Ndipo mkazi anati kwa Eliya, Ndizindikira tsopano kuti ndinu munthu wa Mulungu, ndi kuti mau a Yehova ali m'kamwa mwanuwo ngoona.
Yohane 3:2 - Buku Lopatulika Iyeyu anadza kwa Yesu usiku, nati kwa Iye, Rabi, tidziwa kuti Inu ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kuchita zizindikiro zimene Inu muchita, ngati Mulungu sakhala naye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Iyeyu anadza kwa Yesu usiku, nati kwa Iye, Rabi, tidziwa kuti Inu ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kuchita zizindikiro zimene Inu muchita, ngati Mulungu sakhala naye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa adadza kwa Yesu usiku. Adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, tikudziŵa kuti ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu, pakuti palibe munthu wotha kuchita zizindikiro zozizwitsa zimene Inu mukuzichita, ngati Mulungu sali naye.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anabwera kwa Yesu usiku ndipo anati, “Rabi, ife tikudziwa kuti ndinu aphunzitsi wochokera kwa Mulungu, pakuti palibe amene angachite zizindikiro zodabwitsa zimene Inu mukuchita ngati Mulungu sali naye.” |
Ndipo mkazi anati kwa Eliya, Ndizindikira tsopano kuti ndinu munthu wa Mulungu, ndi kuti mau a Yehova ali m'kamwa mwanuwo ngoona.
Mverani Ine, inu amene mudziwa chilungamo, anthu amene mumtima mwao muli lamulo langa; musaope chitonzo cha anthu, ngakhale kuopsedwa ndi kutukwana kwao.
Ndipo mfumu Zedekiya analumbira m'tseri kwa Yeremiya, kuti, Pali Yehova, amene anatilengera ife moyo uno, sindidzakupha iwe sindidzakupereka iwe m'manja mwa anthu awa amene afuna moyo wako.
Ndipo anatumiza kwa Iye ophunzira ao, pamodzi ndi Aherode, amene ananena, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli woona, ndipo muphunzitsa njira ya Mulungu moona ndithu, ndipo simusamala munthu aliyense; pakuti simuyang'anira pa nkhope ya anthu.
Koma inu musatchedwa Rabi; pakuti Mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale.
Ndipo pamene anafika, ananena naye, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli woona, ndipo simusamala munthu; pakuti simuyang'ana nkhope ya anthu, koma muphunzitsa njira ya Mulungu moona: Nkuloleka kodi kupereka msonkho kwa Kaisara, kapena iai?
Koma Yesu anacheuka, napenya iwo alikumtsata, nanena nao, Mufuna chiyani? Ndipo anati kwa Iye, Rabi (ndiko kunena posandulika, Mphunzitsi), mukhala kuti?
Koma ngati ndichita, mungakhale simukhulupirira Ine, khulupirirani ntchitozo; kuti mukadziwe ndi kuzindikira kuti Atate ali mwa Ine, ndi Ine mwa Atate.
Sukhulupirira kodi kuti ndili Ine mwa Atate, ndi Atate ali mwa Ine? Mau amene ndinena Ine kwa inu sindilankhula kwa Ine ndekha; koma Atate wokhala mwa Ine achita ntchito zake.
Sindikadachita mwa iwo ntchito zosachita wina, sakadakhala nalo tchimo; koma tsopano anaona, nada Ine ndi Atate wanganso.
Chiyambi ichi cha zizindikiro zake Yesu anachita mu Kana wa mu Galileya naonetsera ulemerero wake; ndipo ophunzira ake anakhulupirira Iye.
Yesu ananena naye, Maria. Iyeyu m'mene anacheuka, ananena ndi Iye mu Chihebri, Raboni; chimene chinenedwa, Mphunzitsi.
Ndipo anadza kwa Yohane, nati kwa iye, Rabi, Iye amene anali ndi inu tsidya lija la Yordani, amene munamchitira umboni, taonani yemweyu abatiza, ndipo anthu onse alinkudza kwa Iye.
Koma Ine ndili nao umboni woposa wa Yohane; pakuti ntchito zimene Atate anandipatsa ndizitsirize, ntchito zomwezo ndizichita zindichitira umboni, kuti Atate anandituma Ine.
Ndipo khamu lalikulu la anthu linamtsata Iye, chifukwa anaona zizindikiro zimene anachita pa odwala.
Koma ambiri a m'khamu la anthu anakhulupirira Iye; ndipo ananena, Pamene Khristu akadza kodi adzachita zizindikiro zambiri zoposa zimene adazichita ameneyo?
Ena pamenepo mwa Afarisi ananena, Munthu uyu sachokera kwa Mulungu, chifukwa sasunga Sabata. Koma ena ananena, Munthu ali wochimwa akhoza bwanji kuchita zizindikiro zotere? Ndipo panali kutsutsana mwa iwo.
za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye.
Amuna inu Aisraele, mverani mau awa: Yesu Mnazarayo, mwamuna wochokera kwa Mulungu, wosonyezedwa kwa inu ndi zimphamvu, ndi zozizwa, ndi zizindikiro, zimene Mulungu anazichita mwa Iye pakati pa inu monga mudziwa nokha;
ndi kuti unyinji wa abale mwa Ambuye, pokhulupirira m'zomangira zanga, alimbika mtima koposa kulankhula mau a Mulungu opanda mantha.
Pamenepo Gideoni anatenga amuna khumi mwa anyamata ake, nachita monga Yehova adanena naye; ndipo kunali, popeza anaopa akunyumba ya atate wake, ndi amuna akumudziwo, sanachichite msana, koma usiku.