Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 14:10 - Buku Lopatulika

10 Sukhulupirira kodi kuti ndili Ine mwa Atate, ndi Atate ali mwa Ine? Mau amene ndinena Ine kwa inu sindilankhula kwa Ine ndekha; koma Atate wokhala mwa Ine achita ntchito zake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Sukhulupirira kodi kuti ndili Ine mwa Atate, ndi Atate ali mwa Ine? Mau amene ndinena Ine kwa inu sindilankhula kwa Ine ndekha; koma Atate wokhala mwa Ine achita ntchito zake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Kodi sukukhulupirira kuti Ine ndimakhala mwa Atate, ndipo Atate amakhala mwa Ine? Mau amene ndimakuuzani sachokera kwa Ine ndekha ai, koma Atate amene amakhala mwa Ine, ndiwo amagwira ntchito yao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Kodi sukukhulupirira kuti Ine ndili mwa Atate, ndipo Atate ali mwa Ine? Mawu amene Ine ndiyankhula kwa inu si mawu anga okha koma ndi mawu Atate wokhala mwa Ine, amene akugwira ntchito yake.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 14:10
26 Mawu Ofanana  

Ine ndi Atate ndife amodzi.


Koma ngati ndichita, mungakhale simukhulupirira Ine, khulupirirani ntchitozo; kuti mukadziwe ndi kuzindikira kuti Atate ali mwa Ine, ndi Ine mwa Atate.


ndipo yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthawi yonse. Kodi ukhulupirira ichi?


Pakuti sindinalankhule mwa Ine ndekha; koma Atate wondituma Ine, yemweyu anandipatsa Ine lamulo, limene ndikanene, ndi limene ndikalankhule.


Khulupirirani Ine, kuti Ine ndili mwa Atate ndi Atate ali mwa Ine; koma ngati si chomwecho, khulupirirani Ine chifukwa cha ntchito zomwe.


Tsiku lomwelo mudzazindikira kuti ndili Ine mwa Atate wanga, ndi inu mwa Ine, ndi Ine mwa inu.


Wosandikonda Ine sasunga mau anga; ndipo mau amene mumva sali mau anga, koma a Atate wondituma Ine.


chifukwa mau amene munandipatsa Ine ndinapatsa iwo; ndipo analandira, nazindikira koona kuti ndinatuluka kwa Inu, ndipo anakhulupirira kuti Inu munandituma Ine.


Iyeyu anadza kwa Yesu usiku, nati kwa Iye, Rabi, tidziwa kuti Inu ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kuchita zizindikiro zimene Inu muchita, ngati Mulungu sakhala naye.


Koma Yesu anayankha iwo, Atate wanga amagwira ntchito kufikira tsopano, Inenso ndigwira ntchito.


Pamenepo Yesu anayankha nati kwa iwo, Indetu, indetu ndinena kwa inu, sangathe Mwana kuchita kanthu pa yekha, koma chimene aona Atate achichita, ndicho. Pakuti zimene Iye azichita, zomwezo Mwananso azichita momwemo.


Pamenepo Yesu anayankha iwo, nati, Chiphunzitso changa sichili changa, koma cha Iye amene anandituma Ine.


Chifukwa chake Yesu anati, Pamene mutadzamkweza Mwana wa Munthu, pomwepo mudzazindikira kuti Ine ndine, ndipo sindichita kanthu kwa Ine ndekha, koma monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi.


Zimene ndinaona Ine kwa Atate, ndilankhula; ndipo inunso muchita chimene mudamva kwa atate wanu.


Koma tsopano mufuna kundipha Ine, ndine munthu amene ndinalankhula ndi inu choonadi, chimene ndinamva kwa Mulungu; ichi Abrahamu sanachite.


za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye.


ndiko kunena kuti Mulungu anali mwa Khristu, alinkuyanjanitsa dziko lapansi kwa Iye yekha, osawawerengera zolakwa zao; ndipo anaikiza kwa ife mau a chiyanjanitso.


Pakuti kunamkomera Atate kuti mwa Iye chidzalo chonse chikhalire,


pakuti mwa Iye chikhalira chidzalo cha Umulungu m'thupi,


Pakuti pali atatu akuchita umboni,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa