Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

155 Mau a m'Baibulo Okhudza Nkhondo

Ndi nthawi ya nkhondo ndi mavuto, n’zosavuta kugwidwa ndi mantha komanso kusadziwa choti chingachitike. Koma Baibulo limatipatsa chiyembekezo ndi mphamvu. Pakati pa chisokonezo ndi kutaya mtima, tingapeze chitonthozo mu lonjezo la Mulungu loti adzakhala nafe, ngakhale m’nthawi zovuta kwambiri. Monga mmene lemba la Masalmo 46:1-2 limanenera, “Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezeka msanga m’masautso. Chifukwa chake sitidzachita mantha, ngakhale dziko litasunthika, ndipo mapiri atagwera mkati mwa nyanja.”

Yesu, m’buku la Yohane 16:33, anatiuza, “Ndanena izi kwa inu kuti mukhale ndi mtendere mwa Ine. M’dziko lapansi mudzakhala ndi chisautso; koma limbikani mtima; Ine ndaligonjetsa dziko lapansi.”

Ndi nthawi ya nkhondo ndi mavuto, tikumbukire kuti zida zathu zenizeni si za thupi, koma zauzimu. Pemphero, chikhulupiriro, ndi chiyembekezo ndi zida zathu zamphamvu kwambiri. Tikamaika maganizo ndi mitima yathu pa Mulungu, tingathe kuthana ndi mavuto aliwonse molimba mtima komanso modzidalira.

Mulungu akutiitana kuti tikhale kuunika pakati pa mdima, kuti tikhale ofalitsa chiyembekezo ndi chikondi m’nthawi yovuta ino. Mwa zochita zathu ndi mawu athu, tingasonyeze chikondi ndi mtendere wa Khristu, kupereka chitonthozo ndi chithandizo kwa omwe akutizungulira.

M’nthawi yovuta ino, tidalira Mulungu, tigwire mwamphamvu lonjezo lake la chipulumutso, ndipo tilole chikondi chake chitsogolere miyoyo yathu.


Yakobo 4:1-2

Zichokera kuti nkhondo, zichokera kuti zolimbana mwa inu? Kodi sizichokera kuzikhumbitso zanu zochita nkhondo m'ziwalo zanu?

Dzichepetseni pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani.

Musamanenerana, abale. Wonenera mbale, kapena woweruza mbale wake, anenera lamulo, naweruza lamulo: koma ngati uweruza lamulo, suli wochita lamulo, komatu woweruza.

Woika lamulo ndi woweruza ndiye mmodzi, ndiye amene akhoza kupulumutsa ndi kuononga; koma iwe woweruza mnzako ndiwe yani?

Nanga tsono, inu akunena, Lero kapena mawa tidzapita kulowa kumudzi wakutiwakuti, ndipo tidzagonerako ndi kutsatsa malonda, ndi kupindula nao;

inu amene simudziwa chimene chidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthawi, ndi pamenepo ukanganuka.

Mukadanena inu, Akalola Mulungu, ndipo tikakhala ndi moyo, tidzachita kakutikakuti.

Koma tsopano mudzitamandira m'kudzikuza kwanu; kudzitamandira kulikonse kotero nkoipa.

Potero kwa iye amene adziwa kuchita bwino, ndipo sachita, kwa iye kuli tchimo.

Mulakalaka, ndipo zikusowani; mukupha, nimuchita kaduka, ndipo simukhoza kupeza; mulimbana, nimuchita nkhondo; mulibe kanthu, chifukwa simupempha.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 3:3

pakuti, pokhala pali nkhwidzi ndi ndeu pakati pa inu simuli athupi kodi, ndi kuyendayenda monga mwa munthu?

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 24:6-7

Koma inu mudzayamba kumva za nkhondo, ndi mbiri za nkhondo; onani, musadere nkhawa; pakuti kuyenera kuti izi zioneke; koma chitsiriziro sichinafike.

Pakuti mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zivomezi m'malo akutiakuti.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 120:7

Ine ndikuti, Mtendere; koma polankhula ine, iwowa akuti, Nkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 144:1

Wolemekezeka Yehova thanthwe langa, wakuphunzitsa manja anga achite nkhondo, zala zanga zigwirane nao:

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 29:22

Mwamuna wamkwiyo aputa makangano; waukali achuluka zolakwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Mika 4:3

Ndipo Iye adzaweruza mwa mitundu yambiri ya anthu, nadzadzudzula amitundu amphamvu ali kutali; ndipo iwo adzasula malupanga ao akhale makasu, ndi mikondo yao ikhale zolimira, mtundu wa anthu sudzasamulira mtundu unzake lupanga, kapena kuphunziranso nkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 15:3

Yehova ndiye wankhondo; dzina lake ndiye Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 20:1

Pamene mutuluka pa mdani wanu kunkhondo, ndi kuona akavalo ndi magaleta ndi anthu akuchulukira inu, musawaopa; popeza Yehova Mulungu wanu, amene anakukwezani kukutulutsani m'dziko la Ejipito, ali ndi inu.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mbiri 25:12

Ndi ana a Yuda anagwira zikwi khumi ena amoyo, nabwera nao pamwamba pa thanthwe, naphwanyika onsewo.

Mutu    |  Mabaibulo
Zekariya 14:2

Pakuti ndidzasonkhanitsa amitundu onse alimbane ndi Yerusalemu; ndipo mudziwo udzalandidwa, ndi nyumba zidzafunkhidwa, ndi akazi adzakakamizidwa; ndi limodzi la magawo awiri la mudzi lidzatuluka kunka kundende, koma anthu otsala sadzaonongeka m'mudzimo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 2:4

Iye adzaweruza pakati pa akunja, adzadzudzula mitundu yambiri ya anthu; ndipo iwo adzasula malupanga ao akhale zolimira, ndi nthungo zao zikhale makasu; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 20:4

pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye wakumuka nanu, kugwirira inu pa adani anu, kukupulumutsani.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mbiri 22:8

Koma mau a Yehova anandidzera, kuti, Wakhetsa mwazi wochuluka, popeza wachita nkhondo zazikulu; sudzamangira dzina langa nyumba, popeza wakhetsa pansi mwazi wambiri pamaso panga;

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 18:34

Aphunzitsa manja anga agwire nkhondo; kuti walifuka uta wamkuwa ndi manja anga.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Samueli 17:47

Ndi msonkhano wonse uno udzazindikira kuti Yehova sapulumutsa ndi lupanga, kapena ndi mkondo; pakuti Yehova ndiye mwini nkhondo, ndipo Iye adzakuperekani inu m'manja athu.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Samueli 22:35

Iye aphunzitsa manja anga nkhondo; kotero kuti manja anga alifula uta wamkuwa.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mbiri 20:15

nati iye, Tamverani Ayuda inu nonse, ndi inu okhala m'Yerusalemu, ndi inu mfumu Yehosafati, atero nanu Yehova, Musaope musatenge nkhawa chifukwa cha aunyinji ambiri awa; pakuti nkhondoyi si yanu, koma ya Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 46:1-3

Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m'masautso.

Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu, Ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka pa dziko lapansi.

Yehova wa makamu ali ndi ife, Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.

Chifukwa chake sitidzachita mantha, lingakhale lisandulika dziko lapansi, angakhale mapiri asunthika, nakhala m'kati mwa nyanja.

Chinkana madzi ake akokoma, nachita thovu, nagwedezeka mapiri ndi kudzala kwake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 76:3

Pomwepo anathyola mivi ya pauta; chikopa, ndi lupanga, ndi nkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 144:2

Ndiye chifundo changa, ndi linga langa, msanje wanga, ndi Mpulumutsi wanga; chikopa changa, ndi Iye amene ndimtama; amene andigonjetsera anthu anga.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 9:5

Pakuti zida zonse za mwamuna wovala zida za nkhondo m'phokosomo, ndi zovala zovimvinika m'mwazi, zidzakhala zonyeka ngati nkhuni.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 31:4

Pakuti Yehova atero kwa ine, Monga mkango, ndi mwana wa mkango wobangula pa nyama yake, sudzaopa mau a khamu la abusa oitanidwa kuupirikitsa, ngakhale kudzichepetsa wokha, chifukwa cha phokoso lao; motero Yehova wa makamu adzatsikira kumenyana nkhondo kuphiri la Ziyoni, ndi kuchitunda kwake komwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 42:13

Yehova adzatuluka ngati munthu wamphamvu; adzautsa nsanje ngati munthu wa nkhondo; Iye adzafuula, inde adzakuwa zolimba; adzachita zamphamvu pa adani ake.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 59:19

Chomwecho iwo adzaopa dzina la Yehova kuchokera kumadzulo, ndi ulemerero wake kumene kutulukira dzuwa; pakuti pamene mdani adzafika ngati chigumula, mzimu wa Yehova udzamkwezera mbendera yomletsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 51:20-23

Iwe ndiwe chibonga changa ndi zida zanga za nkhondo; ndi iwe ndidzathyolathyola amitundu, ndi iwe ndidzaononga maufumu;

ndi iwe ndidzathyolathyola kavalo ndi wokwera wake;

ndi iwe ndidzathyolathyola galeta ndi iye wokweramo; ndi iwe ndidzathyolathyola mwamuna ndi mkazi; ndi iwe ndidzathyolathyola wokalamba ndi mnyamata; ndi iwe ndidzathyolathyola mnyamata ndi namwali;

ndi iwe ndidzathyolathyola mbusa ndi zoweta zake; ndi iwe ndidzathyolathyola wakulima ndi goli la ng'ombe lake; ndi iwe ndidzathyolathyola akazembe ndi ziwanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 30:3

Pakuti layandikira tsiku, layandikira tsiku la Yehova, tsiku lamitambo, ndiyo nyengo ya amitundu.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 39:9

Ndipo iwo okhala m'midzi ya Israele adzatuluka, nadzasonkha moto, nadzatentha zida za nkhondo, ndi zikopa zotchinjiriza, mauta, ndi mivi, ndi ndodo, ndi mikondo; ndipo adzasonkha moto nazo zaka zisanu ndi ziwiri;

Mutu    |  Mabaibulo
Amosi 1:1

Mau a Amosi, amene anali mwa oweta ng'ombe a ku Tekowa, ndiwo amene anawaona za Israele masiku a Uziya mfumu ya Yuda, ndi masiku a Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele, zitatsala zaka ziwiri chisanafike chivomezi.

Mutu    |  Mabaibulo
Yoweli 3:9

Mulalikire ichi mwa amitundu, mukonzeretu nkhondo; utsani amuna amphamvu; amuna onse a nkhondo ayandikire nakwere.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:37

Koma m'zonsezi, ife tilakatu, mwa Iye amene anatikonda.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 6:12

Limba nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro, gwira moyo wosatha, umene adakuitanira, ndipo wavomereza chivomerezo chabwino pamaso pa mboni zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 6:12

Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 10:3-4

Pakuti pakuyendayenda m'thupi, sitichita nkhondo monga mwa thupi,

(pakuti zida za nkhondo yathu sizili za thupi, koma zamphamvu mwa Mulungu zakupasula malinga);

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 68:1

Auke Mulungu, abalalike adani ake; iwonso akumuda athawe pamaso pake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:165

Akukonda chilamulo chanu ali nao mtendere wambiri; ndipo alibe chokhumudwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 11:32-34

Ndipo ndinene chiyaninso? Pakuti idzandiperewera nthawi ndifotokozere za Gideoni, Baraki, Samisoni, Yefita; za Davide, ndi Samuele ndi aneneri;

mene mwa chikhulupiriro anagonjetsa maufumu, anachita chilungamo, analandira malonjezano, anatseka pakamwa mikango,

nazima mphamvu ya moto, napulumuka lupanga lakuthwa, analimbikitsidwa pokhala ofooka, anakula mphamvu kunkhondo, anapirikitsa magulu a nkhondo yachilendo.

Mutu    |  Mabaibulo
Genesis 14:14-16

Pamene anamva Abramu kuti mphwake anagwidwa, anatuluka natsogolera anyamata ake opangika, obadwa kunyumba kwake, mazana atatu kudza khumi ndi asanu ndi atatu, nawalondola kufikira ku Dani.

Ndipo anadzigawanizira iwo usiku, iye ndi anyamata ake, nawakantha, nawapirikitsa kufikira ku Hoba, ndiko ku dzanja lamanzere la ku Damasiko.

Ndipo anabwera nacho chuma chonse, nabwera naye Loti yemwe ndi chuma chake, ndi akazi ndi anthu omwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 14:14

Yehova adzakugwirirani nkhondo, ndipo inu mudzakhala chete.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 1:30

Yehova Mulungu wanu wakutsogolera inu, Iye adzathirira inu nkhondo, monga mwa zonse anakuchitirani m'Ejipito pamaso panu;

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 3:22

Musawaopa popeza Yehova Mulungu wanu, ndiye agwirira inu nkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 20:8

Pamenepo akapitao anenenso kwa anthu, ndi kuti, Munthuyo ndani wakuchita mantha ndi wofumuka mtima? Amuke nabwerere kunyumba kwake, ingasungunuke mitima ya abale ake monga mtima wake.

Mutu    |  Mabaibulo
Yoswa 1:9

Kodi sindinakulamulira iwe? Khala wamphamvu, nulimbike mtima, usaope, kapena kutenga nkhawa, pakuti Yehova Mulungu wako ali ndi iwe kulikonse umukako.

Mutu    |  Mabaibulo
Yoswa 10:25

Pamenepo Yoswa ananena nao, Musaope, musatenge nkhawa; khalani amphamvu, nimulimbike mtima; pakuti Yehova adzatero ndi adani anu onse amene mugwirana nao nkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo
Oweruza 5:2

Lemekezani Yehova pakuti atsogoleri m'Israele anatsogolera, pakuti anthu anadzipereka mwaufulu.

Mutu    |  Mabaibulo
Oweruza 7:20

Ndi magulu atatuwo anaomba malipenga, naswa mbiyazo, nagwira miuni ndi dzanja lao lamanzere, ndi malipenga m'dzanja lao lamanja kuwaomba; ndipo anafuula, Lupanga la Yehova ndi la Gideoni.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Samueli 10:5

Ndipo m'tsogolo mwake mudzafika kuphiri la Mulungu, kumene kuli kaboma ka Afilisti; ndipo kudzali kuti pakufika inu kumudziko mudzakomana ndi gulu la aneneri, alikutsika kumsanje ndi chisakasa, ndi lingaka, ndi chitoliro, ndi zeze, pamaso pao; iwo adzanenera;

Mutu    |  Mabaibulo
1 Samueli 13:3

Ndipo Yonatani anathyola kaboma ka Afilisti lokhala ku Geba, ndipo Afilisti anamva za ichi. Ndipo Saulo analiza lipenga m'dziko monse, nati, Amve Ahebri.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Samueli 14:6

Ndipo Yonatani ananena ndi mnyamata wonyamula zida zake, Tiye tipite ku kaboma ka osadulidwa awa; kapena Yehova adzatigwirira ntchito; pakuti palibe chomletsa Yehova kupulumutsa angakhale ndi ambiri kapena ndi owerengeka.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Samueli 14:52

Ndipo panali nkhondo yowawa ndi Afilisti masiku onse a Saulo; ndipo Saulo pakuona munthu wamphamvu, kapena ngwazi, anamtenga akhale naye.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Samueli 17:1-2

Pamenepo Afilisti anasonkhanitsa makamu ao a nkhondo, naunjikana ku Soko wa ku Yuda, namanga zithando pakati pa Soko ndi Azeka ku Efesi-Damimu.

Nati Mfilistiyo, Ine ndinyoza makamu a nkhondo a Israele lero; mundipatse munthu, kuti tilimbane ife awiri.

Ndipo pamene Saulo ndi Aisraele onse anamva mau ao a Mfilistiyo, anadodoma, naopa kwambiri.

Tsono Davide anali mwana wa Mwefurati uja wa ku Betelehemu-Yuda, dzina lake ndiye Yese; ameneyu anali nao ana amuna asanu ndi atatu; ndipo m'masiku a Saulo munthuyo anali nkhalamba, mwa anthu.

Ndipo ana atatu akulu a Yese anatsata Saulo kunkhondoko; ndi maina ao a ana ake atatuwo adapita ku nkhondowo ndiwo Eliyabu woyambayo, ndi mnzake womponda pamutu pake Abinadabu, ndi wachitatu Sama.

Ndipo Davide anali wotsiriza; ndi akulu atatuwo anamtsata Saulo.

Koma Davide akamuka kwa Saulo, nabwerera kudzadyetsa nkhosa za atate wake ku Betelehemu.

Ndipo Mfilistiyo anayandikira m'mawa ndi madzulo, nadzionetsera masiku makumi anai.

Ndipo Yese anati kwa Davide mwana wake, Uwatengere abale ako efa wa tirigu uyu wokazinga, ndi mikate iyi khumi, nuthamangire nazo kuzithando kwa abale ako;

nunyamule nchinchi izi khumi zamase ukapatse mtsogoleri wa chikwi chao, nukaone m'mene akhalira abale ako, nulandire chikole chao.

Tsono Saulo, ndi iwowa, ndi anthu onse a Israele, anali m'chigwa cha Ela, ku nkhondo ya Afilisti.

Ndipo Saulo ndi anthu a Israele anasonkhana, namanga zithando pa chigwa cha Ela, nandandalitsa nkhondo yao kuti akaponyane ndi Afilisti.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Samueli 10:12

Ulimbike mtima, ndipo tichite chamuna lero chifukwa cha anthu athu ndi midzi ya Mulungu wathu; Yehova nachite chomkomera.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Samueli 11:1

Ndipo kunali pofikanso chaka, nyengo yakutuluka mafumu, Davide anatumiza Yowabu, pamodzi ndi anyamata ake, ndi Aisraele onse; ndipo iwo anasakaza ana a Amoni, naumangira misasa yankhondo Raba. Koma Davide anatsalira ku Yerusalemu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mafumu 20:23

Ndipo anyamata a mfumu ya Aramu anati kwa iye, Milungu yao nja kumapiri, ndimo m'mene atilakira; koma tikaponyana nao kuchidikha, zedi tidzaposa mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mafumu 6:16

Nati iye, Usaopa, pakuti okhala pamodzi ndi ife achuluka koposa aja okhala pamodzi ndi iwo.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mafumu 19:35

Ndipo kunali, usiku womwewo mthenga wa Yehova anatuluka, nakantha m'misasa ya Aasiriya zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu kudza zisanu, ndipo pouka anthu mamawa, taonani, onsewo ndi mitembo.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mbiri 5:22

Pakuti adagwa, nafa ambiri, popeza nkhondoyi nja Mulungu. Ndipo anakhala m'malo mwao mpaka anatengedwa ndende.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mbiri 14:11

Atafika tsono ku Baala-Perazimu, Davide anawakantha komweko; nati Davide, Mulungu anapasula adani anga ndi dzanja langa, ngati pokhamulira madzi. Chifukwa chake analitcha dzina la malowo Baala-Perazimu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mbiri 29:11

Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi chipambano, ndi chifumu ndi zanu, Yehova; pakuti zonse zam'mwamba ndi pa dziko lapansi ndi zanu; ufumu ndi wanu, Yehova; ndipo mwakwezeka mutu wa pa zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mbiri 15:7

Koma limbikani inu, manja anu asalende; pakuti ku ntchito yanu kuli mphotho.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mbiri 20:20

Nalawira mamawa, natuluka kunka kuchipululu cha Tekowa; ndipo potuluka iwo, Yehosafati anakhala chilili, nati, Mundimvere ine, Ayuda inu, ndi inu okhala m'Yerusalemu, limbikani mwa Yehova Mulungu wanu, ndipo mudzakhazikika; khulupirirani aneneri ake, ndipo mudzalemerera.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 27:1

Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:14

Oipa anasolola lupanga, nakoka uta wao; alikhe ozunzika ndi aumphawi, aphe amene ali oongoka m'njira.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 55:18

Anaombola moyo wanga kunkhondo yondilaka, ndikhale mumtendere, pakuti ndiwo ambiri okangana nane.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 56:9

Pamenepo adani anga adzabwerera m'mbuyo tsiku lakuitana ine. Ichi ndidziwa, kuti Mulungu avomerezana nane.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 68:30

Dzudzulani chilombo cha m'bango, khamu la mphongo ndi ng'ombe za anthu, yense wakudzigonjera ndi ndalama za siliva; anabalalitsa mitundu ya anthu ya kukondwera nayo nkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 83:1-4

Mulungu musakhale chete; musakhale duu, osanena kanthu, Mulungu.

amene anaonongeka ku Endori; anakhala ngati ndowe ya kumunda.

Muwaike akulu ao ngati Orebu ndi Zeebu; mafumu ao ngati Zeba ndi Zalimuna,

amene anati, Tilande malo okhalamo Mulungu, akhale athu.

Mulungu wanga, muwaike akhale ngati mungu; ngati ziputu zomka ndi mphepo.

Monga moto upsereza nkhalango, ndi monga lawi liyatsa mapiri.

Momwemo muwatsate ndi namondwe, nimuwaopse ndi kamvulumvulu wanu.

Achititseni manyazi pankhope pao; kuti afune dzina lanu, Yehova.

Achite manyazi, naopsedwe kosatha; ndipo asokonezeke, naonongeke.

Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.

Pakuti taonani, adani anu aphokosera, ndipo okwiyira Inu aweramutsa mutu.

Apangana mochenjerera pa anthu anu, nakhalira upo pa obisika anu.

Amati, Tiyeni tiwaononge asakhalenso mtundu wa anthu; ndipo dzina la Israele lisakumbukikenso.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 89:43

Munapinditsa kukamwa kwake kwa lupanga lake, osamuimika kunkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 94:1

Mulungu wakubwezera chilango, Yehova, Mulungu wakubwezera chilango, muoneke wowala.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 144:5-6

Weramutsani thambo lanu, Yehova, nimutsike: Khudzani mapiri ndipo adzafuka.

Ng'animitsani mphezi, ndi kuwabalalitsa; tumizani mivi yanu, ndi kuwapirikitsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 21:31

Kavalo amakonzedweratu chifukwa cha tsiku la nkhondo; koma wopulumutsa ndiye Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 40:2

Munene inu zotonthoza mtima kwa Yerusalemu, nimufuulire kwa iye, kuti nkhondo yake yatha, kuti kuipa kwake kwakhululukidwa; kuti iye walandira mowirikiza m'dzanja la Yehova, chifukwa cha machimo ake onse.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 41:10

usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 41:15

Taona, ndidzakuyesa iwe choombera tirigu chatsopano chakuthwa chokhala ndi mano; iwe udzaomba mapiri ndi kuwapera asalale, ndi kusandutsa zitunda mungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 54:17

Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m'chiweruzo udzalitsutsa. Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova, ndi chilungamo chao chimene chifuma kwa Ine, ati Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 51:46

Mtima wanu usalefuke, musaope chifukwa cha mbiri imene idzamveka m'dzikomu; pakuti mbiri idzafika chaka china, pambuyo pake chaka china mbiri ina, ndi chiwawa m'dziko, wolamulira kumenyana ndi wolamulira.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 38:19

Pakuti ndanena mu nsanje yanga, ndi m'moto wa kuzaza kwanga, Zoonadi tsiku ilo kudzakhala kugwedezeka kwakukulu m'dziko la Israele;

Mutu    |  Mabaibulo
Danieli 2:44

Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzaonongeka kunthawi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu ao onse, nudzakhala chikhalire.

Mutu    |  Mabaibulo
Danieli 11:40

Ndipo nthawi yotsiriza mfumu ya kumwera idzalimbana naye, ndi mfumu ya kumpoto idzamdzera ngati kamvulumvulu, ndi magaleta, ndi apakavalo, ndi zombo zambiri; nadzalowa m'maiko, nadzasefukira ndi kupitirira.

Mutu    |  Mabaibulo
Yoweli 3:14

Aunyinji, aunyinji m'chigwa chotsirizira mlandu! Pakuti layandikira tsiku la Yehova m'chigwa chotsirizira mlandu.

Mutu    |  Mabaibulo
Amosi 2:1

Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Mowabu, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anatentha mafupa a mfumu ya ku Edomu asanduke njereza;

Mutu    |  Mabaibulo
Obadiya 1:15

Pakuti tsiku la Yehova layandikira amitundu onse; monga unachita iwe, momwemo adzakuchitira; chochita iwe chidzakubwerera pamtu pako.

Mutu    |  Mabaibulo
Mika 7:16

Amitundu adzaona nadzachita manyazi ndi mphamvu yao yonse; adzagwira pakamwa, m'makutu mwao mudzagontha.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 24:6

Koma inu mudzayamba kumva za nkhondo, ndi mbiri za nkhondo; onani, musadere nkhawa; pakuti kuyenera kuti izi zioneke; koma chitsiriziro sichinafike.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 26:52

Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Tabweza lupanga lako m'chimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzaonongeka ndi lupanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 21:9

Ndipo pamene mudzamva za nkhondo ndi mapanduko, musaopsedwa; pakuti ziyenera izi ziyambe kuchitika; koma mathedwe sakhala pomwepo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 16:33

Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalingonjetsa dziko lapansi Ine.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 7:43

Ndipo munatenga chihema cha Moleki, ndi nyenyezi ya mulungu Refani, zithunzizo mudazipanga kuzilambira; ndipo ndidzakutengani kunka nanu m'tsogolo mwake mwa Babiloni.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 12:4

Ndipo m'mene adamgwira, anamuika m'ndende, nampereka kwa magulu anai a alonda, lonse anaianai, amdikire iye; ndipo anafuna kumtulutsa kudza naye kwa anthu atapita Paska.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 13:4

pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu, kuchitira iwe zabwino. Koma ngati uchita choipa, opatu, pakuti iye sagwira lupanga kwachabe; pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu wakukwiyira ndi kubwezera chilango wochita zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 15:30

Ndipo ndikudandaulirani, abale, ndi Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi chikondi cha Mzimu, kuti mudzalimbike pamodzi ndi ine m'mapemphero anu kwa Mulungu chifukwa cha ine;

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 1:10

amene anatilanditsa mu imfa yaikulu yotere, nadzalanditsa; amene timyembekezera kuti adzalanditsanso;

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 4:8-9

ndife osautsika monsemo, koma osapsinjika; osinkhasinkha, koma osakhala kakasi;

olondoleka, koma osatayika; ogwetsedwa, koma osaonongeka;

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 5:17

Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zimene muzifuna musazichite.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 1:27

Chokhachi, mayendedwe anu ayenere Uthenga Wabwino wa Khristu: kuti, ndingakhale nditi ndilinkudza ndi kuona inu, ndingakhale nditi ndili kwina, ndikamva za kwa inu, kuti muchilimika mu mzimu umodzi, ndi kugwirira pamodzi ndi moyo umodzi chikhulupiriro cha Uthenga Wabwino;

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:6

Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Atesalonika 5:8

Koma ife popeza tili a usana tisaledzere, titavala chapachifuwa cha chikhulupiriro ndi chikondi; ndi chisoti chili chiyembekezo cha chipulumutso.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Atesalonika 1:4

kotero kuti ife tokha tidzitamandira za inu m'Mipingo ya Mulungu, chifukwa cha chipiriro chanu, ndi chikhulupiriro chanu, m'mazunzo anu onse ndi zisautsozo muzimva;

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 1:18

Lamulo ili ndipereka kwa iwe, mwana wanga Timoteo, kuti, monga mwa zonenera zidakutsogolera iwe kale, ulimbane nayo nkhondo yabwino;

Mutu    |  Mabaibulo
2 Timoteyo 2:3

Umve zowawa pamodzi nane monga msilikali wabwino wa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 11:34

nazima mphamvu ya moto, napulumuka lupanga lakuthwa, analimbikitsidwa pokhala ofooka, anakula mphamvu kunkhondo, anapirikitsa magulu a nkhondo yachilendo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 4:1

Zichokera kuti nkhondo, zichokera kuti zolimbana mwa inu? Kodi sizichokera kuzikhumbitso zanu zochita nkhondo m'ziwalo zanu?

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 12:7

Ndipo munali nkhondo m'mwamba. Mikaele ndi angelo ake akuchita nkhondo ndi chinjoka; chinjokanso ndi angelo ake chinachita nkhondo;

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 19:11

Ndipo ndinaona mutatseguka m'Mwamba; ndipo taonani, kavalo woyera, ndi Iye wakumkwera wotchedwa Wokhulupirika ndi Woona; ndipo aweruza, nachita nkhondo molungama.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 60:12

Mwa Mulungu tidzachita molimbika mtima, ndipo Iye adzapondereza otisautsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 98:1

Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano; popeza anachita zodabwitsa: Dzanja lake lamanja, mkono wake woyera, zinamchitira chipulumutso.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:95

Oipa anandilalira kundiononga; koma ndizindikira mboni zanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 43:1

Koma tsopano atero Yehova, amene anakulenga iwe Yakobo, ndi Iye amene anakupanga iwe Israele, Usaope, chifukwa ndakuombola iwe, ndakutchula dzina lako, iwe uli wanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 37:10

M'mwemo ndinanenera monga anandiuza, ndi mpweya unawalowa, ndipo anakhala ndi moyo, naimirira chilili, gulu la nkhondo lalikulukulu ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 5:9

Odala ali akuchita mtendere; chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 12:25

Ndipo Yesu anadziwa maganizo ao, nati kwa iwo, Ufumu uliwonse wogawanika pa wokha sukhalira kupasuka, ndi mudzi uliwonse kapena banja logawanika pa lokha silidzakhala;

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 24:7

Pakuti mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zivomezi m'malo akutiakuti.

Mutu    |  Mabaibulo
Marko 13:8

Pakuti mtundu wa anthu udzayambana ndi mtundu wina, ndipo ufumu ndi ufumu unzake: padzakhala zivomezi m'malo m'malo; padzakhala njala; izi ndi zoyambira za zowawa.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 14:31

Kapena mfumu yanji pakupita kukomana ndi nkhondo ya mfumu inzake, sathanga wakhala pansi, nafunsana ndi akulu ngati akhoza ndi asilikali ake zikwi khumi kulimbana naye wina uja alikudza kukomana naye ndi asilikali zikwi makumi awiri?

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 22:36

Ndipo anati kwa iwo, Koma tsopano, iye amene ali ndi thumba la ndalama, alitenge, ndi thumba la kamba lomwe; ndipo amene alibe, agulitse chofunda chake, nagule lupanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 14:27

Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. Mtima wanu usavutike, kapena usachite mantha.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 1:8

Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m'Yerusalemu, ndi m'Yudeya lonse, ndi m'Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:31

Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 15:57

koma ayamikike Mulungu, amene atipatsa ife chigonjetso mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 2:14

Koma ayamikike Mulungu, amene atitsogolera m'chigonjetso mwa Khristu, namveketsa fungo la chidziwitso chake mwa ife pamalo ponse.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 2:14

Pakuti Iye ndiye mtendere wathu, amene anachita kuti onse awiri akhale mmodzi, nagumula khoma lakudulitsa pakati,

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 1:28

osaopa adani m'kanthu konse, chimene chili kwa iwowa chisonyezo cha chionongeko, koma kwa inu cha chipulumutso, ndicho cha kwa Mulungu;

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 3:20

Pakuti ufulu wathu uli Kumwamba; kuchokera komwenso tilindirira Mpulumutsi, Ambuye Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 5:8-9

Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire:

ameneyo mumkanize okhazikika m'chikhulupiriro, podziwa kuti zowawa zomwezo zilimkukwaniridwa pa abale anu ali m'dziko.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 3:21

Iye wakupambana, ndidzampatsa akhale pansi ndi Ine pa mpando wachifumu wanga, monga Inenso ndinalakika, ndipo ndinakhala pansi ndi Atate wanga pa mpando wachifumu wake.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 12:11

Ndipo iwo anamlaka iye chifukwa cha mwazi wa Mwanawankhosa, ndi chifukwa cha mau a umboni wao; ndipo sanakonda moyo wao kungakhale kufikira imfa.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 20:10

Ndipo mdierekezi wakuwasokeretsa anaponyedwa m'nyanja ya moto ndi sulufure, kumeneko kulinso chilombocho ndi mneneri wonyengayo; ndipo adzazunzidwa usana ndi usiku kunthawi za nthawi.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 5:8

Yehova, munditsogolere m'chilungamo chanu, chifukwa cha akundizondawo; mulungamitse njira yanu pamaso panga.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 18:39

Pakuti mwandizingiza mphamvu m'chuuno ku nkhondoyo; mwandigonjetsera amene andiukira.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 22:28

Pakuti ufumuwo ngwa Yehova; Iye achita ufumu mwa amitundu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 24:8

Mfumu imene ya ulemerero ndani? Yehova wamphamvu ndi wolimba, Yehova wolimba kunkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 27:3

Lingakhale gulu la ankhondo limanga misasa kuti andithyole, mtima wanga sungachite mantha; ingakhale nkhondo ikandiukira, inde pomweponso ndidzakhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 46:9

Aletsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi; athyola uta, nadula nthungo; atentha magaleta ndi moto.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 2:7

Iye asungira oongoka mtima nzeru yeniyeni; ndiye chikopa cha oyenda molunjika;

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 21:30

Kulibe nzeru ngakhale luntha ngakhale uphungu wotsutsana ndi Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 2:2-4

Ndipo padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pa nsonga ya mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda; mitundu yonse idzasonkhana kumeneko.

Tsiku limenelo munthu adzataya kumfuko ndi kumileme mafano ake asiliva ndi agolide amene anthu anampangira iye awapembedze;

kuti akalowe m'mapanga a m'matanthwe, ndi m'mindala a m'miyala, kuthawa kuopsa kwa Yehova, ndi ulemerero wachifumu wake, podzuka Iye kugwedeza dziko ndi mphamvu.

Siyani munthu, amene mpweya wake uli m'mphuno mwake; chifukwa m'mene awerengedwamo ndi muti?

Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kunka kuphiri la Yehova, kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m'mayendedwe ake; chifukwa m'Ziyoni mudzatuluka chilamulo, ndi mau a Yehova kuchokera m'Yerusalemu.

Iye adzaweruza pakati pa akunja, adzadzudzula mitundu yambiri ya anthu; ndipo iwo adzasula malupanga ao akhale zolimira, ndi nthungo zao zikhale makasu; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 40:10

Taonani, Ambuye Yehova adzadza ngati wamphamvu, ndipo mkono wake udzalamulira; taonani, mphotho yake ili ndi Iye, ndipo chobwezera chake chili patsogolo pa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 54:16-17

Taona, ndalenga wachipala amene avukuta moto wamakala, ndi kutulutsamo chida cha ntchito yake; ndipo ndalenga woononga kuti apasule.

Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m'chiweruzo udzalitsutsa. Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova, ndi chilungamo chao chimene chifuma kwa Ine, ati Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
Mika 4:1-3

Koma kudzachitika masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pamwamba pa mapiri, nilidzakuzika pamwamba pa zitunda; ndi mitundu ya anthu idzayendako.

Imva zowawa, nuyesetse kubala, mwana wamkazi wa Ziyoni, ngati mkazi wakubala; pakuti udzatuluka m'mudzi tsopano, nudzakhala kuthengo, nudzafika ku Babiloni; komweko udzapulumutsidwa; komweko Yehova adzakuombola m'manja a adani ako.

Ndipo tsopano amitundu ambiri asonkhana kuyambana nawe, akuti, Aipsidwe, diso lathu lipenye ku Ziyoni.

Koma sadziwa zolingirira za Yehova, kapena kuzindikira uphungu wake; pakuti anawasonkhanitsa ngati mitolo kudwale.

Nyamuka nupunthe, mwana wamkazi wa Ziyoni; pakuti ndidzasanduliza nyanga yako ikhale yachitsulo, ndi ziboda zako zikhale zamkuwa; ndipo udzaphwanya mitundu yambiri ya anthu; ndipo uzipereka chiperekere phindu lao kwa Yehova, ndi chuma chao kwa Ambuye wa dziko lonse lapansi.

Ndipo amitundu ambiri adzamuka, nadzati, Tiyeni, tikwere kuphiri la Yehova, ndi kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; kuti Iye atiphunzitse njira zake, ndipo tidzayenda m'mabande ake; pakuti ku Ziyoni kudzatuluka chilamulo, ndi ku Yerusalemu mau a Yehova.

Ndipo Iye adzaweruza mwa mitundu yambiri ya anthu, nadzadzudzula amitundu amphamvu ali kutali; ndipo iwo adzasula malupanga ao akhale makasu, ndi mikondo yao ikhale zolimira, mtundu wa anthu sudzasamulira mtundu unzake lupanga, kapena kuphunziranso nkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 10:34

Musalingalire kuti ndidadzera kuponya mtendere pa dziko lapansi; sindinadzera kuponya mtendere, koma lupanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 3:14

Ndipo asilikali omwe anamfunsa iye, nati, Nanga ife tizichita chiyani? Ndipo iye anati kwa iwo, Musaopse, musanamize munthu aliyense; khalani okhuta ndi kulipira kwanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 14:31-32

Kapena mfumu yanji pakupita kukomana ndi nkhondo ya mfumu inzake, sathanga wakhala pansi, nafunsana ndi akulu ngati akhoza ndi asilikali ake zikwi khumi kulimbana naye wina uja alikudza kukomana naye ndi asilikali zikwi makumi awiri?

Koma ngati sakhoza, atumiza akazembe, pokhala winayo ali kutalitali, nafunsa za mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 10:13

Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 4:7-9

Koma tili nacho chuma ichi m'zotengera zadothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife;

ndife osautsika monsemo, koma osapsinjika; osinkhasinkha, koma osakhala kakasi;

olondoleka, koma osatayika; ogwetsedwa, koma osaonongeka;

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 6:9

Koma tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:3-4

Pakuti munafa, ndipo moyo wanu wabisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu.

Pamene Khristu adzaoneka, ndiye moyo wathu, pamenepo inunso mudzaonekera pamodzi ndi Iye m'ulemerero.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 13:6

Kotero kuti tinena molimbika mtima, Mthandizi wanga ndiye Ambuye; sindidzaopa; adzandichitira chiyani munthu?

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 1:12

Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumkonda Iye.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 3:14

Komatu ngatinso mukumva zowawa chifukwa cha chilungamo, odala inu; ndipo musaope pakuwaopa iwo, kapena musadere nkhawa;

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 5:10

Ndipo Mulungu wa chisomo chonse, amene adakuitanani kulowa ulemerero wake wosatha mwa Khristu, mutamva zowawa kanthawi, adzafikitsa inu opanda chilema mwini wake, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 3:5

Iye amene alakika adzamveka motero zovala zoyera; ndipo sindidzafafaniza ndithu dzina lake m'buku la moyo, ndipo ndidzamvomereza dzina lake pamaso pa Atate wanga, ndi pamaso pa angelo ake.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 7:17

chifukwa Mwanawankhosa wakukhala pakati pa mpando wachifumu adzawaweta, nadzawatsogolera ku akasupe a madzi amoyo, ndipo Mulungu adzawapukutira misozi yonse pamaso pao.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 21:4

ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pao; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 22:3

Ndipo sipadzakhalanso temberero lililonse; ndipo mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa udzakhala momwemo; ndipo akapolo ake adzamtumikira Iye,

Mutu    |  Mabaibulo

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye wanga wachikondi, mzimu wanga ukutamanda dzina lanu ndi kukongola kwa chiyero chanu. Ndinu wamkulu, wabwino, wangwiro. Ndikuona chikondi chanu mmawa uliwonse, ndikuzunguliridwa ndi chifundo chanu chachikulu. Zikomo chifukwa chokhala nane nthawi zonse, chifukwa ndinu mphamvu yanga, amene amandilimbikitsa. Zikomo chifukwa cha banja lomwe mwandipatsa, chifukwa cha zonse zomwe ndili nazo, ndipo chifukwa chokhala mtendere wanga pakati pa mkuntho. Zikomo chifukwa cha zinthu zonse, chifukwa ndikudziwa kuti chisamaliro chanu chimakhalapo kosatha kwa onse okukhulupirirani. Tsopano Ambuye, ndikupempha kuti chifuniro chanu chilamulire dziko lino, kuti muchite mogwirizana ndi maganizo anu, ndi kuti muteteze miyoyo. Ndikudziwa kuti tili m'masiku otsiriza, ndipo Mawu anu amati tidzamva za nkhondo ndi mphekesera za nkhondo, koma mitima yathu isachite mantha. Ndikukupemphani kuti mutithandize kukhala chete m'chiyembekezo chomwe tili nacho mwa Inu. Atate wokondedwa, tibiseni pamalo anu otetezeka, ndipo mutenge ulamuliro pa zinthu zonse. M'dzina la Yesu, Ameni.