Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa

Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano


Masalimo 48 - Buku Lopatulika Buku Lopatulika
Masalimo 48

Ukoma ndi ulemerero wa Ziyoni
Nyimbo. Salimo la ana a Kora.

1 Yehova ndiye wamkulu, ayenera kulemekezekadi, m'mzinda wa Mulungu wathu, m'phiri lake loyera.

2 Phiri la Ziyoni, chikhalidwe chake nchokoma kumbali zake za kumpoto, ndilo chimwemwe cha dziko lonse lapansi, mzinda wa mfumu yaikulu.

3 Mulungu adziwika m'zinyumba zake ngati msanje.

4 Pakuti, taonani, mafumuwo anasonkhana, anapitira pamodzi.

5 Anapenya mudziwo, ndipo pamenepo anadabwa; anaopsedwa, nathawako.

6 Pomwepo anagwidwa nako kunthunthumira; anamva chowawa, ngati wam'chikuta.

7 Muswa zombo za ku Tarisisi ndi mphepo ya kum'mawa.

8 Monga tidamva, momwemo tidapenya m'mzinda wa Yehova wa makamu, m'mzinda wa Mulungu wathu, Mulungu adzaukhazikitsa kunthawi yamuyaya.

9 Tidalingalira zachifundo chanu, Mulungu, m'kati mwa Kachisi wanu.

10 Monga dzina lanu, Mulungu, momwemo lemekezo lanu ku malekezero a dziko lapansi; m'dzanja lamanja lanu mudzala chilungamo.

11 Likondwere phiri la Ziyoni, asekere ana aakazi a Yuda, chifukwa cha maweruzo anu.

12 Zungulirani Ziyoni, ndipo muuzinge, werengani nsanja zake.

13 Penyetsetsani malinga ake, yesetsani zinyumba zake; kuti mukaziwerengere mibadwo ikudza m'mbuyo.

14 Pakuti Mulungu ameneyo ndiye Mulungu wathu kunthawi za nthawi, adzatitsogolera kufikira imfa.

Bible Society of Malawi

Bible Society of Malawi