye wakukhulupirira. Pomwepo atate wa mwana anafuula, nanena, Ndikhulupirira; thandizani kusakhulupirira kwanga. Ndipo pamene Yesu anaona kuti khamu la anthu lilikuthamangira pamodzi, anadzudzula mzimu woipawo, nanena ndi uwo, Mzimu wosalankhula ndi wogontha iwe, Ine ndikulamula iwe, tuluka mwa iye, ndipo usalowenso mwa iye. Ndipo pamene unafuula, numng'ambitsa, unatuluka; ndipo mwana anakhala ngati wakufa; kotero kuti ambiri ananena, Wamwalira. Koma Yesu anamgwira dzanja lake, namnyamutsa; ndipo anaimirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 7:25-30

Koma pomwepo mkazi, kabuthu kake kanali ndi mzimu wonyansa, pamene anamva za Iye, anadza, nagwa pa mapazi ake. Koma mkaziyo anali Mgriki, mtundu wake Msiro-Fenisiya. Ndipo anampempha Iye kuti atulutse chiwanda m'mwana wake. Ndipo ananena naye, Baleka, athange akhuta ana; pakuti si kwabwino kuti titenge mkate wa ana, ndi kuutayira tiagalu. Koma iye anavomera nanena ndi Iye, Ine Ambuye; tingakhale tiagalu ta pansi pa gome tikudyako nyenyeswa za ana. Ndipo anati kwa iye, Chifukwa cha mau amene, muka; chiwanda chatuluka m'mwana wako wamkazi. Pakuti Afarisi, ndi Ayuda onse sakudya osasamba m'manja ao, kuti asungire mwambo wa akulu; Ndipo anachoka kunka kunyumba kwake, napeza mwana atamgoneka pakama, ndi chiwanda chitatuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 9:32-33

Ndipo pamene iwo analikutuluka, onani, anabwera naye kwa Iye munthu wosalankhula, wogwidwa ndi chiwanda. Ndipo m'mene chinatulutsidwa chiwandacho, wosalankhulayo analankhula, ndipo makamu a anthu anazizwa, nanena, Kale lonse sichinaoneke chomwecho mwa Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 8:16

Ndipo pakudza madzulo, anabwera nao kwa Iye anthu ambiri ogwidwa ndi ziwanda; ndipo Iye anatulutsa mizimuyo ndi mau, nachiritsa akudwala onse;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 17:14-18

Ndipo pamene iwo anadza kukhamu la anthu, kunafika kwa Iye munthu, namgwadira Iye, nati, Ambuye, chitirani mwana wanga chifundo; chifukwa adwala nkhunyu, kuzunzika koipa: pakuti amagwa kawirikawiri pamoto, ndi kawirikawiri m'madzi. Ndipo ndinadza naye kwa ophunzira anu, koma iwo sanathe kumchiritsa. Ndipo Yesu anayankha nati, Ha, obadwa osakhulupirira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji? Ndidzalekerera inu nthawi yanji? Mudze naye kwa Ine kuno. Ndipo Yesu anamdzudzula; ndipo chiwanda chinatuluka mwa iye; ndipo mnyamatayo anachira kuyambira nthawi yomweyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 16:16

Ndipo panali, pamene tinali kunka kukapemphera, anakomana ndi ife mdzakazi wina amene anali ndi mzimu wambwebwe, amene anapindulira ambuye ake zambiri pakubwebweta pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 8:2

ndi akazi ena amene anachiritsidwa ziwanda ndi nthenda zao, ndiwo, Maria wonenedwa Magadala, amene ziwanda zisanu ndi ziwiri zinatuluka mwa iye,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 19:16

Ndipo munthu, mwa iye amene munali mzimu woipa, anawalumphira nawaposa, nawalaka onse awiriwo, kotero kuti anathawa m'nyumba amaliseche ndi olasidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:8

Chiritsani akudwala, ukitsani akufa, konzani akhate, tulutsani ziwanda: munalandira kwaulere, patsani kwaulere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 3:11-12

Ndipo mizimu yonyansa, m'mene inamuona Iye, inamgwadira, nifuula, niti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu. Ndipo anailimbitsira mau kuti isamuulule Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:17-20

Ndipo makumi asanu ndi awiri aja anabwera mokondwera, nanena, Ambuye, zingakhale ziwanda zinatigonjera ife m'dzina lanu. Ndipo anati kwa iwo, Ndinaona Satana alinkugwa ngati mphezi wochokera kumwamba. Taonani, ndakupatsani ulamuliro wakuponda pa njoka ndi zinkhanira, ndi pa mphamvu iliyonse ya mdaniyo; ndipo kulibe kanthu kadzakuipsani konse. Ndipo ananena kwa iwo, Dzinthu dzichuluka, koma antchito achepa; potero pemphani Mwini dzinthu, kuti akankhe antchito kukututa kwake. Koma musakondwera nako kuti mizimu idakugonjerani, koma kondwerani kuti maina anu alembedwa m'Mwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 9:25-27

Ndipo pamene Yesu anaona kuti khamu la anthu lilikuthamangira pamodzi, anadzudzula mzimu woipawo, nanena ndi uwo, Mzimu wosalankhula ndi wogontha iwe, Ine ndikulamula iwe, tuluka mwa iye, ndipo usalowenso mwa iye. Ndipo pamene unafuula, numng'ambitsa, unatuluka; ndipo mwana anakhala ngati wakufa; kotero kuti ambiri ananena, Wamwalira. Koma Yesu anamgwira dzanja lake, namnyamutsa; ndipo anaimirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 5:15

Ndipo anadza kwa Yesu, napenya wogwidwa ziwandayo alikukhala pansi, wovala ndi wa nzeru zake zabwino, ndiye amene anali ndi legio; ndipo anaopa iwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:4

Inu ndinu ochokera mwa Mulungu, tiana, ndipo munailaka; pakuti Iye wakukhala mwa inu aposa iye wakukhala m'dziko lapansi. Iwo ndiwo ochokera m'dziko lapansi;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:1

Khristu anatisandutsa mfulu, kuti tikhale mfulu; chifukwa chake chilimikani, musakodwenso ndi goli la ukapolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 16:20

Ndipo Mulungu wa mtendere adzaphwanya Satana pansi pa mapazi anu tsopano lino. Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:7

Potero mverani Mulungu; koma kanizani mdierekezi, ndipo adzakuthawani inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:13

amene anatilanditsa ife kuulamuliro wa mdima, natisunthitsa kutilowetsa m'ufumu wa Mwana wa chikondi chake;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse, ulemerero ndi ulemu zikhale zako! Mulungu wanga wakumwamba ndimabwera kwa Inu kudzera mwa Ambuye wanga Yesu Khristu. Atate Woyera, ndikupemphani podziwa kuti Inu nokha muli ndi Mphamvu yomasula ndipo ndikutenga ulamuliro umene mwandipatsa kudzera mwa Mzimu Woyera wanu kuti ndigwetse maganizo onse abodza ndi chinyengo omwe abwera pa moyo wanga. Pakadali pano ndikudzudzula mzimu uliwonse woyipa ndi ntchito iliyonse yoipa ndikuzilengeza kuti sizigwira ntchito. Mawu anu amati: "Koma ngati ine nditulutsa ziwanda ndi Mzimu wa Mulungu, ndiye kuti Ufumu wa Mulungu wafika kwa inu. Iye amene sali nane ali kunditsutsa; ndipo iye amene sasuntha nane amabalalitsa." Ndikukupemphani kuti mulimbitse chikhulupiriro changa ndipo mundithandize kugonjetsa mantha, chisokonezo chilichonse, kuti kuyuma tsopano Mzimu Woyera utenge ulamuliro wa maganizo anga, malingaliro anga ndi umunthu wanga wonse. Lero ndikusiya uchimo ndi zonyansa zonse ndipo ndikudzilongeza kuti ndine womasuka ku ukapolo uliwonse wa mdani. Ambuye, ndikupemphani kuti mumasule ndi kubwezeretsa miyoyo ya anthu omwe pakadali pano akukumana ndi zovuta, kaya ndi matenda, zachuma kapena m'banja. Ndimawalengeza kuti ali omasuka ku zowawa zonse, chifukwa kumene kuli Mzimu wanu wa Ambuye, kuli ufulu. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa