Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 6:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo khamu lalikulu la anthu linamtsata Iye, chifukwa anaona zizindikiro zimene anachita pa odwala.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo khamu lalikulu la anthu linamtsata Iye, chifukwa anaona zizindikiro zimene anachita pa odwala.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Khamu lalikulu la anthu lidamtsatira, chifukwa lidaaona zizindikiro zozizwitsa zimene adaachita pakuchiritsa anthu odwala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 ndipo gulu lalikulu la anthu linamutsata Iye chifukwa linaona zizindikiro zodabwitsa zimene anazichita pa odwala.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 6:2
19 Mawu Ofanana  

Koma Yesu m'mene anadziwa, anachokera kumeneko: ndipo anamtsata Iye anthu ambiri; ndipo Iye anawachiritsa iwo onse,


Ndipo makamu ambiri a anthu anasonkhanira kwa Iye, kotero kuti Iye analowa m'ngalawa, nakhala pansi, ndipo khamu lonse linaima pamtunda.


Ndipo Iye anatuluka, naona khamu lalikulu la anthu, nachitira iwo chifundo, nachiritsa akudwala ao.


Ndipo pakutsika pake paphiripo, inamtsata mipingo yambiri ya anthu.


Koma iye anatuluka nayamba kulalikira ndithu, ndi kubukitsa mauwo, kotero kuti Yesu sanathe kulowanso poyera m'mudzi, koma anakhala padera m'mapululu; ndipo anadza kwa Iye anthu a kumalo onse.


Ndipo anthu anawaona alikumuka, ndipo ambiri anawazindikira, nathamangira limodzi kumeneko pamtunda, ochokera m'midzi monse, nawapitirira.


Pamenepo ansembe aakulu ndi Afarisi anasonkhanitsa akulu, nanena, Titani ife? Chifukwa munthu uyu achita zizindikiro zambiri.


Chifukwa cha ichinso khamulo linadza kudzakomana ndi Iye, chifukwa anamva kuti Iye adachita chizindikiro ichi.


Koma angakhale adachita zizindikiro zambiri zotere pamaso pao iwo sanakhulupirire Iye;


Chiyambi ichi cha zizindikiro zake Yesu anachita mu Kana wa mu Galileya naonetsera ulemerero wake; ndipo ophunzira ake anakhulupirira Iye.


Koma pamene anali mu Yerusalemu pa Paska pachikondwerero, ambiri anakhulupirira dzina lake, pakuona zizindikiro zake zimene anachitazi.


Ndipo zizindikiro zina zambiri Yesu anazichita pamaso pa ophunzira ake, zimene sizinalembedwe m'buku ili;


Iyeyu anadza kwa Yesu usiku, nati kwa Iye, Rabi, tidziwa kuti Inu ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kuchita zizindikiro zimene Inu muchita, ngati Mulungu sakhala naye.


Chifukwa chake, anthu, poona chizindikiro chimene anachita, ananena, kuti, Ameneyo ndiye mneneri ndithu wakudzayo m'dziko lapansi.


M'mawa mwake khamu la anthu limene linaima tsidya lija la nyanja linaona kuti palibe ngalawa ina koma imodzi, ndi kuti Yesu sanalowe pamodzi ndi ophunzira ake m'ngalawamo, koma ophunzira ake adachoka pa okha;


Yesu anayankha iwo nati, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Mundifuna Ine, si chifukwa munaona zizindikiro, koma chifukwa munadya mkate, nimunakhuta.


Chifukwa chake anati kwa Iye, Ndipo muchita chizindikiro chanji, kuti tione ndi kukhulupirira Inu? Muchita chiyani?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa