Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


146 Mau a m'Baibulo Okhudza Umphawi

146 Mau a m'Baibulo Okhudza Umphawi

M'mawu a Mulungu, timawerenga momwe Iye amatilimbikitsira kuthandiza osauka ndi kusamalira ofooka. Mtima wake umagunda chifukwa cha osowa, ndipo akutiuza kuti tichitepo kanthu powateteza!

Tili anthu a Mulungu, tiyenera kukumbukira kuti malemba ndi chisonyezero cha nzeru, chilango, ndi chikondi chosatha cha Mulungu, ndipo mmenemo Ambuye amalankhula nafe tonse kuti titonthoze ndikuthandiza osauka ndi osoŵa a dziko lino.

M’buku la Miyambo 3:27-28 (Buku Lopatulika) limati: “Usakana kuchitira zabwino munthu woyenera, pamene uli ndi mphamvu yochitira zimenezo. Usanene ndi mnzako, Pita, nubwerenso, ndipo mawa ndidzakupatsa, pamene uli nazo tsopano.” Kuyambira m’chipangano chakale mpaka chatsopano, tikuona chikhumbo cha Mulungu kuti ana ake achitire chifundo osauka ndi osoŵa.

Yesu anati osauka adzakhala nafe nthawi zonse, anatinso amene achitira chifundo osauka, odwala, ndi osoŵa, kwenikweni amatumikira Yesu mwiniwake (Mateyu 25:35-40) ndipo chifukwa chake, adzalandira mphotho.

Ndikukulangiza pano, kuti usakane kuchita zabwino, khalani chitoliro cha madalitso kwa onse omwe alibe chiyembekezo ndikusiya chizindikiro chosatha cha chikondi m'derali lomwe lawonongeka ndi chidani ndi kusayanjanitšana.




Afilipi 4:12

Ndadziwa ngakhale kupeputsidwa, ndadziwanso kusefukira; konseko ndi m'zinthu zonse ndalowa mwambo wakukhuta, ndiponso wakumva njala; wakusefukira, ndiponso wakusowa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:9

Tsegula pakamwa pako nuweruze molungama, nunenere osauka ndi aumphawi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 6:10

monga akumva chisoni, koma akukondwera nthawi zonse; monga aumphawi, koma akulemeretsa ambiri; monga okhala opanda kanthu, ndipo akhala nazo zinthu zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:35

Adzatisiyanitsa ndani ndi chikondi cha Khristu? Nsautso kodi, kapena kupsinjika mtima, kapena kuzunza, kapena njala, kapena usiwa, kapena zoopsa kapena lupanga kodi?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 9:18

Pakuti sadzaiwalika nthawi zonse waumphawi, kapena chiyembekezo cha ozunzika sichidzaonongeka kosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 10:12

Ukani, Yehova; samulani dzanja lanu, Mulungu; musaiwale ozunzika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:7

Alipo wodziyesa wolemera, koma alibe kanthu; alipo wodziyesa wosauka, koma ali ndi chuma chambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:17

Wochitira waumphawi chifundo abwereka Yehova; adzambwezera chokoma chakecho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:3

Odala ali osauka mumzimu; chifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:20

Ndipo Iye anakweza maso ake kwa ophunzira ake, nanena, Odala osauka inu; chifukwa uli wanu ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 82:3

Weruzani osauka ndi amasiye; weruzani molungama ozunzika ndi osowa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:6

Munthu uyu wozunzika anafuula, ndipo Yehova anamumva, nampulumutsa m'masautso ake onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:9

monga kwalembedwa, Anabalalitsa, anapatsa kwa osauka; chilungamo chake chikhale kunthawi yonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 2:5

Mverani, abale anga okondedwa; kodi Mulungu sanasankha osauka a dziko lapansi akhale olemera ndi chikhulupiriro, ndi olowa nyumba a ufumu umene adaulonjeza kwa iwo akumkonda Iye?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:2

Wolemera ndi wosauka akumana, wolenga onsewo ndiye Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 3:11

Koma iye anayankha nanena kwa iwo, Iye amene ali nao malaya awiri apatse kwa iye amene alibe; ndi iye amene ali nazo zakudya achite chomwecho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:31

Wotsendereza aumphawi atonza Mlengi wake; koma wochitira wosauka chifundo amlemekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 14:13-14

Koma pamene ukonza phwando uitane aumphawi, opunduka, otsimphina, akhungu; ndipo udzakhala wodala; chifukwa iwo alibe chakubwezera iwe mphotho; pakuti idzabwezedwa mphotho pa kuuka kwa olungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 12:5-6

Nanga mafuta onunkhira awa sanagulitsidwa chifukwa ninji ndi marupiya atheka mazana atatu, ndi kupatsidwa kwa osauka? Ndipo ndidziwa kuti lamulo lake lili moyo wosatha; chifukwa chake zimene ndilankhula, monga momwe Atate wanena ndi Ine, momwemo ndilankhula. Koma ananena ichi si chifukwa analikusamalira osauka, koma chifukwa anali mbala, ndipo pokhala nalo thumba, amaba zoikidwamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:22

Chotikondetsa munthu ndicho kukoma mtima kwake; ndipo wosauka apambana munthu wonama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 24:14

Musamasautsa wolembedwa ntchito, wakukhala waumphawi ndi wosauka, wa abale anu kapena wa alendo ali m'dziko mwanu, m'midzi mwanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:3

Ndipo ndingakhale ndipereka chuma changa chonse kudyetsa osauka, ndipo ndingakhale ndipereka thupi langa alitenthe m'moto, koma ndilibe chikondi, sindipindula kanthu ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 4:18

Mzimu wa Ambuye uli pa Ine, chifukwa chake Iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino: anandituma Ine kulalikira am'nsinga mamasulidwe, ndi akhungu kuti apenyanso, kutulutsa ndi ufulu ophwanyika,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 26:11

Pakuti nthawi zonse muli nao aumphawi pamodzi nanu; koma simuli ndi Ine nthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:25

Ndinali mwana ndipo ndakalamba; ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 2:10

pokhapo kuti tikumbukire aumphawi; ndicho chomwe ndinafulumira kuchichita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:17

Koma iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, naona mbale wake ali wosowa ndi kutsekereza chifundo chake pommana iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:27

Wogawira aumphawi sadzasowa; koma wophimba maso ake adzatembereredwa kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 109:16

Chifukwa kuti sanakumbukire kuchita chifundo, koma analondola wozunzika ndi waumphawi, ndi wosweka mtima, kuti awaphe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 22:25

Ukakongoletsa ndalama anthu anga osauka okhala nanu, usamkhalira ngati wangongole; usamwerengera phindu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:15

Chuma cha wolemera ndi mudzi wake wolimba; koma umphawi wao uononga osauka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 72:12-13

Pakuti adzapulumutsa waumphawi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphawi, nadzapulumutsa moyo wa aumphawi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:33

Gulitsani zinthu muli nazo, nimupatse mphatso zachifundo; mudzikonzere matumba a ndalama amene sakutha, chuma chosatha m'Mwamba, kumene mbala siziyandikira, ndipo njenjete siziononga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 41:1

Wodala iye amene asamalira wosauka! Tsiku la tsoka Yehova adzampulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 30:8-9

Mundichotsere kutali zachabe ndi mabodza; musandipatse umphawi, ngakhale chuma, mundidyetse zakudya zondiyenera; ndingakhute ndi kukukanani, ndi kuti, Yehova ndani? Kapena ndingasauke ndi kuba, ndi kutchula dzina la Mulungu wanga pachabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:21

Yesu ananena naye, Ngati ufuna kukhala wangwiro, pita, kagulitse zomwe uli nazo, nupatse aumphawi, ndipo udzakhala ndi chuma Kumwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 72:4

Adzaweruza ozunzika a mwa anthu, adzapulumutsa ana aumphawi, nadzaphwanya wosautsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:1

Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:24-25

Alipo wogawira, nangolemerabe; aliponso womana chomwe ayenera kupatsa nangosauka. Mtima wa mataya udzalemera; wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 11:5

akhungu alandira kuona kwao, ndi opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ndi ogontha akumva, ndi akufa aukitsidwa, ndi kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:17-19

Lamulira iwo achuma m'nthawi yino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziwika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo; kuti achite zabwino, nachuluke ndi ntchito zabwino, nakondwere kugawira ena, nayanjane; nadzikundikire okha maziko okoma ku nyengo ikudzayi, kuti akagwire moyo weniweniwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 69:33

Pakuti Yehova amvera aumphawi, ndipo sapeputsa am'ndende ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:5

Wochitira chiphwete aumphawi atonza Mlengi; wokondwera ndi tsoka sadzapulumuka chilango.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 18:22

Koma m'mene Yesu anamva, anati kwa iye, Usowa chinthu chimodzi: gulitsa zilizonse uli nazo, nugawire osauka; ndipo udzakhala nacho chuma chenicheni m'Mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:42

Kwa iye wopempha iwe umpatse, ndipo kwa iye wofuna kukukongola usampotolokere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:96

Ndinapenya malekezero ake a ungwiro wonse; koma lamulo lanu ndi lotakasuka ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:26

Pakuti kunakondweretsa a ku Masedoniya ndi Akaya kuchereza osauka a kwa oyera mtima a ku Yerusalemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:21

Woipa akongola, wosabweza, koma wolungama achitira chifundo, napereka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 5:8

Ukaona anthu alikutsendereza aumphawi, ndi kuchotsa chilungamo ndi chiweruzo mwachiwawa pa dera lina la dziko, usazizwepo; pakuti mkulu wopambana asamalira; ndipo alipo akulu ena oposa amenewo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 25:4

Chifukwa Inu mwakhala linga la aumphawi, linga la osowa m'kuvutidwa kwake, pobisalira chimphepo, mthunzi wa pa dzuwa, pamene kuomba kwa akuopsa kufanana ndi chimphepo chakuomba tchemba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:20

Waumphawi adedwa ndi anzake omwe; koma akukonda wolemera achuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:19-31

Ndipo panali munthu mwini chuma amavala chibakuwa ndi nsalu yabafuta, nasekera, nadyerera masiku onse; Ndipo anamuitana, nati kwa iye, Ichi ndi chiyani ndikumva za iwe? Undiwerengere za ukapitao wako; pakuti sungathe kukhalabe kapitao. ndipo wopemphapempha wina, dzina lake Lazaro, adaikidwa pakhomo pake wodzala ndi zilonda, ndipo anafuna kukhuta ndi zakugwa pa gome la mwini chumayo; komatu agalunso anadza nanyambita zilonda zake. Ndipo kunali kuti wopemphayo adafa, ndi kuti anatengedwa iye ndi angelo kunka kuchifuwa cha Abrahamu; ndipo mwini chumayo adafanso, naikidwa m'manda. Ndipo m'dziko la akufa anakweza maso ake, pokhala nao mazunzo, naona Abrahamu patali, ndi Lazaro m'chifuwa mwake. Ndipo anakweza mau nati, Atate Abrahamu, mundichitire chifundo, mutume Lazaro, kuti aviike nsonga ya chala chake m'madzi, naziziritse lilime langa; pakuti ndizunzidwadi m'lawi ili la moto. Koma Abrahamu anati, Mwana, kumbukira kuti unalandira zokoma zako pakukhala m'moyo iwe, momwemonso Lazaro zoipa; ndipo tsopano iye asangalatsidwa pano, koma iwe uzunzidwadi. Ndipo pamwamba pa izi, pakati pa ife ndi inu pakhazikika phompho lalikulu, kotero kuti iwo akufuna kuoloka kuchokera kuno kunka kwa inu sangathe, kapena kuchokera kwanuko kuyambuka kudza kwa ife, sangathenso. Koma anati, Pamenepo ndikupemphani, Atate, kuti mumtume kunyumba ya atate wanga; pakuti ndili nao abale asanu; awachitire umboni iwo kuti iwonso angadze kumalo ano a mazunzo. Koma Abrahamu anati, Ali ndi Mose ndi aneneri; amvere iwo. Ndipo kapitao uyu anati mumtima mwake, Ndidzachita chiyani, chifukwa mbuye wanga andichotsera ukapitao? Kulima ndilibe mphamvu, kupemphapempha kundichititsa manyazi. Koma anati, Iai, Atate Abrahamu, komatu ngati wina akapita kwa iwo wochokera kwa kufa adzasandulika mtima. Koma anati kwa iye, Ngati samvera Mose ndi aneneri, sadzakopeka mtima ngakhale wina akauka kwa akufa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 127:2

Kuli chabe kwa inu kulawirira mamawa ndi kusagonerapo madzulo, kudya mkate wosautsa kuupeza; kuli tero kuti izi apatsa okondedwa ake ngati m'tulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:9

Mwini diso lamataya adzadala; pakuti apatsa osauka zakudya zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 112:5

Wodala munthu wakuchitira chifundo, nakongoletsa; adzalimbika nao mlandu wake poweruzidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 146:7

ndiye wakuchitira chiweruzo osautsika; ndiye wakupatsa anjala chakudya; Yehova amasula akaidi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:13

Patsani zosowa oyera mtima; cherezani aulendo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:176

Ndinasochera ngati nkhosa yotayika; funani mtumiki wanu; pakuti sindiiwala malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 15:7-8

Akakhala ndi inu munthu waumphawi, ndiye wina wa abale anu, m'umodzi wa midzi yanu, m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, musakhakala mtima wanu, kapena kuumitsa dzanja lanu kukaniza mbale wanu waumphawi; koma muzimtansira dzanja lanu ndithu ndi kumkongoletsa ndithu zofikira kusowa kwake, monga umo amasowa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:11

koma chaka chachisanu ndi chiwiri uuleke, ugone; kuti aumphawi a anthu a mtundu wako adyemo, ndipo zotsalira nyama za kuthengo zizidye; momwemo uzichita ndi munda wako wamphesa, ndi munda wako wa azitona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 5:1-4

Nanga tsono achuma inu, lirani ndi kuchema chifukwa cha masautso anu akudza pa inu. Tengani, abale, chitsanzo cha kumva zowawa ndi kuleza mtima, aneneri amene analankhula m'dzina la Ambuye. Taonani tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo. Koma makamaka, abale anga, musalumbire, kungakhale kutchula kumwamba kapena dziko, kapena lumbiro lina lililonse; koma inde wanu akhale inde, ndi iai wanu akhale iai; kuti mungagwe m'chiweruziro. Kodi wina wa inu akumva zowawa? Apemphere. Kodi wina asekera? Aimbire. Pali wina kodi adwala mwa inu? Adziitanire akulu a Mpingo, ndipo apemphere pa iye, atamdzoza ndi mafuta m'dzina la Ambuye: ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo Ambuye adzamuukitsa; ndipo ngati adachita machimo adzakhululukidwa kwa iye. Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake. Eliya anali munthu wakumva zomwezi tizimva ife, ndipo anapemphera chipempherere kuti isavumbe mvula; ndipo siinagwa mvula pa dziko zaka zitatu kudza miyezi isanu ndi umodzi. Ndipo anapempheranso; ndipo m'mwamba munatsika mvula, ndi dziko lidabala zipatso zake. Abale anga, ngati wina wa inu asochera posiyana ndi choonadi, ndipo ambweza iye mnzake; Chuma chanu chaola ndi zovala zanu zajiwa ndi njenjete. azindikire, kuti iye amene abweza wochimwa kunjira yake yosochera adzapulumutsa munthu kwa imfa, ndipo adzavundikira machimo aunyinji. Golide wanu ndi siliva wanu zachita dzimbiri, ndipo dzimbiri lake lidzachita mboni zoneneza inu, ndipo zidzadya nyama yanu ngati moto. Mwadzikundikira chuma masiku otsiriza. Taonani, mphotho ya antchitowo anasenga m'minda yanu, yosungidwa ndi inu powanyenga, ifuula; ndipo mafuulo a osengawo adalowa m'makutu a Ambuye wa makamu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:24

Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 30:7-9

Zinthu ziwiri ndakupemphani, musandimane izo ndisanamwalire: Mundichotsere kutali zachabe ndi mabodza; musandipatse umphawi, ngakhale chuma, mundidyetse zakudya zondiyenera; ndingakhute ndi kukukanani, ndi kuti, Yehova ndani? Kapena ndingasauke ndi kuba, ndi kutchula dzina la Mulungu wanga pachabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:13

Wotseka makutu ake polira waumphawi, nayenso adzalira koma osamvedwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:2

Nyamuliranani zothodwetsa, ndipo kotero mufitse chilamulo cha Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 10:17-18

Yehova, mwamva chikhumbo cha ozunzika, mudzakhazikitsa mtima wao, mudzatchereza khutu lanu; kuti muweruze mlandu wa amasiye ndi wokhalira mphanthi, kuti munthu wa pa dziko lapansi angaonjeze kuopsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:10

M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 8:9

Pakuti mudziwa chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti, chifukwa cha inu anakhala wosauka, angakhale anali wolemera, kuti inu ndi kusauka kwake mukakhale olemera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 24:14-15

Musamasautsa wolembedwa ntchito, wakukhala waumphawi ndi wosauka, wa abale anu kapena wa alendo ali m'dziko mwanu, m'midzi mwanu. Pa tsiku lake muzimpatsa kulipira kwake, lisalowepo dzuwa; pakuti ndiye waumphawi, ndi mtima wake ukhumba uku; kuti angakulirireni kwa Yehova, ndipo kukukhalireni tchimo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 68:10

Gulu lanu linakhala m'dziko muja. Mwa ukoma wanu munalikonzera ozunzika, Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:16

Wotsendereza waumphawi kuti achulukitse chuma chake, ndi wopatsa wolemera kanthu, angosauka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:20-21

ndipo wopemphapempha wina, dzina lake Lazaro, adaikidwa pakhomo pake wodzala ndi zilonda, ndipo anafuna kukhuta ndi zakugwa pa gome la mwini chumayo; komatu agalunso anadza nanyambita zilonda zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:75

Ndidziwa kuti maweruzo anu ndiwo olungama, Yehova, ndi kuti munandizunza ine mokhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:29

Iye alimbitsa olefuka, naonjezera mphamvu iye ameme alibe mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:11

Wolemera adziyesa wanzeru; koma wosauka wozindikira aululitsa zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 146:5-6

Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti amthandize, chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake. Amene analenga zakumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zili m'mwemo. Ndiye wakusunga choonadi kosatha,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:23-24

Ndipo Yesu anati kwa ophunzira ake, Indetu ndinena kwa inu, kuti munthu mwini chuma adzalowa movutika mu Ufumu wa Kumwamba. Ndiponso ndinena kwa inu, Nkwapafupi kuti ngamira ipyole diso la singano, koposa mwini chuma kulowa Ufumu wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 72:13

Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphawi, nadzapulumutsa moyo wa aumphawi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 7:12

Pakuti nzeru itchinjiriza monga ndalama zitchinjiriza; koma kudziwa kupambana, chifukwa nzeru isunga moyo wa eni ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:24

Koma tsoka inu eni chuma! Chifukwa mwalandira chisangalatso chanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 88:15

Wozunzika ine ndi wofuna kufa kuyambira ubwana wanga; posenza zoopsa zanu, ndithedwa nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 132:15

Ndidzadalitsatu chakudya chake; aumphawi ake ndidzawakhutitsa ndi mkate.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:7

Wolungama asamalira mlandu wa osauka; koma woipa alibe nzeru yakuudziwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:25

Fulumira kuyanjana ndi mnzako wamlandu, pamene uli naye panjira; kapena mnzako wamlandu angakupereke iwe kwa woweruza mlandu, ndi woweruzayo angapereke iwe kwa msilikali, nuponyedwe iwe m'nyumba yandende.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 137:6

Lilime langa limamatike kunsaya zanga, ndikapanda kukumbukira inu; ndikapanda kusankha Yerusalemu koposa chimwemwe changa chopambana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:28

Wokhulupirira chuma chake adzagwa; koma olungama adzaphuka ngati tsamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:10

Misona ya mkango isowa nimva njala, koma iwo akufuna Yehova sadzasowa kanthu kabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 4:10

Pakuti akagwa, wina adzautsa mnzake; koma tsoka wakugwa wopanda womnyamutsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:18

Tiana, tisakonde ndi mau, kapena ndi lilime, komatu ndi kuchita ndi m'choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:4

Pakuti zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiriro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:36

Lingitsani mtima wanga kumboni zanu, si ku chisiriro ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 5:3-5

Chitira ulemu amasiye amene ali amasiye ndithu. Koma ngati wamasiye wina ali nao ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kuchitira ulemu a m'banja lao, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu. Koma iye amene ali wamasiye ndithu, nasiyidwa yekha, ayembekezera Mulungu, nakhalabe m'mapembedzo ndi mapemphero usiku ndi usana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:4

Wochita ndi dzanja laulesi amasauka; koma dzanja la akhama lilemeretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:32

Iye amene sanatimana Mwana wake wa Iye yekha, koma anampereka chifukwa cha ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi Iye?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 78:70-72

Ndipo anasankha Davide mtumiki wake, namtenga kumakola a nkhosa. Anamtenga kuja anatsata zoyamwitsa, awete Yakobo, anthu ake, ndi Israele, cholandira chake. Potero anawaweta monga mwa mtima wake wangwiro; nawatsogolera ndi luso la manja ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:12

Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho chilamulo ndi aneneri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:15

Ndipo Iye anati kwa iwo, Yang'anirani, mudzisungire kupewa msiriro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 107:41

Koma aika waumphawi pamsanje posazunzika, nampatsa mabanja ngati gulu la nkhosa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:5

Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 4:24

Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 58:6

Kodi kumeneku si kusala kudya kumene ndinakusankha: kumasula nsinga za zoipa, ndi kumasula zomanga goli, ndi kuleka otsenderezedwa amuke mfulu, ndi kuti muthyole magoli onse?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 31:20

Pobisalira pamaso panu mudzawabisa kwa chiwembu cha munthu, mudzawabisa iwo mumsasa kuti muwalanditse pa kutetana kwa malilime.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 23:1-3

Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa. Andigonetsa kubusa lamsipu, anditsogolera kumadzi odikha. Atsitsimutsa moyo wanga; anditsogolera m'mabande a chilungamo, chifukwa cha dzina lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 5:10

Wokonda siliva sadzakhuta siliva; ngakhale wokonda chuma sadzakhuta phindu; ichinso ndi chabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 4:7

Pakuti akusiyanitsa iwe ndani? Ndipo uli nacho chiyani chosati wachilandira? Koma ngati wachilandira udzitamanda bwanji, monga ngati sunachilandira?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:9

Koma tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 69:29

Koma ine ndine wozunzika ndi womva zowawa; chipulumutso chanu, Mulungu, chindikweze pamsanje.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 30:9

ndingakhute ndi kukukanani, ndi kuti, Yehova ndani? Kapena ndingasauke ndi kuba, ndi kutchula dzina la Mulungu wanga pachabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:35

pakuti ndinali ndi njala, ndipo munandipatsa Ine kudya; ndinali ndi ludzu, ndipo munandimwetsa Ine; ndinali mlendo, ndipo munachereza Ine;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 2:1

Abale anga, pakuti muli nacho chikhulupiriro cha Ambuye wathu Yesu Khristu, Ambuye wa ulemerero, musakhale okondera ndi kusamala maonekedwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 35:10

Mafupa anga onse adzanena, Yehova, afanana ndi Inu ndani, wakulanditsa wozunzika kwa iye amene amposa mphamvu, ndi wozunzika ndi waumphawi kwa iye amfunkhira?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 109:31

Popeza adzaima pa dzanja lamanja la waumphawi, kumpulumutsa kwa iwo akuweruza koipa moyo wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 112:9

Anagawagawa, anapatsa aumphawi; chilungamo chake chikhalitsa kosatha; nyanga yake idzakwezeka ndi ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:2

Chuma cha uchimo sichithangata; koma chilungamo chipulumutsa kuimfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 149:4

Popeza Yehova akondwera nao anthu ake; adzakometsa ofatsa ndi chipulumutso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 113:7

Amene autsa wosauka kumchotsa kufumbi, nakweza waumphawi kumchotsa kudzala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 3:14

Ndipo asilikali omwe anamfunsa iye, nati, Nanga ife tizichita chiyani? Ndipo iye anati kwa iwo, Musaopse, musanamize munthu aliyense; khalani okhuta ndi kulipira kwanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 41:17

Wosauka ndi wosowa afuna madzi, ndipo palibe, ndi lilime lao lilephera, chifukwa cha ludzu; Ine Yehova ndidzawayankha, Ine Mulungu wa Israele sindidzawasiya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 41:30

ndipo pambuyo pao zidzauka zaka zisanu ndi ziwiri za njala; ndipo anthu adzaiwala zochuluka zonsezo m'dziko la Ejipito; ndipo njala idzapululutsa dziko;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:21

Pakuti wakumwaimwa ndi wosusukayo adzasauka; ndipo kusinza kudzaveka munthu nsanza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 22:24

Pakuti sanapeputsa ndipo sananyansidwe ndi zunzo la wozunzika; ndipo sanambisire nkhope yake; koma pomfuulira Iye, anamva.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:18

Pakuti ndiyesa kuti masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzaonetsedwa kwa ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 109:16-17

Chifukwa kuti sanakumbukire kuchita chifundo, koma analondola wozunzika ndi waumphawi, ndi wosweka mtima, kuti awaphe. Inde, anakonda kutemberera, ndipo kudamdzera mwini; sanakondwere nako kudalitsa, ndipo kudamkhalira kutali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 58:10

ndipo ngati upereka kwa wanjala chimene moyo wako umakhumba, ndi kukhutitsa moyo wovutidwa, pomwepo kuunika kwako kudzauka mumdima, ndipo usiku wako udzanga usana;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:22

Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:3

Yehova samvetsa njala moyo wa wolungama; koma amainga chifuniro cha wochimwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 20:35

M'zinthu zonse ndinakupatsani chitsanzo, chakuti pogwiritsa ntchito, kotero muyenera kuthandiza ofooka ndi kukumbuka mau a Ambuye Yesu, kuti anati yekha, Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:19-21

Musadzikundikire nokha chuma pa dziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba: Chifukwa chake pamene paliponse upatsa mphatso zachifundo, usamaomba lipenga patsogolo pako, monga amachita onyenga m'masunagoge, ndi m'makwalala, kotero kuti atamandidwe ndi anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao. koma mudzikundikire nokha chuma m'Mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziononga, ndipo mbala siziboola ndi kuba; pakuti kumene kuli chuma chako, komwe udzakhala mtima wakonso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:10

Ndipo Mulungu wa chisomo chonse, amene adakuitanani kulowa ulemerero wake wosatha mwa Khristu, mutamva zowawa kanthawi, adzafikitsa inu opanda chilema mwini wake, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:24

Alipo wogawira, nangolemerabe; aliponso womana chomwe ayenera kupatsa nangosauka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 62:10

Musakhulupirire kusautsa, ndipo musatama chifwamba; chikachuluka chuma musakhazikepo mitima yanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:23

M'kulima kwa osauka muli zakudya zambiri; koma zinazo zimaonongeka posowa chiweruzo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 21:3-4

Ndipo Iye anati, Zoonadi ndinena kwa inu, wamasiye uyu waumphawi anaikamo koposa onse; pamene iphukira, muipenya nimuzindikira pa nokha kuti dzinja lili pafupi pomwepo. Inde chotero inunso, pakuona zinthu izi zilikuchitika, zindikirani kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi. Indetu ndinena ndinu, Mbadwo uno sudzapitirira, kufikira zonse zitachitika. Kumwamba ndi dziko lapansi zidzapita; koma mau anga sadzapita. Koma mudziyang'anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha; pakuti lidzatero ndi kufikira anthu onse akukhala pankhope pa dziko lonse lapansi. Koma inu dikirani nyengo zonse, ndi kupemphera, kuti mukalimbike kupulumuka zonse zimene zidzachitika, ndi kuimirira pamaso pa Mwana wa Munthu. Ndipo usana uliwonse Iye analikuphunzitsa m'Kachisi; ndi usiku uliwonse anatuluka, nagona pa phiri lotchedwa la Azitona. Ndipo anthu onse analawira mamawa kudza kwa Iye ku Kachisi kudzamvera Iye. pakuti onse amenewa anaika mwa unyinji wao pa zoperekazo; koma iye mwa kusowa kwake anaikamo za moyo wake, zonse anali nazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 135:6

Chilichonse chimkonda Yehova achichita, kumwamba ndi pa dziko lapansi, m'nyanja ndi mozama monse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:14

Mfumu yolamulira osauka mwantheradi, mpando wake udzakhazikika kufikira nthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 116:6

Yehova asunga opusa; ndidafooka ine, koma anandipulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:17-18

Koma iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, naona mbale wake ali wosowa ndi kutsekereza chifundo chake pommana iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji? Tiana, tisakonde ndi mau, kapena ndi lilime, komatu ndi kuchita ndi m'choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:45

Ndipo zimene anali nazo, ndi chuma chao, anazigulitsa, nazigawira kwa onse, monga momwe yense anasowera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:30

Koma ngati Mulungu aveka chotero udzu wa kuthengo, ukhala lero, ndi mawa uponyedwa pamoto, nanga si inu kopambana ndithu, inu akukhulupirira pang'ono?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 146:5-7

Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti amthandize, chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake. Amene analenga zakumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zili m'mwemo. Ndiye wakusunga choonadi kosatha, ndiye wakuchitira chiweruzo osautsika; ndiye wakupatsa anjala chakudya; Yehova amasula akaidi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:16

Zochepa zake za wolungama zikoma koposa kuchuluka kwao kwa oipa ambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:39

koma ndinena kwa inu, Musakanize munthu woipa; koma amene adzakupanda iwe pa tsaya lako lamanja, umtembenuzire linanso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:6

Waumphawi woyenda mwangwiro apambana ndi yemwe akhotetsa njira zake, angakhale alemera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 3:28

Muno mulibe Myuda, kapena Mgriki, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; pakuti muli nonse mmodzi mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 20:26-28

Sikudzakhala chomwecho kwa inu ai; koma amene aliyense akafuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu; ndipo amene aliyense akafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala kapolo wanu: monga Mwana wa Munthu sanadze kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Atate wanga wakumwamba, moyo wanga wonse ukukulemekezani ndi kukweza ukulu wanu, ndikutamanda dzina lanu ndi kukongola kwa chiyero chanu. Ndaona kuti ndinu wabwino ndipo mukundiyitana kuti ndionetse chikondi chanu padziko lapansi. Chifukwa cha ichi, panopa ndikukweza manja anga kumwamba, kukupemphani chifukwa cha osauka a dziko lino. Ambuye, onani kusowa kwakukulu m'miyoyo yawo. Ndikukupemphani kuti chifundo chanu ndi chikondi chanu ziwafikire, kuti chisomo chanu ndi chiyanjo chanu zikhale pa iwo, kuwapatsa mphamvu zomwe akufunikira kuti apitirize. Awamasulireni ku zoyipa za iwo amene akukonzekera kuwachitira zoipa, awatetezeni ku ozunza ndi ochita nkhanza. Apatseni chisomo chanu Mulungu wokondedwa, kuti akondwere ndi ubwino wanu ndipo maso awo adzazidwe ndi chiyembekezo cha tsogolo labwino mwa inu. Awonetseni chikondi chanu ndipo mutithandize ife kukhala njira yodalitsira iwo. Chitsani kusayanjanitsidwa kulikonse kwa anthu anu ndipo nthawi zonse tikhale okonzeka kupereka chakudya chathu kwa anjala ndi madzi kwa aumira. M'dzina la Yesu, tikukupemphani kuti muwateteze, muwapatse zonse zomwe akufunikira ndipo mudalitse miyoyo yawo. M'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa