Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 22:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo anatumiza kwa Iye ophunzira ao, pamodzi ndi Aherode, amene ananena, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli woona, ndipo muphunzitsa njira ya Mulungu moona ndithu, ndipo simusamala munthu aliyense; pakuti simuyang'anira pa nkhope ya anthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo anatumiza kwa Iye ophunzira ao, pamodzi ndi Aherode, amene ananena, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli woona, ndipo muphunzitsa njira ya Mulungu moona ndithu, ndipo simusamala munthu aliyense; pakuti simuyang'anira pa nkhope ya anthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Adatuma ophunzira ao ena pamodzi ndi ena a m'chipani cha Herode kwa Yesu. Iwoŵa adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, tikudziŵa kuti Inu mumanena zoona, mumaphunzitsa malamulo a Mulungu moona, ndipo simuwopa munthu aliyense. Paja Inu simuyang'anira kuti uyu ndani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Anatumiza ophunzira awo kwa Iye pamodzi ndi Aherodia. Anati, “Aphunzitsi, tidziwa kuti ndinu wangwiro ndi kuti mumaphunzitsa mawu a Mulungu monga mwa choonadi. Simutekeseka ndi anthu, popeza simusamala kuti kodi ndi ndani?

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 22:16
36 Mawu Ofanana  

Koma Mikaya anati, Pali Yehova, zimene Yehova adzanena nane ndidzanena ine.


Amanena za bodza munthu yense ndi mnansi wake, amanena ndi mlomo wothyasika, ndi mitima iwiri.


Pakuti m'kamwa mwao mulibe mau okhazikika; m'kati mwao m'mosakaza; m'mero mwao ndi manda apululu; lilime lao asyasyalika nalo.


Pakamwa pake mposalala ngati mafuta amkaka, koma mumtima mwake munali nkhondo, mau ake ngofewa ngati mafuta oyenga, koma anali malupanga osololasolola.


Wosyasyalika mnzake atcherera mapazi ake ukonde.


Chilamulo cha zoona chinali m'kamwa mwake, ndi chosalungama sichinapezeke m'milomo mwake; anayenda nane mumtendere ndi moongoka, nabweza ambiri aleke mphulupulu.


Chifukwa chake Inenso ndakuikani onyozeka ndi ochepseka kwa anthu onse, popeza simunasunge njira zanga, koma munaweruza mwankhope pochita chilamulo.


nanena, Mphunzitsi, Mose anati, Ngati munthu akafa wopanda mwana, mphwake adzakwatira mkazi wake, nadzamuukitsira mbale wake mbeu.


chimodzimodzi wachiwiri, ndi wachitatu, kufikira wachisanu ndi chiwiri.


Nati Iye, Mukani kumzinda kwa munthu wina wake, mukati kwa Iye, Mphunzitsi anena, Nthawi yanga yayandikira; ndidzadya Paska kwanu pamodzi ndi ophunzira anga.


Ndipo pomwepo anadza kwa Yesu, nati, Tikuoneni, Rabi; nampsompsonetsa.


Ndipo pamene Iye anatuluka kutsata njira, anamthamangira munthu, namgwadira Iye, namfunsa, Mphunzitsi wabwino, ndidzachita chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?


Ndipo anatuma kwa Iye ena a Afarisi ndi a Aherode, kuti akamkole Iye m'kulankhula kwake.


Ndipo pamene anafika, ananena naye, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli woona, ndipo simusamala munthu; pakuti simuyang'ana nkhope ya anthu, koma muphunzitsa njira ya Mulungu moona: Nkuloleka kodi kupereka msonkho kwa Kaisara, kapena iai?


Ndipo Afarisi anatuluka, ndipo pomwepo anamkhalira upo ndi Aherode, wakumuononga Iye.


Ndipo Iye anawalamula, nanena, Yang'anirani, penyani kuti mupewe chotupitsa mkate cha Afarisi, ndi chotupitsa mkate cha Herode.


Ndipo anamfunsa Iye, nanena, Mphunzitsi, ife tidziwa kuti munena ndi kuphunzitsa kolunjika, ndi kusasamalira nkhope ya munthu, koma muphunzitsa njira ya Mulungu koonadi;


Ndipo Yesu anayankha nati kwa iye, Simoni, ndili ndi kanthu kakunena kwa iwe. Ndipo iye anavomera, Mphunzitsi, nenani.


Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.


Pamenepo Pilato anati kwa Iye, Nanga kodi ndiwe Mfumu? Yesu anayankha, Munena kuti ndine Mfumu. Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza kudziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi. Yense wakukhala mwa choonadi amva mau anga.


Iye wolankhula zochokera kwa iye yekha afuna ulemu wa mwini yekha. Iye wakufuna ulemu wa Iye amene anamtuma, yemweyu ali woona, ndipo mwa Iye mulibe chosalungama.


Pakuti sitikhala monga ambiriwo, akuchita malonda nao mau a Mulungu; koma monga mwa choona mtima, koma monga mwa Mulungu pamaso pa Mulungu, tilankhula mwa Khristu.


koma takaniza zobisika za manyazi, osayendayenda mochenjerera, kapena kuchita nao mau a Mulungu konyenga; koma ndi maonekedwe a choonadi; tidzivomeretsa tokha ku chikumbumtima cha anthu onse pamaso pa Mulungu.


Kotero kuti ife sitidziwanso munthu tsopano monga mwa thupi; ndipo ngati tazindikira Khristu monga mwa thupi, koma tsopano sitimzindikiranso motero.


Pakuti kodi ndikopa anthu tsopano, kapena Mulungu? Kapena kodi ndifuna kukondweretsa anthu? Ndikadakhala wokondweretsabe anthu, sindikadakhala kapolo wa Khristu.


Koma iwo akuyesedwa ali kanthu (ngati anali otani kale, kulibe kanthu kwa ine; Mulungu salandira nkhope ya munthu) iwo omvekawo sanandionjezere ine kanthu;


amene anati za atate wake ndi amai wake, sindinamuone; Sanazindikire abale ake, sanadziwe ana ake omwe; popeza anasamalira mau anu, nasunga chipangano chanu.


komatu monga Mulungu anativomereza kutiikiza Uthenga Wabwino, kotero tilankhula; osati monga okondweretsa anthu, koma Mulungu; amene ayesa mitima yathu.


Koma nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, yosadzikometsera pamaso.


Ndipo tidziwa kuti Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife chidziwitso, kuti tizindikire Woonayo, ndipo tili mwa Woonayo, mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iye ndiye Mulungu woona ndi moyo wosatha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa