Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 3:26 - Buku Lopatulika

26 Ndipo anadza kwa Yohane, nati kwa iye, Rabi, Iye amene anali ndi inu tsidya lija la Yordani, amene munamchitira umboni, taonani yemweyu abatiza, ndipo anthu onse alinkudza kwa Iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Ndipo anadza kwa Yohane, nati kwa iye, Rabi, Iye amene anali ndi inu tsidya lija la Yordani, amene munamchitira umboni, taonani yemweyu abatiza, ndipo anthu onse alinkudza kwa Iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Choncho ophunzirawo adadza kwa Yohane namuuza kuti, “Aphunzitsi onanitu, munthu uja amene anali ndi inu patsidya pa Yordani, yemwe uja munkamuchitira umboniyu, nayenso akubatiza, ndipo anthu onse akuthamangira kwa Iye.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Iwo anabwera kwa Yohane anati, “Rabi, munthu uja munali naye mbali inayo ya mu mtsinje wa Yorodani, amene munamuchitira umboni, taonani naye akubatizanso, ndipo aliyense akupita kwa Iye.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 3:26
23 Mawu Ofanana  

Wakumva pemphero Inu, zamoyo zonse zidzadza kwa Inu.


Ndiponso ndinapenyera mavuto onse ndi ntchito zonse zompindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ake achitira munthu nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Ndadzilumbira ndekha, mau achokera m'kamwa mwanga m'chilungamo, ndipo sadzabwerera, kuti mabondo onse adzandigwadira Ine, malilime onse nadzalumbira Ine.


ndi kulonjeredwa m'misika, ndi kutchedwa ndi anthu, Rabi.


Koma inu musatchedwa Rabi; pakuti Mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale.


Yohane achita umboni za Iye, nafuula nati, Uyu ndiye amene ndinanena za Iye, Wakudzayo pambuyo panga analipo ndisanabadwe ine; chifukwa anakhala woyamba wa ine.


Iyeyu anadza mwa umboni kudzachita umboni za kuunikaku, kuti onse akakhulupirire mwa iye.


Uku ndiko kuunika kwenikweni, kumene kuunikira anthu onse akulowa m'dziko lapansi.


Ngati timleka Iye kotero, onse adzakhulupirira Iye; ndipo adzadza Aroma nadzachotsa malo athu ndi mtundu wathu.


Chifukwa chake Afarisi ananena wina ndi mnzake, Muona kuti simupindula kanthu konse; onani dziko litsata pambuyo pake pa Iye.


Iyeyu anadza kwa Yesu usiku, nati kwa Iye, Rabi, tidziwa kuti Inu ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kuchita zizindikiro zimene Inu muchita, ngati Mulungu sakhala naye.


Chifukwa chake pamene Ambuye anadziwa kuti Afarisi adamva kuti Yesu anayesa anthu ophunzira, nawabatiza koposa Yohane


(angakhale Yesu sanabatize yekha koma ophunzira ake),


Pa mphindikati iyi ophunzira ake anampempha Iye, ndi kunena, Rabi, idyani.


Inu munatuma kwa Yohane, ndipo iye anachitira umboni choonadi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa